Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchoka pa Nkhani Kufika pa Filimu

Kuchoka pa Nkhani Kufika pa Filimu

Kuchoka pa Nkhani Kufika pa Filimu

PA ZAKA zingapo zapitazi, makampani opanga mafilimu ku America atulutsa mafilimu ambiri otchuka ndiponso obweretsa phindu lalikulu la ndalama. Zimenezi zakhudza dziko lonse lapansi, chifukwa mafilimu ambiri a ku America amawatulutsa m’mayiko ena patangotha milungu yochepa, ndipo nthawi zina masiku ochepa, atawatulutsa ku United States. Ndipo mafilimu ena amatulutsidwa padziko lonse lapansi tsiku lomwelo. Dan Fellman, pulezidenti woyang’anira za malonda a mafilimu ku United States pa kampani inayake yotchuka yopanga mafilimu (Warner Brothers Pictures) anati: “Malonda a mafilimu padziko lonse lapansi akukula ndipo akusangalatsa kwambiri, choncho tikamapanga mafilimu, timaona kuti tili ndi mwayi wotha kuwagulitsa padziko lonse lapansi.” Masiku ano, kuposa kale lonse, zomwe zimachitika ku America zimakhudza makampani a asangalatsi padziko lonse lapansi. *

Koma kupeza phindu pa filimu sichinthu chophweka ngati momwe tingaganizire. Mafilimu ambiri amafunika apange ndalama zoposa madola wani handiredi miliyoni kuti angobweza chabe ndalama zomwe anapangira ndi kutsatsira malonda filimuyo. Ndipo zoti kaya iyenda malonda kapena ayi zimadalira anthu oonerera amene makonda awo amakhala ovuta kudziwiratu. David Cook, pulofesa wa maphunziro a mafilimu pa yunivesite inayake ku United States (Emory University), anati: “Simungathe kudziwa kuti anthu panthawi yakutiyakuti adzakonda filimu yamtundu wanji.” Choncho kodi anthu opanga mafilimu amatani kuti filimu yawo idzayende malonda? Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tiyenera kumvetsa zinthu zingapo zokhudza momwe amapangira mafilimu. *

Ntchito Imene Amagwira Asanayambe Kupanga Filimu

Ntchito yomwe amagwira asanayambe kupanga filimu nthawi zambiri ndi imene imatenga nthawi yaitali kwambiri popanga filimu ndiponso ndi mbali imodzi yofunika kwambiri. Monga momwe zimakhalira ndi ntchito iliyonse yaikulu, kukonzekera n’kofunika kwambiri. Cholinga chake chimakhala choti ndalama iliyonse yomwe awononga asanayambe kupanga filimu ithandize kuti asadzawononge ndalama zambiri akamadzapanga filimuyo.

Kupanga filimu kumayamba ndi kupeza nkhani yake, yomwe ikhoza kukhala yopeka kapena yochokera ku zochitika zenizeni. Munthu wodziwa kulemba amalemba nkhaniyo. Nkhani yolembedwayo akhoza kuisintha kambirimbiri isanafike poti asangalatsidwa nayo ndipo yafika poti akhoza kuigwiritsa ntchito pojambula filimuyo. Nkhani yomalizirayi imakhala ndi mawu a filimuyo komanso imafotokoza mwachidule zomwe ziyenera kuchitika pojambula filimuyo. Imaperekanso malangizo kwa opanga filimuyo, monga pofunika kuika kamera ndi zomwe ziyenera kuchitika pakati pa magawo a filimuyo.

Nkhaniyi ili kumayambiriro kwenikweni kolembedwa m’pamene amaigulitsa kwa mkonzi wa mafilimu. * Kodi ndi nkhani yotani imene mkonzi wa mafilimu angakonde? Nthawi zambiri mafilimu a m’chilimwe amapangira kwenikweni achinyamata a zaka 13 mpaka 19 ndi achinyamata a zaka 20 mpaka 25, “amene amakonda kudya chimanga cha mbuluuli” akamaonera filimu, malinga ndi zomwe ananena munthu winawake wodziwa bwino za mafilimu. Choncho mkonzi angakopeke ndi nkhani imene imakhudza kwambiri achinyamata.

