Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Oonerera Opanda Chitetezo

Oonerera Opanda Chitetezo

Oonerera Opanda Chitetezo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU FINLAND

KWA ana ambiri, zinthu ngati mafilimu, ma TV, mavidiyo, ma DVD, masewera a pakompyuta, ndi Intaneti ndi zinthu zoti amaonerera kapena kugwiritsa ntchito nthawi zonse. Bungwe loyang’anira za mafilimu ku Finland posachedwapa linafalitsa lipoti linalake. Lipotilo linati “malinga ndi kafukufuku wina, nthawi imene ana ndi achinyamata amakhala akuonerera kapena kugwiritsa ntchito TV, kompyuta ndi zinthu zina zotero ndi yochuluka kuwirikiza ka 20 mpaka ka 30 kuposa nthawi imene amacheza ndi anthu a m’banja mwawo.” * Koma n’zomvetsa chisoni kuti zimenezi zimachititsa ana kuonerera zinthu zoipa zambiri.

M’mayiko ena, akuluakulu a boma amayesera kuteteza ana pokhazikitsa misinkhu yoyenera kuonerera mapulogalamu enaake ndiponso zizindikiro zodziwira ngati pulogalamu ili yabwino kapena yoipa. Koma malinga ndi lipotilo, ana ndi makolo awo nthawi zambiri samvetsa tanthauzo la zizindikirozo, kapena amaona ngati n’zosafunika kwenikweni. Kuwonjezera apo, malo ambiri oonetsa makanema kapena obwereketsa mavidiyo satsatira malamulo a misinkhu ya anthu omwe ayenera kuonerera mafilimuwo. Komanso mapulogalamu ndi mafilimu ena sakhala ndi zizindikiro zosonyeza ngati ali abwino kapena oipa.

Mmodzi mwa aphunzitsi amene anafunsidwa nawo mafunso pa kafukufukuyo anati: “Zikuoneka kuti ana a sukulu saona kuti filimu ndi yoipa ngati mulibe kukhetsana magazi.” Mavidiyo ndi masewera a pakompyuta ambiri, ndiponso ngakhale mafilimu osonyeza zidole zikulankhula amene anakonzedwera makamaka ana aang’ono, amakhala ndi zinthu zoipa zomwe zingawavulaze.

Lipotilo linati banja lililonse lili ndi “udindo waukulu wosankha mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV abwino oti ana azionerera.” Lipotilo linamaliza ndi funso lofunika kwambiri lakuti: “Kodi achikulirefe tili ndi chilakolako, mphamvu, ndi njira zotetezera ana athu kuti asaonerere zinthu zoipa zomwe zingathe kuwavulaza?”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Lipotilo linali lotchedwa “Misinkhu Yoyenera Kuonerera Mapulogalamu Enaake, Ndiponso Kuteteza Ana” ndipo linalembedwa atachita kafukufuku amene anaphatikizapo ana a sukulu 340 a ku pulayimale limodzi ndi makolo awo ndi aphunzitsi awo.