Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinatha Kutumikira Mulungu Ngakhale Zinali Zovuta

Ndinatha Kutumikira Mulungu Ngakhale Zinali Zovuta

Ndinatha Kutumikira Mulungu Ngakhale Zinali Zovuta

YOSIMBIDWA NDI IVAN MIKITKOV

“Ngati ukhalabe m’tawuni yathu ino, tikutumizanso kundende,” anandichenjeza choncho wapolisi wa bungwe la chitetezo cha boma lotchedwa Soviet State Security Committee (KGB). Ndinali nditangotulutsidwa kumene m’ndende nditakhalamo zaka 12. Mayi ndi bambo anga anali akudwala kwambiri ndipo amafunika kuti ndikawathandize. Kodi ndikanachita bwanji pamenepa?

NDINABADWA mu 1928 m’mudzi wa T̩aul m’dziko la Moldova. * Pamene ndinali ndi chaka chimodzi, bambo anga a Alexander anakacheza ku Ias̩i ku Romania, kumene anakumana ndi Ophunzira Baibulo, amene panopa amatchedwa Mboni za Yehova. Atabwerera ku T̩aul, anauza anthu a m’banja mwawo ndi oyandikana nawo nyumba zinthu zimene anaphunzira kwa Ophunzira Baibulo aja. Posakhalitsa gulu laling’ono la Ophunzira Baibulo linapangidwa ku T̩aul.

Popeza ndinali mwana wamng’ono kwambiri m’banja la ana aamuna anayi, kuyambira ndili khanda nthawi zonse ndinkakhala ndi anthu okonda zinthu zauzimu, amene anandipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. M’kupita kwa nthawi, ndinazindikira kuti potumikira Yehova ndidzakumana ndi chitsutso, ndiponso kuti zidzakhala zovuta. Ndimakumbukira bwino apolisi akufufuza m’nyumba mwathu kambirimbiri, kufuna mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene tinabisa. Zimenezi sizinandichititse mantha. Ndinaphunzira pamene tinali kukambirana za m’Baibulo kuti ngakhale Mwana wa Mulungu amene, Yesu Kristu, komanso ophunzira ake, anazunzidwa. Pamisonkhano yathu nthawi zambiri ankatikumbutsa kuti otsatira Yesu ayenera kuyembekezera kuzunzidwa.—Yohane 15:20.

Ndinalimbikitsidwa Kuti Ndithe Kuthana ndi Chizunzo

Mu 1934, pamene ndinali ndi zaka sikisi zokha, anawerenga kalata mu mpingo wathu ku T̩aul yotiuza za kuzunzika kwa Akristu anzathu m’dziko la Germany limene linali kulamulidwa ndi Anazi. Anatilimbikitsa kuti tiziwapempherera. Ngakhale kuti ndinali ndidakali mwana, ndimaikumbukirabe kalata imeneyo.

Patatha zaka zinayi kuchokera nthawi imeneyi, ndinakumana ndi chiyeso choyamba cha chikhulupiriro changa. Panthawi ya maphunziro a chipembedzo kusukulu, wansembe wa mpingo wa Orthodox anandiuza mobwerezabwereza kuti ndivale korona m’khosi mwanga. Nditakana, anauza ana onse m’kalasimo kuti avale korona wawo posonyeza kuti anali anthu opemphera opita ku tchalitchi. Kenaka wansembeyo anafunsa anthu a m’kalasimo uku akundiloza ineyo kuti: “Kodi mukufuna munthu ngati uyu m’kalasi mwanu muno? Onse amene sakumufuna aimike manja.”

Popeza ana a sukuluwo ankaopa wansembeyo, onse anaimika manja awo. Akunditembenukira ineyo, wansembeyo anati: “Ukuona, palibe amene akufuna kukhala mnzako. Choka m’nyumba ino pompanopa.” Patapita masiku angapo, mkulu wa sukuluyo anabwera kunyumba kwathu. Atatha kulankhula ndi makolo anga, anandifunsa ngati ndinkafuna kupitiriza sukulu. Ndinamuuza kuti ndinkafuna. Iye anayankha kuti: “Kwa nthawi yonse imene ine ndili mkulu wa sukulu imeneyi, uzibwera kusukulu ndipo wansembeyo sadzakuvutitsanso.” Iye anasungadi mawu ake ndipo kwa nthawi yonse yomwe anali mkulu wa sukuluyo, wansembe uja sanandivutitsenso.