Nkhani imene imakhala bwino kwambiri ndi imene imakhudza anthu a misinkhu yosiyanasiyana. Mwachitsanzo, filimu yokhudza munthu wotchuka wa m’magazini yazithunzi ingakope kwambiri ana aang’ono amene amamudziwa bwino munthuyo. Ndipo mosakayikira makolo awo angapite nawo limodzi kukaonera filimuyo. Koma kodi opanga mafilimu amakopa bwanji achinyamata? Liza Mundy analemba m’magazini inayake (The Washington Post Magazine) kuti, “chinsinsi chake chagona pa kuikamo zinthu zokopa kwambiri.” Kuikamo mawu otukwana, mbali zosonyeza chiwawa choopsa kwambiri, ndi kugonana kwambiri ndi njira imodzi “yothandizira kuti filimu ipange ndalama zambiri poonetsetsa kuti anthu a msinkhu uliwonse athe kukopeka nayo.”

Ngati mkonzi akuona kuti nkhaniyo ikhoza kukhala filimu yabwino, akhoza kuigula n’kuyesa kupeza munthu wotchuka wotsogolera mafilimu ndi munthu wotchuka wochita mafilimu kuti adzachite nawo filimuyo. Kukhala ndi munthu wotchuka wotsogolera mafilimu ndiponso munthu wotchuka wochita mafilimu kumachititsa anthu kukopeka ndi filimuyo ikatuluka. Komabe, ngakhale isanatuluke, kukhala ndi anthu otchuka popanga filimuyo kungakope anthu oti aikepo ndalama zothandizira kuti filimu ipangidwe.

Ntchito ina yomwe imachitika asanayambe kupanga filimu ndiyo kujambula zithunzi za magawo a filimuyo. Zithunzi zimenezi zimasonyeza mbali zosiyanasiyana za filimuyo, makamaka magawo amene anthu amafunika kuchitapo zinthu zinazake. Zithunzizi zimakhala ngati pulani ya munthu amene adzatsogolere ntchito yojambula filimuyo ndipo zimachepetsa nthawi imene ingawonongeke pojambula. Monga momwe munthu wina wotsogolera ndi kulemba nkhani za mafilimu dzina lake Frank Darabont ananenera, “palibenso chimene chimakwiyitsa kwambiri kuposa kungoimaima pa malo ojambulira filimu kuwononga nthawi yanu yojambulira filimuyo pofunafuna malo abwino oti muike kamera.”

Pali zinthu zinanso zambiri zomwe zimafunika kuzikonzeratu ntchito yojambula filimu isanayambike. Mwachitsanzo, kodi adzajambulira kuti filimuyo? Kodi padzafunika kupita ku malo kwina? Kodi zinthu za m’nyumba zidzaikidwa bwanji? Kodi padzafunika zovala zapadera? Ndani adzayendetse ntchito yokhudzana ndi kuunika, zodzoladzola kumaso, ndi kukonza tsitsi la ochita filimuyo? Nanga bwanji za mawu, zithunzi ndi kuwala kwapadera, ndiponso anthu othandizira kuchita mbali zina zovuta za filimuyo? Izi ndi zinthu zochepa chabe pa ntchito yopanga mafilimu zimene ayenera kuganizira asanayambe n’komwe kujambula filimuyo. Mukaona mawu amene amawasonyeza filimu yotchuka ikatha mudzaona kuti pamakhala anthu ambirimbiri amene amagwira nawo ntchito zosiyanasiyana koma zosaonekera popanga filimuyo. Munthu wina wogwira ntchito zaluso amene wapanga nawo mafilimu ambiri anati: “Pamafunika chikhamu cha anthu kuti mupange filimu yotchuka.”

