Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Maukwati a Amuna Okhaokha Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Mulungu Amavomereza Maukwati a Amuna Okhaokha Kapena Akazi Okhaokha?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amavomereza Maukwati a Amuna Okhaokha Kapena Akazi Okhaokha?

PA MWAMBO winawake m’tchalitchi, amuna awiri aimirira atagwirana manja pamaso pa bishopu wotchuka wa mpingo wa Episkopi. Iwo akupanga “pangano . . . pamaso pa Mulungu ndi tchalitchi.” Bishopuyo atavala mkanjo wokongola wagolide ndiponso woyera, akudalitsa ukwati wa amuna awiriwo pamaso pa anthu oonerera. Kenaka amuna awiriwo akukupatirana ndi kupsompsonana ndipo anthu akuimirira n’kuwaombera m’manja. Malinga ndi bishopu ameneyu, maukwati a amuna okhaokha kapena akazi okhaokha oterewa “ndi opatulika ndipo afunika kudalitsidwa, . . . ndiponso afunika kuonedwa kuti ndi oyera chifukwa ndi oterodi.”

Komabe, atsogoleri ena achipembedzo anena poyera kuti amadana kwambiri ndi maukwati a amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Cynthia Brust, mneneri wa bungwe loimira mabishopu a mpingo wa Episkopi osagwirizana ndi kusintha kwa zinthu lotchedwa American Anglican Council anati: “Takhumudwa kwambiri ndi zomwe wachita [bishopu] ameneyu. Kudalitsa maukwati a amuna okhaokha kapena akazi okhaokha n’kosemphaniranatu ndi chiphunzitso chomveka bwino cha m’Baibulo pa nkhani ya ukwati ndi kugonana.” Iye anawonjezera kuti “kugonana kuyenera kuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi omwe achita ukwati woyera.”

Kusiyana maganizo kwakukulu komwe kulipo pa nkhani imeneyi sikuti kukungokhudza chipembedzo chokha. Padziko lonse lapansi, anthu andale akukangana, poganizira zomwe zimenezi zingatanthauze pa nkhani ya chikhalidwe, ndale, ndi zachuma. Zili choncho chifukwa zingasokoneze kwambiri nkhani ya mapenshoni, kulandira chithandizo cha mankhwala pogwiritsa ntchito inshuwalansi imodzi monga anthu okwatirana, komanso misonkho.

Nkhani zokhudza ufulu wa anthu ndiponso kufunika koti zinthu zinazake zivomerezedwe mwalamulo nthawi zambiri zimakhala zovuta, ndipo anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani zoterozo. Akristu oona amasamala kuti asatenge nawo mbali iliyonse, ndipo amatero popewa kunenapo zilizonse pankhani za ndale. (Yohane 17:16) * Komabe, anthu ena amene amakhulupirira Baibulo amaona kuti akusokonezeka maganizo pankhani ya maukwati a amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, ndiponso kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Kodi maukwati a amuna okhaokha kapena akazi okhaokha mumawaona bwanji? Kodi lamulo la Mulungu pa nkhani ya ukwati n’lotani? Kodi mmene mumaonera nkhani imeneyi zimakhudza bwanji ubwenzi wanu ndi Mulungu?

Mlengi Wathu Ndi Amene Amakhazikitsa Malamulo Oti Tiziyendera

Maboma asanayambe n’komwe kukhala ndi malamulo oyendetsera ukwati, Mlengi wathu anakhazikitsa kalekale malamulo okhudza ukwati. Buku loyambirira la m’Baibulo limatiuza kuti: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo lotchedwa Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words, mawu achihebri akuti “mkazi,” amatanthauza “munthu wamkazi.” Yesu nayenso anasonyeza kuti anthu okwatirana ayenera kukhala “mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4.

Choncho Mulungu anafuna kuti ukwati ukhale mgwirizano wosatherapo ndiponso wachikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi. Amuna ndi akazi analengedwa kuti azitha kuthandizana, choncho akhoza kupatsana zosowa zawo zokhudza maganizo awo, moyo wawo wauzimu, ndi chilakolako chawo chogonana.

Nkhani yodziwika bwino ya m’Baibulo yokhudza Sodomu ndi Gomora imasonyeza momwe Mulungu amaonera kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Mulungu anati: “Kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo . . . kuchimwa kwawo kuli kulemera ndithu.” (Genesis 18:20) Kunyansa kwa khalidwe la anthu panthawi imeneyo kunaonekera pamene alendo awiri aamuna anapita kunyumba kwa munthu wolungama Loti kukacheza. “Anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m’mbali zonse; ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe [“tigonane nawo,” NW].” (Genesis 19:4, 5) Baibulo limati: “Anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.”—Genesis 13:13.

Amunawo ‘anatenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha.’ (Aroma 1:27) Iwo ‘anatsata zilakolako zachilendo.’ (Yuda 7) M’mayiko amene anthu amachita makampeni olimbikitsa ufulu wa anthu ogonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, ena anganene kuti si bwino kugwiritsa ntchito mawu akuti “zachilendo” pofotokoza zinthu zimene anthu amenewa amachita. Komabe, kodi Mulungu si amene amanena ngati chinthu chili chachibadwa kapena ayi? Iye analamula anthu ake akale kuti: “Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi, chonyansa ichi.”—Levitiko 18:22.

Mudzafunika Kuyankha kwa Mulungu

Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu savomereza kapena kulekerera kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Iye amadananso ndi anthu ‘ovomerezana ndi iwo akuchita’ zimenezi. (Aroma 1:32) Ndipo amuna okhaokha kapena akazi okhaokha akanena kuti akwatirana sizitanthauza kuti kugonana kwawo tsopano kwasanduka kolemekezeka. Lamulo la Mulungu loti “ukwati uchitidwe ulemu ndi onse” limatanthauza kuti sangavomereze ukwati wa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, umene amauona kuti ndi chinthu chonyansa.—Ahebri 13:4.

Komabe, ndi thandizo la Mulungu, aliyense akhoza kuphunzira ‘kudzipatula ku dama,’ limene limaphatikizapo kugonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, ndipo akhoza “kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu.” (1 Atesalonika 4:3, 4) Koma n’zoona kuti nthawi zina kuchita zimenezi sikukhala kophweka. Nathan *, amene kale ankagonana ndi amuna anzake anati: “Ndinkaganiza kuti sindingathe kusiya kuchita zimenezi.” Koma anasintha ndi thandizo la “Mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:11) Monga momwe Nathan anazindikirira, palibe vuto limene lili lalikulu kwambiri moti Yehova sangalithe, chifukwa Iye amapereka mphamvu ndi thandizo lofunika kuti munthu athe kutsatira mfundo Zake ndi kulandira madalitso Ake.—Salmo 46:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mboni za Yehova sizichita nawo zionetsero kapena makampeni a ndale alionse ofuna kusintha malamulo a m’dziko mwawo, ngakhale malamulowo akhale osemphana ndi zimene chikumbumtima chawo chimawauza chifukwa choti aphunzira Baibulo.

^ ndime 14 Si dzina lake lenileni.

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Photo by Chris Hondros/Getty Images