Kodi Yesu Kristu Ndi Ndani?
Kodi Yesu Kristu Ndi Ndani?
MALINGA ndi mbiri yakale yodalirika, munthu wotchedwa Yesu anabadwa zaka zopitirira 2,000 zapitazo ku Betelehemu, yomwe inali tawuni yaing’ono ku Yudeya. Herode Wamkulu anali mfumu ku Yerusalemu panthawi imeneyo, ndipo Kaisara Augusto anali mfumu ya Roma. (Mateyu 2:1; Luka 2:1-7) Anthu ophunzira mbiri yakale achiroma a m’zaka 200 zoyambirira nthawi zambiri sankatchula za Yesu, popeza atsogoleri achiroma panthawi imeneyo ankafuna kupondereza Chikristu.
Komabe, buku linalake la mbiri yakale (The Historians’ History of the World), linati: “Zochita za [Yesu] zinasintha kwambiri mbiri kuposa zochita za munthu wina aliyense, ngakhale tikapanda kuganizira za chipembedzo. Nyengo yatsopano, imene mayiko ambiri otukuka a padzikoli amaivomereza, inayambira pa kubadwa kwa [Yesu].”
Magazini inayake (Time) inati mabuku ambiri alembedwa onena za Yesu kuposa onena za munthu wina aliyense m’mbiri. Ambiri a mabuku amenewa amayankha makamaka funso lakuti kodi Yesu ndi ndani kwenikweni. Mwina pakhala kutsutsana kwakukulu pa nkhani imeneyi kuposa pa nkhani ina iliyonse m’mbiri ya anthu.
Amene Anayambirira Kufunsa Kuti Yesu Ndi Ndani
Pamene Mariya anauzidwa kuti adzakhala ndi mwana ndipo adzamutcha dzina lake Yesu, anafunsa kuti: “Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?” Mngelo wa Mulungu Gabrieli anayankha kuti: ‘Mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.’—Luka 1:30-35.
Patapita nthawi, Yesu anachita zozizwitsa zimene zinadabwitsa atumwi ake. Pamene namondwe wamkulu anatsala pang’ono kumiza bwato lawo pa Nyanja ya Galileya, Yesu anakhazikitsa bata panyanjapo pokalipira namondweyo kuti: “Tonthola, khala bata.” Podabwa, atumwi ake anafunsa kuti: ‘Uyu ndani nanga?’—Marko 4:35-41; Mateyu 8:23-27.
Anthu ambiri pa nthawi ya Yesu ankafunsa kuti kodi Yesu ndi ndani, choncho iye anafunsa atumwi ake kuti kodi anthu ankanena kuti iyeyo ndi ndani. Iwo anayankha kuti: “Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.” Anthu onsewa anali atafa kale. Kenaka Yesu anafunsa kuti: “Koma inu mutani kuti Ine ndine Mateyu 16:13-16; Luka 4:41.
yani?” Poyankha, Simoni Petro anati: ‘Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’ Ngakhale ziwanda, zomwe ndi angelo oipa, zinati kwa Yesu: ‘Inu ndinu Mwana wa Mulungu.’—Kodi Yesu Ananena Kuti Iye Anali Ndani?
Ngakhale kuti Yesu sankakonda kunena kuti anali Mwana wa Mulungu, iye anavomereza zimenezo. (Marko 14:61, 62; Yohane 3:18; 5:25, 26; 11:4) Koma nthawi zambiri ankanena kuti anali ‘Mwana wa munthu.’ Ponena kuti iye anali mwana wa munthu, ankagogomezera kubadwa kwake monga munthu, kuti iye analidi munthu weniweni. Choncho anadzisonyezanso kukhala “mwana wa munthu” amene Danieli anaona m’masomphenya. Danieli anaona mwana wa munthuyo akuonekera pamaso pa Mulungu Wamphamvuyonse, “Nkhalamba ya kale lomwe.”—Mateyu 20:28; Danieli 7:13.
M’malo molengeza kuti iye anali Mwana wa Mulungu, Yesu ankafuna kuti anthu azindikire okha zimenezi. Ndipo ngakhale anthu amene sanali atumwi ake anazindikira zimenezo, kuphatikizapo Yohane Mbatizi ndi Marita yemwe anali mnzake wa Yesu. (Yohane 1:29-34; 11:27) Anthu amenewa anakhulupirira kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa. Iwo anazindikira kuti Yesu poyamba anali kumwamba ngati munthu wauzimu wamphamvu ndipo Mulungu anasamutsa mozizwitsa moyo wake n’kuuika m’mimba mwa namwali Mariya.—Yesaya 7:14; Mateyu 1:20-23.
Kufanana Kwake ndi Munthu Woyamba, Adamu
M’mbali zambiri, Yesu anali wofanana ndi munthu woyamba, Adamu. Mwachitsanzo, awiri onsewa anali anthu angwiro amene analibe bambo waumunthu. (Genesis 2:7, 15) Choncho Baibulo limati Yesu anali ‘Adamu wotsiriza,’ munthu wangwiro amene akanatha kukhala ‘chiwombolo m’malo mwa onse.’ Moyo wa Yesu unali wofanana ndi wa “munthu woyamba, Adamu,” amene Mulungu anamulenga wangwiro.—1 Akorinto 15:45; 1 Timoteo 2:5, 6.
M’Baibulo, Adamu woyamba amatchedwa “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Komabe, Adamu ameneyo anataya ubwenzi wamtengo wapatali umene anali nawo ndi Mulungu monga mwana wake mwa kusamvera dala Mulungu. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu anali wokhulupirika kwa Atate ake a kumwamba nthawi zonse, ndipo anakhalabe Mwana wokondweretsa Mulungu. (Mateyu 3:17; 17:5) Baibulo limati anthu onse amene amakhulupirira Yesu, ndi kuvomereza kuti iye ndi Mpulumutsi wawo, akhoza kulandira moyo wosatha.—Yohane 3:16, 36; Machitidwe 5:31; Aroma 5:12, 17-19.
Komabe, anthu ena amanena kuti Yesu sikuti ndi Mwana wa Mulungu chabe komanso kuti iye ndi Mulungu. Amanena kuti Yesu ndiponso Atate ake onse awiri ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi zimenezo n’zoona? Kodi tinganene kuti Yesu ndi mbali inanso ya Mulungu? Kodi zimenezo n’zimene Yesu kapena wolemba Baibulo wina aliyense ananena? Indedi, kodi Mulungu woona yekha ndi ndani? Kodi Yesu anati Mulungu woona yekha ndi ndani? Tiyeni tione.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]
Palibenso Munthu Wina Wodziwika Kuposa Yesu
Nkhani ya moyo wa Yesu inalembedwa ndi anthu anayi omwe analipo nthawi imeneyo, Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane. Awiri mwa amenewa anali anzake apamtima a Yesu. Mabuku a anthu anayiwa, amene mayina ake ali ofanana ndi mayina a anthuwo, nthawi zambiri amatchedwa mauthenga abwino. Mbali za mabuku amenewa azimasulira m’zinenero zopitirira masauzande awiri. Mabuku ang’onoang’ono amenewa nthawi zambiri amawaphatikiza ndi mabuku ena amene amapanga Baibulo. Mabuku a mauthenga abwino amene agulitsidwa, kaya pawokha kapena monga mbali ya Baibulo lathunthu, ndi ochuluka kwambiri kuposa mabuku ena onse m’mbiri. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu ndi wodziwika kwambiri kuposa munthu wina aliyense amene anakhalako.
[Chithunzi patsamba 15]
Atumwi anafunsa kuti ‘Uyu ndani nanga?’