Chizunzo Chikula

Mu 1940, dera lomwe tinali kukhalamo, lotchedwa Bessarabia, linakhala mbali ya dziko la Soviet Union. Pa June 13 ndi 14, m’chaka cha 1941, anthu onse amene anali otchuka pandale kapena m’njira zina anasamutsidwira ku dziko la Siberia. Mboni za Yehova sizinakhudzidwe ndi kusamutsidwa kumeneku. Koma kuyambira nthawi imeneyo kupita m’tsogolo, tinkachita misonkhano yathu ndi kulalikira mosamala.

Kumapeto kwa mwezi wa June mu 1941, dziko la Germany molamulidwa ndi Anazi mwadzidzidzi linaukira dziko la Soviet Union, lomwe kufika mpaka pa nthawi imeneyo linali kumbali yake. Pasanapite nthawi yaitali, asilikali a dziko la Romania analandanso dera la Bessarabia. Zimenezi zinatibweretsanso pansi pa ulamuliro wa dziko la Romania.

M’midzi ina yapafupi nafe, Mboni zimene zinakana kulowa gulu la asilikali achiromaniya zinamangidwa, ndipo zambiri mwa izo zinalamulidwa kukhala zaka 20 m’ndende zozunzirako anthu. Bambo anaitanidwa kuti apite ku polisi ndipo anamenyedwa kwambiri chifukwa choti anali Mboni. Ndiponso, ineyo ndinatengedwa mwankhanza ku sukulu kuti ndizikapemphera nawo m’tchalitchi.

Zochitika pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse zinasintha. Mu March 1944, dziko la Soviet Union linalanda dera la kumpoto kwa Bessarabia m’kanthawi kochepa. Pofika mu August, linali litalanda dziko lonselo. Ine ndinali ndi zaka pafupifupi 20 zokha pa nthawi imeneyo.

Pasanapite nthawi yaitali, anthu onse a thanzi labwino a m’mudzi wathu analembedwa usilikali m’gulu la asilikali a boma la Soviet Union. Koma Mboni zinakana kutenga nawo mbali pa nkhondo. Choncho zinalamulidwa kukhala zaka teni m’ndende. Mu May 1945, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha ku Ulaya pamene dziko la Germany linavomereza kuti lagonja. Komabe, Mboni zambiri ku Moldova zinakhalabe m’ndende mpaka mu 1949.

Kuvutika Nkhondo Itatha

Nkhondo itatha mu 1945, m’dziko la Moldova munagwa chilala choopsa. Ngakhale kunali chilala choterocho, boma la Soviet Union linapitirizabe kukakamiza alimi kuti azipereka mbali yaikulu ya zokolola zawo ngati msonkho. Zimenezi zinachititsa kuti kukhale njala yoopsa. Pofika mu 1947, ndinali nditaona mitembo yambirimbiri ya anthu m’misewu ya ku T̩aul. Mchimwene wanga Yefim anamwalira, ndipo kwa milungu ingapo ndinali wofooka kwambiri chifukwa cha njala moti ndinkalephera kuyenda. Koma kenaka njalayo inatha, ndipo Mboni zimene tinapulumukafe tinapitiriza ntchito yathu yolalikira. Ine ndinkalalikira m’mudzi wathu, pamene mchimwene wanga Vasile, amene anali wamkulu ndi zaka seveni kuposa ine, ankalalikira m’midzi yoyandikana nayo.

Pamene Mboni zinayamba kulimbikira kwambiri ntchito yawo yolalikira, akuluakulu a boma anayamba kutiyang’anitsitsa zochita zathu. Chifukwa cha kulalikira kwathu, komanso chifukwa chakuti sitinkachita nawo zandale kapena ntchito yausilikali, boma la Soviet Union linayamba kufufuza mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’nyumba zathu ndi kutimanga. Mu 1949, Mboni zina za m’mipingo yoyandikana ndi mpingo wathu anazisamutsira ku Siberia. Choncho, kachiwirinso, ife amene tinatsalafe tinayamba kuchita utumiki wathu mosamala kwambiri.