Kujambula Filimu

Kujambula filimu kukhoza kukhala ntchito yotha nthawi, yosasangalatsa, ndiponso yotha ndalama. Indedi, kungowononga mphindi imodzi yokha kungakudyereni masauzande ambiri a ndalama. Nthawi zina anthu ochita filimu, othandizira, ndi katundu, amafunika kuwapititsa ku dziko linalake lakutali. Koma kaya akujambulira kuti, tsiku lililonse lomwe akujambula filimu ndalama zambiri zimawonongeka.

Anthu oona za kuunika, okonza tsitsi, ndi odziwa za zodzoladzola kumaso ndiwo ena mwa anthu amene amakhala oyambirira kufika pa malo ojambulira filimu. Tsiku lililonse lojambula filimu, anthu ochita filimuyo akhoza kutha maola angapo akuwakonzakonza kuti aoneke bwino. Kenaka amayamba kujambula, kumene kumatenga tsiku lonse.

Wotsogolera filimuyo amaonetsetsa mmene akujambulira gawo lililonse. Ngakhale gawo losavuta likhoza kutenga tsiku lonse pojambula. Magawo ambiri m’filimu amawajambula ndi kamera imodzi, choncho gawo lililonse amalijambula kambirimbiri kuchokera pamalo osiyanasiyana. Kuwonjezera apo, angafunike kujambula mobwerezabwereza gawo lomwelomwelo kuti ajambule pamene achita bwino kwambiri kapena kuti akonze vuto linalake. Akamajambula magawo aakulu, amakhoza kujambula zinthu zomwezomwezo nthawi 50 kapena kuposa pamenepo. Kenaka, mwina akamaliza kujambula tsiku limenelo, wotsogolera amaonerera zonse zomwe ajambula ndipo amasankha zomwe ayenera kusunga. Ntchito yojambulayi ikhoza kutenga milungu ingapo, ngakhale miyezi kumene.

Ntchito Yosonkhanitsa Mbali Zonse Pamodzi Akatha Kujambula

Akatha kujambula, amasankha mbali zomwe akuzifuna n’kuzilumikiza kuti zikhale filimu imodzi. Choyamba, amaika pamodzi mawu ndi zithunzi. Kenaka mkonzi amasonkhanitsa mbali zosiyanasiyana za filimuyo n’kupanga filimu yoyambirira.

Panthawi imeneyi m’pamene amaphatikizanso mawu ndi zithunzi zapadera. Nthawi zina amagwiritsa ntchito makompyuta kuti apange zithunzi zapaderazo. Imeneyi ndi imodzi mwa ntchito zovuta kwambiri popanga filimu. Zotsatira zake zikhoza kukhala zochititsa chidwi ndiponso zooneka ngati zenizenidi.

Amaphatikizanso nyimbo panthawi imeneyi ndipo mbali imeneyi masiku ano ikukhala yofunika kwambiri m’mafilimu. Edwin Black analemba m’magazini inayake yonena za nyimbo za m’mafilimu (Film Score Monthly) kuti: “Opanga mafilimu masiku ano akufuna nyimbo zochuluka kuposa kale zomwe anazikonzera filimuyo basi. Samangofuna nyimbo zokwana mphindi 20 basi kapena zongoimba panthawi zofunika kwambiri m’filimuyo, koma nthawi zambiri amafuna nyimbo zopitirira ola lathunthu.”

Nthawi zina filimu yomwe angomaliza kumene kuikonza amaionetsa kwa anthu angapo, mwina anzake a wotsogolera filimuyo kapena anthu ogwira nawo ntchito limodzi amene sanapange nawo filimuyo. Malinga ndi zomwe anganene anthu amenewa, wotsogolerayo angajambulenso magawo ena kapena kuwachotsa. Nthawi zina asinthapo mathero onse a filimu chifukwa choti anthu omwe anaiona koyambirira sanasangalale nawo.

