Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akuonetsa Mafilimu Ati Chilimwe Chino?

Kodi Akuonetsa Mafilimu Ati Chilimwe Chino?

Kodi Akuonetsa Mafilimu Ati Chilimwe Chino?

KODI chilimwe chikafika mumaganiza zochita chiyani? Kunja kukayamba kutentha, mwina mumaganiza zokayenda, mwina kunyanja kapena ku malo kwinakwake kosangalatsa.

Koma anthu amene amapanga mafilimu amakhulupirira kuti anthu ochuluka adzathera maola ambiri a m’chilimwe ali m’nyumba zoonetsera mafilimu. Ku United States kokha kuli malo oonetsera mafilimu pafupifupi 35,000, ndipo m’zaka zaposachedwapa pafupifupi theka la ndalama zonse zomwe amapeza akagulitsa matikiti oonera mafilimu m’dziko limenelo amazipeza m’chilimwe. * Heidi Parker, amene amalemba magazini inayake yonena za mafilimu (Movieline) anati: “Zili ngati ndalama zimene amalonda amapanga nthawi ya Khirisimasi.”

Koma zimenezi sikuti zinali chonchi kale. Nthawi ya chilimwe ku United States anthu ambiri sankapita koonera mafilimu, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti malo ambiri oonetsera mafilimu azionetsa mafilimu ochepa chabe kapena aziwatseka m’chilimwe. Koma pofika zaka za pakati pa m’ma 1970, malo oonetsera mafilimu okhala ndi makina oziziritsira mpweya anayamba kukopa anthu amene amafuna kuthawa kutentha. Ana a sukulu amene amakhala ali patchuthi anali gulu lina la anthu lomwe likanatha kubweretsera anthu oonetsa mafilimu ndalama zambiri, ndipo opanga mafilimu anazindikira zimenezi. Pasanapite nthawi yaitali, anayamba kutulutsa filimu yotchuka chilimwe chilichonse. Mafilimu oterewa anasintha kapangidwe ndi katsatsidwe ka mafilimu, monga momwe tionere.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ku United States, nyengo ya mafilimu a m’chilimwe imayamba mu May ndipo imatha mu September.