Panthawi imeneyi, ndinayamba kudwala matenda amene ankangoipiraipira. Pomalizira pake madokotala anandiuza kuti ndinali ndi TB ya m’mafupa, ndipo mu 1950 mwendo wanga wamanja anauika mu pulasitala.

Kusamutsidwira ku Siberia

Pa April 1, 1951, mwendo wanga ukadali mu pulasitala, ine ndi anthu a m’banja mwathu limodzi ndi Mboni zina tinamangidwa ndipo anatisamutsira ku Siberia.  * Popeza tinalibe nthawi yokwanira yoti tikonzekere, tinangotenga zakudya zochepa zokha ndipo zinatha patangotha nthawi yochepa.

Kenaka, titatha pafupifupi milungu iwiri tili m’sitimayo, tinafika ku Asino, m’chigawo cha Tomsk. Kumeneko anatitsitsa m’sitimamo ngati ng’ombe. Ngakhale kuti kunali kukuzizira kwambiri, tinasangalala kwambiri kupumanso mpweya wabwino. Mu May, pamene madzi oundana a mumtsinje anayamba kusungunuka, anatikweza sitima yapamadzi n’kuyenda nafe ulendo wa makilomita 100 kutipititsa ku Torba, kumene kunali malo ochekerako matabwa m’dera lozizira la nkhalango ya ku Siberia. Kunoko tinayamba ukaidi wathu wogwira ntchito yakalavula gaga, umene anatiuza kuti sudzatha.

Ngakhale kuti kugwira ntchito yakalavula gaga pamalo ochekera matabwa kunali kosiyana ndi kukhala m’ndende, nthawi zonse ankayang’anitsitsa zochita zathu. Usiku anthu a m’banja mwathu tinkagona limodzi mu bogi ya sitima. Nyengo yofunda imeneyo tinamanga nyumba, zomwe mbali imodzi zinali pansi pa nthaka mbali ina pamwamba, kuti zidzatiteteze m’nyengo yozizira yomwe inali kubwera.

Chifukwa mwendo wanga unali mu pulasitala, anandilola kuti ndisamagwire nawo ntchito m’nkhalango, ndipo anandipatsa ntchito yopanga misomali. Ntchito imeneyi inandipatsa mwayi wochita nawo mwakabisila ntchito yokopa magazini a Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo. Mwa njira inayake mabuku amenewa nthawi ndi nthawi ankalowetsedwa mwakabisira m’dera lathu kuchokera kumadzulo kwa Ulaya, komwe kunali kutali makilomita masauzande ambiri.

Kugwidwa ndi Kuikidwa M’ndende

Mu 1953, mwendo wanga uja anauchotsa mu pulasitala. Koma panthawi imeneyi, ngakhale kuti ndinali wosamala kwambiri, ntchito yanga yauzimu, kuphatikizapo kukopa mabuku ofotokoza za m’Baibulo, inadziwika ndi apolisi a KGB. Chifukwa cha zimenezi, ine pamodzi ndi Mboni zina, ndinalamulidwa kukhala m’ndende yozunzirako anthu kwa zaka 12. Koma panthawi ya mlandu wathu, tonsefe tinapereka umboni wabwino kwambiri wa Mulungu wathu, Yehova, ndi zolinga zake zabwino kwa anthu.

Akaidife pomalizira pake anatitumiza ku ndende zozunzirako anthu zosiyanasiyana kufupi ndi ku Irkutsk, womwe unali ulendo wa makilomita ambiri kupita kummawa. Ndende zimenezi anazimanga kuti zikhale malo ozunzirako anthu amene ankaonedwa kuti anali adani a dziko la Soviet Union. Kuyambira pa April 8, 1954, mpaka kumayambiriro kwa 1960, ndinakhala m’ndende 12 zoterozo. Kenaka anandisamutsa kuyenda mtunda wa makilomita 3,000 kumadzulo kupita ku dera lalikulu lokhala ndi ndende zambirimbiri zozunzirako anthu ku Mordovia, pafupifupi makilomita 400 kummwera chakummawa kwa mzinda wa Moscow. Kumeneko ndinakhala ndi mwayi wokumana ndi Mboni zokhulupirika zochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko la Soviet Union.