Pamapeto pake filimuyo ikatha amaitulutsa m’malo oonetsera mafilimu. Panthawi imeneyi m’pamene zimayamba kudziwika kuti kaya filimuyo iyenda malonda kapena anthu sasangalala nayo, kapena ikhala pakatim’pakati. Koma sikuti ndi ndalama zokha basi zomwe zingawonongeke Ngati munthu wochita kapena wotsogolera mafilimu apanga mafilimu angapo omwe anthu sanasangalale nawo, wochita filimuyo akhoza kulephera kupezanso ntchito zina, ndipo mbiri ya wotsogolerayo ikhoza kuwonongeka. Wotsogolera mafilimu wina dzina lake John Boorman anati: “Ndinaona anzanga angapo akulowa pansi pambuyo potulutsa mafilimu angapo osasangalatsa. Vuto la ntchito yopanga mafilimu n’loti ngati ukulephera kupangira mabwana ako ndalama, amakuchotsa ntchito.”

Koma anthu akaima pakhomo la nyumba zoonetsera mafilimu, maganizo awo sakhala pa ntchito za anthu opanga mafilimuwo. Mosiyana ndi zimenezo, iwo mwina amakhala akudzifunsa mafunso ngati oti: ‘Kodi filimu imeneyi ndisangalala nayo? Kodi ikugwirizana ndi ndalama zomwe ndalipira kuti ndiionere? Kodi filimu yake ikhala yoipa kapena yonyansa? Kodi ndi yoyenera kwa ana anga?’ Kodi mungayankhe bwanji mafunso amenewa posankha mafilimu oti muonere?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Anita Elberse, pulofesa wa pa yunivesite inayake yotchuka ku United States (Harvard Business School), anati: “Ngakhale kuti masiku ano mafilimu nthawi zambiri amapanga ndalama zambiri kunja kwa dziko la United States kusiyana ndi zomwe amapanga m’dzikolo, ndalama zomwe filimu yapanga ku United States ndi chizindikiro chofunikabe kwambiri cha momwe malonda ake ayendere kunja.”

^ ndime 3 Ngakhale kuti mafilimu akhoza kuwapanga mosiyanasiyana, zimene tifotokoze pano ndi njira imodzi yomwe angapangire mafilimu.

^ ndime 7 Nthawi zina mkonzi amamutsatsa nkhani yachidule, osati yolembedwa mwatsatanetsatane. Ngati waikonda nkhaniyo, akhoza kuigula n’kupeza anthu oti amalizitse kuilemba.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Simungathe kudziwa kuti anthu panthawi yakutiyakuti adzakonda filimu yamtundu wanji.” Anatero David Cook, pulofesa wa maphunziro a mafilimu

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 6, 7]

KUTSATSA MALONDA KUTI FILIMU IKHALE YOTCHUKA KWAMBIRI

Filimuyo yatha tsopano. Anthu mamiliyoni ambiri tsopano akhoza kuiona. Kodi anthu aikonda? Taganizirani njira zingapo zimene anthu opanga mafilimu amagwiritsa ntchito potsatsa malonda filimu yawoyo kuti itchuke kwambiri.

MPHEKESERA: Njira imodzi yabwino kwambiri yokopera anthu kuti azifuna kuona filimu ndiyo kudzera m’manong’onong’o a anthu, kapena kuti mphekesera. Nthawi zina mphekesera zimenezi zimayamba kumveka miyezi ingapo filimuyo isanatuluke. Mwina amalengeza kuti atulutsa filimu yachiwiri yotsatizana ndi ina yomwe inatuluka kale. Kodi ochita filimu amene anali mu filimu yoyamba ija alimonso mu yachiwiriyi? Kodi idzakhala yabwino (kapena yoipa) ngati yoyamba ija?

