Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinthu Sizikuwayendera Bwino Achinyamata

Zinthu Sizikuwayendera Bwino Achinyamata

Zinthu Sizikuwayendera Bwino Achinyamata

▪ Ku United States, mwana wa sukulu wa zaka 15 anaombera ana a sukulu anzake a m’kalasi mwawo, ndipo anapha anthu awiri n’kuvulaza anthu 13.

▪ Ku Russia, gulu la achinyamata oledzera linapha mwankhanza mtsikana wa zaka nayini n’kumenyanso bambo ake ndi msuweni wake.

▪ Ku Britain, mnyamata wa zaka 17 anamenya ndi kubaya ndi mpeni mnyamata wina wocheperapo. Iye anauza apolisi kuti: “Poyamba sikuti ndimafuna kumupha, koma nditaona kuti wayamba kutuluka magazi, basi ndinangoganiza zomumalizitsa.”

ZINTHU zosakhulupirika ngati zimenezi sikuti zikungochitika mwa apo ndi apo ayi, ndipo sitinganene kuti zimenezi ndi zinthu zachilendo zosachitikachitika. Nkhani ina ya m’magazini yotchedwa Professional School Counseling inati: “Vuto la achinyamata ochita zachiwawa lakula kwambiri masiku ano.” Zinthu zomwe zakhala zikuchitika zikugwirizana ndi mawu amenewa.

Bungwe loona zochitika m’masukulu ku United States lotchedwa U.S. National Center for Education Statistics linati, ngakhale kuti m’dziko limenelo ziwawa zochitika m’masukulu zachepako, “ana a sukulu a zaka zoyambira 12 mpaka 18 anachitidwa ziwawa koma osaphedwa kapena anaberedwa nthawi zokwana mamiliyoni awiri m’chaka cha 2001.” Ndipo ana a sukulu opezerera anzawo akuti awonjezekanso.

Koma sikuti ziwawa zonse zomwe achinyamata amachita ku United States amachitira ana a sukulu anzawo okha basi. Bungwe tinalitchula lija linanenanso kuti “pa zaka zisanu zochokera mu 1997 kufika mu 2001, aphunzitsi anachitidwa ziwawa koma osaphedwa nthawi zopitirira wani miliyoni ku sukulu, kuphatikizapo kuberedwa nthawi 817,000 ndi kuchitidwa ziwawa za mtundu wina nthawi 473,000.” Kuwonjezera apo, “aphunzitsi 9 pa aphunzitsi 100 alionse a kupulayimale ndi kusekondale anawopsezedwa ndi mwana wa sukulu kuti akhoza kuwapweteka, ndipo aphunzitsi 4 pa aphunzitsi 100 alionse anamenyedwa ndi mwana wa sukulu.”

Nanga kodi zinthu zili bwanji m’mayiko ena? Bungwe lina lofalitsa nkhani linati, “m’dziko la China, achinyamata ophwanya malamulo okwana 69,780 anamangidwa mu 2003,” kusonyeza kuti anawonjezeka kuposa mu 2002. Bungwe lofalitsa nkhanilo linati achinyamata ambiri amene anaphwanya malamulo anali m’magulu a zigawenga. Lipoti lochokera ku Japan mu 2003 linanenanso kuti achinyamata ndi amene anapalamula theka la milandu yonse imene inachitika pa zaka teni zapitazi.

Mankhwala Osokoneza Bongo Akuwononga Kwambiri Matupi a Achinyamata

Umboni wina wosonyeza kuti zinthu sizili bwino ndi wokhudza mmene achinyamata ambiri akuwonongera matupi awo. Lipoti limene linafalitsidwa ndi bungwe loona za kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo lotchedwa U.S. National Institute on Drug Abuse linati, pafupifupi theka la achinyamata onse a ku United States amakhala atagwiritsako ntchito mankhwala osokoneza bongo asanamalize sukulu ya sekondale. Lipotilo linapitirizanso kuti: “Achinyamata ambiri amamwa mowa masiku ano. Pafupifupi ana a sukulu anayi pa ana a sukulu asanu alionse amakhala atamwako mowa (osati kungolawa chabe) akamamaliza sukulu ya sekondale; ndipo pafupifupi theka amakhala atamwako mowa akamafika giredi eyiti.”

