Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zingathandize Achinyamata Masiku Ano

Zimene Zingathandize Achinyamata Masiku Ano

Zimene Zingathandize Achinyamata Masiku Ano

ACHINYAMATA masiku ano akukulira m’dziko limene nthawi zina limaoneka lochititsa mantha kwambiri. Ena a iwo amasowa chochita pamene akuona makolo awo akupatukana kapena kusudzulana. Ena amaona anzawo a kusukulu akuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita zaumbanda. Ambiri amakakamizidwa ndi anzawo kuti agonane, ndiponso kuti agonane amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Ndipo pafupifupi achinyamata onse nthawi zina amavutika chifukwa choona kuti palibe amene akuwamvetsa, chifukwa chosungulumwa, ndiponso chifukwa cha matenda a maganizo.

Kodi achinyamata amafunika chiyani kuti athe kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo? Dr. Robert Shaw analemba kuti: “Ana amafunika kukhala ndi kwinakwake komwe angapezeko mfundo zodalirika za makhalidwe abwino, zomwe zingawathandize kupeza anzawo abwino, kusankha bwino zochita, ndi kumvera anthu ena chisoni.” Baibulo lili ndi mfundo za makhalidwe abwino zothandiza kwambiri, chifukwa lili ndi maganizo a Mlengi wathu. Kodi palinso wina kuposa Yehova Mulungu amene angadziwe zomwe tikufunikira kuti zinthu zitiyendere bwino mu nthawi zovuta zomwe tikukhala zino?

Baibulo Lili ndi Malangizo Othandizadi

Mfundo za m’Baibulo zimathandizadi, makamaka kwa makolo ndi anthu ena achikulire amene akufuna kuthandiza achinyamata kuti zinthu ziwayendere bwino pamene akukula.

Mwachitsanzo, Baibulo limavomereza kuti “utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” Kapena, monga momwe Baibulo la Today’s English Version limanenera, “ana mwachibadwa amachita zinthu zopusa, zopanda nzeru.” (Miyambo 22:15) Achinyamata ena amachita zinthu zachikulu poyerekezera ndi msinkhu wawo, komabe akadali ana osadziwa zambiri. Choncho amadzikayikira, amakhala ndi zilakolako zinazake, ndiponso amavutika maganizo. Zinthu zimenezi zimachitikira aliyense akamakula. (2 Timoteo 2:22) Kodi achinyamata amenewa angathandizidwe bwanji?

Baibulo limalimbikitsa makolo ndi ana kulankhulana bwino nthawi zonse. Limalimbikitsa makolo kuti aziphunzitsa mwachangu ana awo mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu ‘pokhala pansi m’nyumba zawo, ndi poyenda panjira, ndi pogona pansi, ndi pouka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Kulankhulana koteroko kumathandiza m’njira ziwiri. Choyamba, kumaphunzitsa wachinyamatayo njira za Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Chachiwiri, kumalimbikitsa makolo ndi ana kukambirana zinthu. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka pamene ana akusanduka achikulire, chifukwa pa nthawi imeneyi akhoza kudzipatula n’kukhala osungulumwa.

N’zoona kuti achinyamata ambiri amasungulumwa nthawi zina kwa nthawi yochepa. Koma ena amangokhala osungulumwa nthawi zonse. Buku lina la achinyamata linati: “Achinyamata amenewa amanena kuti zimawavuta kupeza anzawo kusukulu, alibe munthu amene angacheze naye, amasungulumwa, zimawavuta kuchititsa ana ena kuwakonda, ndiponso amaona kuti palibe amene angalankhule naye akafunika thandizo.” *

Makolo ndi achikulire ena ofuna kuthandiza angakhale ndi chidwi ndi achinyamata n’kuwathandiza kulimbana ndi mavuto awo. Angachite zimenezi motani? Mkonzi wamkulu wa magazini ina ya achinyamata anati: “Njira yokhayo yodziwira zimene achinyamata akuganiza ndiyo kuwafunsa.” Mwachidziwikire, pamafunika nthawi ndi kuleza mtima kuti mulimbikitse achinyamata kukuululirani mavuto amene akuwadetsa nkhawa. Koma musatope, chifukwa kuchita zimenezi mwakhama kuli ndi phindu lake.—Miyambo 20:5.

Amafunika Kuwaikira Malire

Kuwonjezera pa kulankhulana bwino, achinyamata amafunika kuti muwaikire malire, ndipo pansi pa mtima amafuna zimenezo. Baibulo limati, “mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Akatswiri akukhulupirira kuti kusaikira ana malire ooneka bwino mwina n’kumene kumachititsa achinyamata ambiri kuphwanya malamulo. Shaw, amene tamutchula kale uja anati: “Ngati mwana nthawi zonse mumangomulola kuchita zilizonse zomwe akufuna ndipo simumuletsa chilichonse, saphunzira zoti anthu ena alinso ndi moyo wawo, maganizo, zosowa, ndi zofuna zawo. Akapanda kuphunzira kumvera ena chisoni, mwanayo sadzatha kukonda anthu ena.”

