Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Akufunafuna Mayankho

Achinyamata Akufunafuna Mayankho

Achinyamata Akufunafuna Mayankho

Pamene mwambo wachikatolika wa nambala 17 wokumbukira Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse unachitika mu 2002 ku Toronto, m’dziko la Canada, anthu masauzande ambiri anapita kumeneko kuchokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Ngakhale kuti Mboni za Yehova sizinachite nawo mwambowo, zinadziwa kuti mu mzindawo mudzafika achinyamata ambirimbiri. Kodi Mbonizo zinakonzekera bwanji zimenezi? Mogwirizana ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira, izo zinapezerapo mpata wolankhula zinthu za m’Malemba ndi anthuwo.—Machitidwe 16:12, 13.

Mbonizo zinayamikira achinyamatawo chifukwa chokonda zinthu zauzimu. Zimenezi zinachititsa kuti acheze bwino ndi anthu ambiri pa nkhani za m’Malemba. Mboni ina inafunsa mtsikana wina ngati zimene zinali kuchitika pa mwambo wokumbukira Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse umenewo zinali zogwirizana ndi zimene anali kuyembekezera. Mtsikanayo anayankha kuti: “Mpaka pano, zomwe zachitika ndizo kuimba ndi kuvina kokha basi, koma sipakuchitika chilichonse chomwe chikulimbitsa chikhulupiriro changa.”

Mboniyo kenaka inapatsa mtsikanayo kabuku kotchedwa Buku la Anthu Onse, ndipo inafotokoza kuti kamayankha mafunso ambiri amene anthu afunsapo okhudza Baibulo, monga akuti “Kodi ndi Mawudi a Mulungu?” ndiponso “Kodi tingadziwe bwanji kuti silinasinthe kuchokera pamene linalembedwa?”

Mtsikanayo anayankha kuti: “Amenewo ndi mafunso amene akundizunguza mutu pamoyo wanga panopa. Ndikufunika kupeza mayankho a mafunso amenewa. Ndikufuna ndiwerenge kabuku kameneka pompanopa. Mwina kabuku kameneka kakhala chinthu chaphindu kwambiri chomwe ndipeze pa ulendo wanga wonsewu.”

Ameneyo anali munthu mmodzi yekha mwa anthu ambiri omwe Mboni zinacheza nawo, omwe anabwera ku mwambo wachikatolika wokumbukira Tsiku la Achinyamata Padziko Lonse. Ngati nanunso mungakonde kulandira kabuku ka masamba 32 kakuti Buku la Anthu Onse, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Buku la Anthu Onse.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.