Chiwerewere

Masiku ano pamene Edzi yafalikira, kuchita chiwerewere n’koopsa kwabasi. Komabe, achinyamata ambiri amaona ngati kugonana ndi masewera chabe. Mwachitsanzo, achinyamata ena a ku United States ayamba kugwiritsa ntchito mawu atsopano okuluwika, omveka ngati akukamba za nkhani yamasewera, akamanena za kugonana kwachisawawa. Amanena zoti ali ndi anzawo oti azigona nawo akafuna. Anzawo oterewa amakhala oti si zibwenzi zawo ndiponso oti sadandaula ndi kugonana koteroko.

Wolemba nkhani wina dzina lake Scott Walter anafotokozapo za mapwando kumene anthu amagonana ndi anthu ambirimbiri. Iye anati achinyamata ena okhala m’mizinda amachita mapwando oterewa makolo awo ali kuntchito. Paphwando limodzi loterolo, mtsikana wina analengeza kuti “agona ndi anyamata onse amene anali pamenepo. . . . Kumapwando oterowo kunkapezeka ana aang’ono kwambiri, ena a zaka 12 zokha.”

Zimenezi n’zinthu zovuta kumvetsa, si choncho? Koma si zodabwitsa kwa akatswiri amene afufuza khalidwe la achinyamata pankhani ya kugonana. Dr. Andrea Pennington analemba kuti: “Pa zaka 20 zapitazi, taona kuti zaka zimene achinyamata akumayamba kugonana zikucheperachepera. Si zachilendonso kuona anyamata ndi atsikana aang’ono kwambiri, ena a zaka 12 zokha, akuyamba kugonana.”

Pankhani imeneyi, lipoti lina limene linatuluka m’nyuzipepala ya USA Today linali lodetsa nkhawa kwambiri. Lipotilo linati: “Achinyamata aang’ono kwambiri a m’dziko muno ochulukirachulukira . . . akumagonana m’kamwa. . . . Achinyamata ayamba kukhulupirira kuti ‘kumeneku sikugonana kwenikweni.’” Malinga ndi kafukufuku wina wa atsikana 10,000, “atsikana 80 pa atsikana 100 alionse anati anali anamwali, koma atsikana 25 pa atsikana 100 alionse anali atagonanapo m’kamwa ndi munthu wina. Ndipo atsikana 27 pa atsikana 100 alionse anati ‘munthu umachita zimenezo ndi mnyamata kuti usangalale basi.’”

Maganizo ngati amenewo pa nkhani ya kugonana afalikiranso m’mayiko ena. Bungwe la UNESCO linati: “Achinyamata ambiri a ku Asia ali pangozi yoti akhoza kutenga kachilombo ka HIV kudzera m’njira ya kugonana chifukwa ambiri a iwo akumayamba kugonana ali aang’ono.” Ndipo bungwelo linawonjezera kuti: “Achinyamata ambiri sakutsatiranso chikhalidwe cha makolo awo cha ku Asia ndipo akumagonana asanalowe m’banja, komanso nthawi zambiri amagonana ndi anthu osiyanasiyana.”

Kodi zizindikiro zina zoti achinyamata zinthu sizikuwayendera bwino n’zotani? Magazini ina ya ku Canada yotchedwa Women’s Health Weekly inati: “Atsikana 25 pa atsikana 100 alionse a zaka za pakati pa 16 ndi 19 adzadwala matenda aakulu a maganizo.” Komabe, matenda a maganizo amagwira anyamata ndi atsikana omwe. Malinga ndi lipoti la U.S.News & World Report, chaka chilichonse achinyamata okwana 5,000 amadzipha. Lipotilo linati, pa chifukwa chosadziwika bwino, “anyamata amadzipha kwambiri kuwirikiza kasikisi kuposa atsikana.”

Mosakayikira, mbadwo wa achinyamata a masiku ano uli pamavuto kwambiri. Kodi n’chiyani chikuchititsa mavuto amenewa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

STR/AFP/Getty Images