Dr. Stanton Samenow, amene wagwira ntchito ndi ana ovuta kwa zaka zambiri, anafotokoza maganizo omwewo. Iye analemba kuti: “Makolo ena amaganiza kuti ana ayenera kuchita chilichonse chomwe akufuna. Molakwa, amaganiza kuti kumuikira mwana malire kapena kumuuza zochita n’kumulemetsa ndiponso kumuwonongera ubwana wake. Koma ngati alephera kumuikira malire, zotsatira zake zingakhale zoipa kwambiri. Makolo amenewa sazindikira kuti mnyamata kapena mtsikana amene salangidwa angavutike kuphunzira kudziletsa.”

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti makolo ayenera kungokhala ovuta basi? Ayi. Kuika malire ndi mbali imodzi yokha yolera bwino ana. Ngati kuchitidwa monyanyira, kuika malamulo ambiri okhwima kungachititse kuti pakhomo pasamasangalatse. Baibulo limati: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”—Akolose 3:21; Aefeso 6:4.

Choncho, nthawi ndi nthawi makolo ayenera kuonanso bwinobwino njira zawo zophunzitsira ndi kulangira ana awo, makamaka anawo akamakula n’kuyamba kusonyeza kuti akukhwima maganizo. Mwina malamulo kapena ziletso zina mukhoza kuzichepetsako kapena kuzisintha, malinga ndi zinthu zimene mwanayo akuchita zosonyeza kuti wayamba kukhala wodalirika.—Afilipi 4:5.

Kulimbikitsa Mgwirizano

Monga momwe nkhani yapita ija yasonyezera, Baibulo linaneneratu kuti dzikoli lidzakumana ndi “nthawi zowawitsa” Mulungu asanachitepo kanthu kuti athetse kuipa padziko pano. Umboni ukusonyeza kuti tikukhala mu nthawi imeneyo, mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu losamvera Mulungu lino. Mofanana ndi achikulire, achinyamata ayenera kupirira m’dziko limene ladzaza ndi anthu “odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakhoza kudziletsa.”—2 Timoteo 3:1-5. *

Makolo amene akuona kuti anasiya kulankhulana bwino ndi mwana wawo angachitepo kanthu kuti ayambirenso kugwirizana naye, poyambiranso kulankhula naye pang’onopang’ono. N’zoyamikirika kuti makolo ambiri akuyesetsa kuthandizadi ana awo ndi kudziwa zomwe zikuchitika pamoyo wa anawo.

Baibulo n’lothandiza kwambiri pankhani imeneyi. Lathandiza makolo ambiri kukwanitsa udindo wawo ndiponso lathandiza achinyamata kupewa misampha imene ikanatha kuwapweteka kwambiri. (Deuteronomo 6:6-9; Salmo 119:9) Popeza Baibulo n’lochokera kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, tingakhulupirire kuti lili ndi mfundo zothandiza kwambiri kwa achinyamata masiku ano. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Buku lomwelo linati mosiyana ndi wachinyamata amene amasungulumwa nthawi zina, achinyamata ena amakhala osungulumwa nthawi zambiri ndiponso kwa nthawi yaitali. Wachinyamata woteroyo “amakhulupirira kuti adzakhala wopanda mnzake mpaka kalekale, kuti palibe chomwe angachite kuti asinthe zimenezo, ndiponso kuti zimenezi zili choncho chifukwa choti iyeyo ali ndi vuto.” Amakhulupiriranso kuti zinthu “sizingasinthe, kapena sizidzasintha.”

^ ndime 16 Onani mutu 11 m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 18 Mboni za Yehova zapeza kuti buku lofotokoza za m’Baibulo lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza n’lothandiza kwambiri. Mutu uliwonse mwa mitu yake 39 umayankha funso lochititsa chidwi. Nayi mitu yake ina: “Kodi Ndingapange Bwanji Mabwenzi Enieni?” “Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanga?” “Kodi Ndingachititse Motani Kusukidwa Kwanga Kuchoka?” “Kodi Ndili Wokonzekera Kupalana Ubwenzi?” “Kodi Nkuneneranji Kuti Ayi ku Mankhwala Oledzeretsa?” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?”

[Chithunzi patsamba 10]

Uzani nkhawa zanu wachikulire amene amafuna kukuthandizani