Nthawi zina, mphekesera zimabuka chifukwa cha kusiyana maganizo pa mbali inayake ya filimuyo, mwina zithunzi zosonyeza kugonana zimene zili zoipa kwambiri poganizira kuti filimuyo idzaonedwa ndi aliyense. Kodi gawo limenelo n’loipadi ngati momwe anthu akuneneramo? Kodi filimuyo yapyola malire ovomerezeka? Anthu opanga mafilimu amasangalala anthu akamatsutsana pa nkhani inayake yokhudza filimuyo chifukwa amakhala akuwatsatsira malonda kwaulere. Nthawi zina kutsutsana kumene kumabukako kumachititsa kuti anthu ambiri apite kukaonerera filimuyo akamaionetsa koyamba.

ZIKWANGWANI, MANYUZIPEPALA, MA TV, NDI ZINA ZOTERO: Nthawi zambiri potsatsa malonda a filimu amagwiritsa ntchito zikwangwani, manyuzipepala, kapena ma TV. Amathanso kuonetsa mbali zina za filimuyo anthu asanaonere filimu yomwe abwera kudzaonera m’malo oonetsera mafilimu, ndi kufunsa mafunso anthu ochita mafilimu akamanena za mafilimu awo amene achita posachedwapa. Masiku ano Intaneti ndi imene anthu akugwiritsa ntchito kwambiri potsatsa mafilimu.

MALONDA A ZINTHU ZINA: Kugulitsa zinthu zina potsatsa malonda a filimuyo kungachititse kuti anthu atengeke nayo maganizo isanatuluke. Mwachitsanzo, filimu inayake yokhudza munthu wotchuka wa m’buku lazithunzi asanaitulutse anagulitsa mabokosi oikamo zakudya, makapu, zibangili, ndolo, zovala, zitsulo zoikapo makiyi, mawotchi, nyali zamagetsi, masewero a papepala, ndi zina zambiri zomwe analembapo zinthu zokhudzana ndi filimuyo. Joe Sisto analemba m’magazini inayake yosangalatsa anthu a m’bungwe linalake la maloya (American Bar Association) kuti: “Nthawi zambiri, pafupifupi theka la zinthu zina zotsatsa malonda a filimu zimagulitsidwa filimuyo isanatuluke n’komwe.”

MAVIDIYO OONERA KUNYUMBA: Filimu imene sinapange ndalama zambiri ku malo oonetsera mafilimu ingakokere ndi ndalama zochokera ku malonda a mavidiyo amene anthu amaonera kunyumba kwawo. Bruce Nash, amene amatsata bwino momwe mafilimu amapangira ndalama, anati “malonda a mavidiyo amabweretsa pafupifupi theka la ndalama zonse zomwe mafilimu amapanga.”

ZIZINDIKIRO ZOSONYEZA NGATI FILIMU ILI YABWINO KAPENA YOIPA: Anthu opanga mafilimu aphunzira kugwiritsa ntchito zizindikiro zosonyeza ngati filimu ili yabwino kapena yoipa kuti ziwathandize kutsatsa malonda a mafilimu awo. Mwachitsanzo, angaike dala zinthu zinazake m’filimu kuti aipatse chizindikiro choti ndi yoipa, n’cholinga choti akope anthu achikulire. Komanso, nthawi zina angachotsemo zinthu zoipa zochepa kuti asaipatse chizindikiro choti ndi yoipa, n’cholinga choti akope achinyamata. Liza Mundy analemba m’magazini inayake (The Washington Post Magazine) kuti chizindikiro chosonyeza kuti filimu ndi yoyenera achinyamata “chasanduka njira yotsatsira malonda a mafilimu. Opanga mafilimu amagwiritsa ntchito zimenezi kutumizira uthenga achinyamata, ndi ana amene amafuna kuonera mafilimu a achinyamata, kuti filimuyo idzakhala ndi zinthu zokoma kwabasi.” Chizindikirocho chimapereka “uthenga wosiyana kwa makolo ndi ana awo,” analemba choncho Mundy, chifukwa “chimachenjeza makolo koma chimakopa ana.”