Akuluakulu a boma la Soviet Union anazindikira kuti Mboni akazilola kucheza ndi akaidi ena omwe sanali Mboni, ena a iwo ankakhalanso Mboni. Choncho ku ndende za ku Mordovia, kumene kunali ndende zozunzirako anthu zambirimbiri pa malo okwana mtunda wa makilomita 30 kapena kuposa pamenepo, anayesetsa kutilekanitsa kuti tisamacheze ndi akaidi ena. Mboni pafupifupi 400 anaziika pamodzi m’ndende yathu. Pa mtunda wa makilomita angapo kuchoka pamenepa, alongo pafupifupi 100 anawaika m’ndende ina pagulu la ndende zimenezi.

M’ndende yathu, ndinachita khama kuthandiza nawo pa ntchito yokonza misonkhano yachikristu komanso kukopa mabuku ofotokoza za m’Baibulo, omwe analowetsedwa mwakabisira m’ndendemo. Zikuoneka kuti oyang’anira ndendewo anadziwa za ntchito imeneyi. Patangotha nthawi yochepa, mu August 1961, anandilamula kukakhala chaka chimodzi ku ndende yoipa kwambiri yomwe inamangidwa panthawi ya ulamuliro wa ma czar yotchedwa Vladimir. Ndendeyi inali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 200 kumpoto chakummawa kwa Moscow. Munthu woyendetsa ndege wa ku United States, dzina lake Francis Gary Powers, amene ndege yake anaiwombera pa May 1, 1960, pamene ankauluka pamwamba pa dziko la Russia kuti achite zaukazitape, nayenso anali m’ndende imeneyi mpaka mu February 1962.

Pamene ndinali ku ndende ya Vladimir, ankandipatsa chakudya chochepa kwambiri chongokwanira kuti ndisafe. Ndinatha kupirira njala, chifukwa ndinapirira nayo ndili mwana, koma kuzizira koopsa kwa m’chaka cha 1961ndi 1962 n’kumene ndinavutika nako kwambiri. Mapaipi otenthetsa m’chipinda anali atawonongeka, ndipo m’chipinda mwanga munazizira kwambiri kufika poundana madzi. Dokotala wina anaona kuti moyo wanga unali pangozi, ndipo anakonza zoti andisamutsire m’chipinda china m’ndendemo momwe munali mosazizira kwambiri pa milungu imene kunja kunali kuzizira kwambiri.

Ndinalimbikitsidwa Kuti Ndithe Kulimbana ndi Zovutazo

Munthu akhoza kukhala ndi maganizo ofooketsa atakhala miyezi yambiri ali m’ndende, ndipo zimenezi n’zimene oyang’anira ndende amafuna. Komabe, ndinkapemphera nthawi zonse ndipo ndinalimbikitsidwa ndi mzimu wa Yehova ndiponso malemba amene ndinkakumbukira.

Makamaka pamene ndinali m’ndende ya Vladimir m’pamene ndinagwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo oti ndinali ‘wopanikizidwa mwa mtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha’ ndipo ‘ndinathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.’ (2 Akorinto 4:8-10) Patatha chaka chimodzi, anandibwezeretsa ku ndende zozunzirako anthu za ku Mordovia zija. Ku ndende zimenezi, ndinamaliza ukaidi wanga wa zaka 12 pa April 8, 1966. Pamene anali kunditulutsa m’ndende, pofotokoza khalidwe langa anati ndine “wokanika kusintha.” Kwa ine, umenewo unali umboni woonekeratu wakuti ndinakhala wokhulupirika kwa Yehova.

Nthawi zambiri ndafunsidwapo kuti tinatha bwanji kulandira ndi kukopa mabuku ofotokoza za m’Baibulo tili m’ndende za boma la Soviet Union ngakhale kuti ankayesetsa kutiletsa kuchita zimenezi. Ndi chinsinsi chimene ochepa okha akuchidziwa, monga momwe ananenera mkaidi wina wa ku Latvia amene anamangidwa pazifukwa za ndale ndipo anatha zaka zinayi m’ndende ya azimayi ku Potma. Iye atatuluka m’ndende mu 1966 analemba kuti: “Mboni mwa njira inayake zinkathabe kulandira mabuku ambirimbiri.” Iye anamaliza ndi kunena kuti: “Zinkakhala ngati angelo ankauluka pamwamba usiku n’kumagwetsa mabukuwo.” Zoonadi, tinatha kukwanitsa ntchito yathu chifukwa cha thandizo la Mulungu basi.

Nthawi ya Ufulu Pang’ono

Nditatulutsidwa, amene anali kutsogolera ntchito yolalikira anandipempha kuti ndisamukire ku madzulo kwa dziko la Ukraine, kufupi ndi dziko la Moldova, kuti ndikathandize abale athu a ku Moldova. Komabe, popeza kale ndinali mkaidi ndipo apolisi a KGB anali kuonetsetsa zomwe ndinali kuchita, sindikanatha kuchita zambiri. Patatha zaka ziwiri, ndinasamukira ku dziko la Kazakhstan lolamulidwa ndi boma la Soviet Union, komwe akuluakulu a boma sankafufuza kwambiri mapepala olowera m’dziko, ngakhale kuti akanati andigwire akanatha kunditumizanso kundende. Kenaka mu 1969, pamene makolo anga anadwala kwambiri, ndinasamukira ku Ukraine kuti ndikawasamalire. Ndili kumeneko, m’tawuni ya Artyomosk, kumpoto kwa mzinda waukulu wa Donetsk, wapolisi wa KGB anandiopseza kuti akhoza kunditumizanso kundende, monga momwe ndanenera poyambirira pa nkhani ino.

Koma kenaka ndinadzazindikira kuti wapolisiyo ankangofuna kundiopseza basi. Analibe umboni wokwanira woti akanatha kundimangira. Popeza ndinkafunitsitsa kupitiriza utumiki wanga wachikristu ndipo apolisi a KGB akanandilondalondabe kulikonse komwe ndikanapita, ndinapitiriza kusamalira makolo anga. Bambo ndi mayi anga anamwalira ali okhulupirikabe kwa Yehova. Bambo anamwalira mu November 1969, koma amayi anakhalabe ndi moyo mpaka mu February 1976.

Pamene ndinabwereranso ku Ukraine, ndinali ndi zaka 40. Pamene ndinkasamalira makolo anga kumeneko, ndinkasonkhana mu mpingo umodzi ndi mtsikana wina dzina lake Maria. Iye anali ndi zaka eyiti zokha pamene, mofanana ndi banja lathu, iye limodzi ndi makolo ake anasamutsidwa ku Moldova kupita ku Siberia kumayambiriro kwa mwezi wa April mu 1951. Maria anati ankakonda mmene ndinkaimbira. Chimenechi chinali chiyambi cha ubwenzi wathu, ndipo ngakhale kuti tonsefe tinali otanganidwa mu utumiki, tinatha kupeza nthawi yokulitsa ubwenzi wathu. Pofika mu 1970, anavomera zoti tikwatirane.

Posakhalitsa mwana wathu wamkazi Lidia, anabadwa. Kenaka mu 1983, pamene Lidia anali ndi zaka teni, munthu amene kale anali Mboni anandipereka kwa apolisi a KGB. Panthawi imeneyo ndinali nditatha zaka pafupifupi teni ndikutumikira ngati woyang’anira woyendayenda kumadzulo konse kwa dziko la Ukraine. Anthu otsutsa ntchito yathu anatha kupeza anthu oti apereke umboni wabodza pamlandu wanga, ndipo ndinalamulidwa kukhala m’ndende kwa zaka zisanu.

Ndili m’ndende anandilekanitsa ndi Mboni zina. Ngakhale kuti ndinakhala wolekanitsidwa ndi anthu ena choncho kwa zaka zambiri, palibe munthu aliyense kapena chinthu chilichonse chomwe chikanandiletsa kulankhula ndi Yehova, ndipo nthawi zonse Yehova anandilimbikitsa. Kuwonjezera apo, ndinapeza mipata yolalikira kwa akaidi ena. Kenaka, nditakhala m’ndende zaka zinayi, ndinatulutsidwa n’kuyambiranso kukhalira limodzi ndi mkazi wanga ndi mwana wathu wamkazi. Onse awiriwa anakhala okhulupirikabe kwa Yehova.

Kubwereranso ku Moldova

Tinakhala chaka china chimodzi ku Ukraine ndipo kenaka tinabwerera ku Moldova kukakhaliratu kumeneko, komwe kumafunika abale okhwima mwauzimu kuti akathandize. Panthawi imeneyi, boma la Soviet Union linkatiloleza kuyenda momasukako kuposa kale. Tinafika ku Bălţi mu 1988, kumene Maria ankakhala asanasamutsidwire ku Siberia zaka 37 m’mbuyomo. Mu 1988, mu mzinda wachiwiri kwa mzinda waukulu kwambiri mu Moldova monse umenewu munali Mboni pafupifupi 375. Tsopano muli Mboni zopitirira 1,500. Ngakhale tinkakhala ku Moldova, ndinkatumikirabe ngati woyang’anira woyendayenda ku Ukraine.

Pofika panthawi imene gulu lathu linavomerezedwa ndi boma ku Soviet Union mu March 1991, anthu ambiri anali atakhumudwa ndi kulephera kwa Chikomyunizimu. Ambiri anali osowa pogwira ndiponso analibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo. Choncho pamene dziko la Moldova linakhala dziko lodziimira palokha, ambiri mwa anthu oyandikana nafe nyumba ndiponso ngakhale anthu amene kale ankatizunza anakhala ndi chidwi kwambiri kuti tiwalalikire. Titasamutsidwira ku Siberia mu 1951, Mboni zochepa zokha n’zimene zinatsala ku Moldova, koma tsopano m’dziko laling’ono la anthu pafupifupi 4,200,000 limeneli muli Mboni zopitirira 18,000. Kuvutika kwathu kwam’mbuyomu kwafafanizika ndi zokumana nazo zosangalatsa zomwe takhala nazo.

M’zaka za m’ma 1990, ndinafunika kusiya kutumikira ngati woyang’anira woyendayenda chifukwa cha kudwala. Nthawi zina ndimakhumudwa chifukwa cha matenda angawo. Koma ndazindikira kuti Yehova amadziwa zimene timafunikira kuti tilimbikitsidwe. Amatipatsa chilimbikitso chomwe tikufunikira panthawi yoyenera. Ndikanakhala ndi mwayi wokhalanso moyo wanga kachiwiri, kodi ndikanasankha moyo wamtundu wina? Ayi. M’malo mwake ndimalakalaka ndikanakhala wolimba mtima kwambiri mu utumiki wanga m’mbuyomu ndiponso wachangu kwambiri.

Ndikuona kuti Yehova wandidalitsa ndiponso kuti atumiki ake onse ndi anthu odala kaya akhale ndi moyo wotani. Tili ndi chiyembekezo chowala, chikhulupiriro cholimba, ndipo ndife otsimikiza kuti posachedwapa aliyense adzakhala ndi thanzi labwino m’dziko latsopano limene Yehova watilonjeza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Dzina la panopa la dzikoli, lakuti Moldova, ndi limene tigwiritse ntchito mu nkhani ino, osati mayina ake akale akuti Moldavia kapena Moldavian Soviet Socialist Republic.

^ ndime 21 Kumapeto kwa milungu iwiri yoyambirira ya m’mwezi wa April 1951, akuluakulu a boma la Soviet Union anagwira mwadongosolo Mboni za Yehova zopitirira 7,000 ndi mabanja awo zomwe zinali kukhala kumadzulo kwa dziko la Soviet Union n’kuzikweza sitima kuyenda nazo ulendo wa makilomita ambiri kuzisamutsira ku dziko la Siberia.

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Nyumba yathu pamene tinasamutsidwira ku Torba ku Siberia mu 1953. Bambo ndi mayi (kumanzere), ndi mchimwene wanga Vasile ndi mwana wake (kumanja)

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili m’ndende yozunzirako anthu mu 1955

[Chithunzi patsamba 31]

Alongo achikristu ku Siberia, pamene Maria (amene ali pansi kumanzere) anali ndi zaka 20

[Chithunzi patsamba 31]

Tili ndi mwana wathu, Lidia

[Chithunzi patsamba 31]

Ukwati wathu mu 1970

[Chithunzi patsamba 31]

Ndili ndi Maria masiku ano