Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene “Mulungu Woona Yekha” Walonjeza

Zimene “Mulungu Woona Yekha” Walonjeza

Zimene “Mulungu Woona Yekha” Walonjeza

YEHOVA MULUNGU anaika mwamuna ndi mkazi oyambirira m’paradaiso pa dziko lapansi, m’munda wa Edene. Iye anawauza kuti akhale ndi ana ndipo ‘agonjetse dziko lapansi,’ zomwe zikutanthauza kuti akanayenera kufutukula malo awo okhala a Paradaiso pamene banja lawo linali kukula. (Genesis 1:26-28; 2:15) Kodi cholinga cha Mulungu choti anthu akhale m’paradaiso pa dziko lapansi chidzakwaniritsidwa?

Inde, chidzakwaniritsidwa. Malinga ndi ulosi wa m’Baibulo, “[Yehova] wameza imfa ku nthawi yonse” ndipo “adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” Zimenezi zikadzachitika, anthu “adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tam’lindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tam’lindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.”—Yesaya 25:8, 9.

Buku lomalizira la m’Baibulo limafotokoza momwe dziko lapansili lidzakhalire, dongosolo la zinthu lolamulidwa ndi Satanali likadzachotsedwa. Ponena za “dziko latsopano” lopangidwa ndi anthu okonda Mulungu, Baibulo limati: “Chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:1-4.

Amenewa ndi malonjezo osangalatsadi kwambiri. Kodi tingawakhulupirire? Taonani momwe imfa ya Yesu yansembe, ndiponso zozizwitsa zomwe anachita zimatipatsira umboni wokhulupirira kuti Mulungu adzachita zilizonse zomwe walonjeza.—2 Akorinto 1:20.

Yesu Anapereka Moyo Wake Ngati Dipo

Satana atachititsa Adamu kusamvera Mulungu ndi kuchimwa, ana onse a Adamu anatengera uchimo wake. Baibulo limati: “Monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” Komabe, nkhani ya m’Baibuloyo imapitiriza kuti: “Ndi kumvera kwa mmodzi [munthu wangwiro, Yesu] ambiri adzayesedwa olungama.” (Aroma 5:12, 19) Monga momwe tafotokozera mu nkhani yoyambirira ya nkhani zino, Yesu ndiye ‘Adamu wotsiriza,’ amene “ali wakumwamba,” ndipo anapereka moyo wake ngati “dipo la anthu ambiri.”—1 Akorinto 15:45, 47; Mateyu 20:28.

Choncho onse amene amakhulupirira Yesu angalandire “mawomboledwe [ku uchimo] mwa mwazi wake” ndipo angathe kukhala ndi moyo wosatha. (Aefeso 1:7; Yohane 3:36) Ndithudi tiyenera kusangalala kuti Yehova Mulungu anakonda anthu kwambiri moti anapereka Mwana wake ngati Mpulumutsi wathu. (Luka 2:10-12; Yohane 3:16) Kuganizira bwino zomwe Yesu anachita pothandiza anthu ovutika m’zaka 100 zoyambirira kumatisonyeza zomwe zidzachitike m’tsogolo. Ndipo zimene Yesu anachita zinali zochititsadi chidwi.

Zomwe Zidzachitike M’dziko Latsopano

Yesu anatha kuchiritsa munthu wodwala aliyense amene anamubweretsa kwa iye. Palibe amene analephera kumuchiritsa, kaya matenda ake anali otani. Kuwonjezera apo, anadyetsa mozizwitsa anthu ambirimbiri ndi nsomba zochepa ndi mikate yochepa yokha, ndipo anachita zimenezi nthawi zingapo.—Mateyu 14:14-22; 15:30-38.

Yesu atathandiza munthu amene anabadwa wakhungu kuyambiranso kuona, anthu oyandikana nawo nyumba ndi anzake a munthuyo anavomereza kuti chimenechi chinalidi chozizwitsa, koma atsogoleri achipembedzo achiyuda sanakhulupirire zimenezo. Choncho munthu amene anayambiranso kuona uja anawauza mfundo yakuti: “Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire. Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.”—Yohane 9:32, 33.

Panthawi ya utumiki wa Yesu, msuwani wake Yohane Mbatizi, amene anali m’ndende, anatumiza amithenga kuti akaone ngati zimene anali kumva za Yesu zinali zoona. Baibulo limati: “Nthawi yomweyo [Yesu] anachiritsa anthu ambiri nthenda zawo, ndi zovuta, ndi mizimu yoipa; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.” Kenaka Yesu anauza amithengawo kuti: “Muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa.”—Luka 7:18-22.

Taganizirani mfundo iyi: Ngati chinthu chabwino chinachitika kale, kodi zimenezo sizingakutsimikizireni kuti chikhoza kuchitikanso? Pochita zozizwitsa, Yesu anasonyeza pang’ono pokha zomwe adzachite padziko lonse mu ulamuliro wake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Zozizwitsa zomwe anachita ndi umboni wakuti anatumidwa ndi Mulungu ndiponso kuti ndi Mwanadi wa Mulungu.

Panthawi ya ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, maulosi osangalatsa adzakwaniritsidwadi. Monga momwe maulosi ananeneratu, maso a akhungu adzatsegulidwa, makutu a ogontha adzatseguka, olumala adzatumpha ngati nswala, ndipo sipadzakhala wodwala. Padzakhalanso mtendere ndi kutetezeka padziko lonse lapansi. Ngakhale zinyama zimene panopa zimawopsa zidzakhala pamtendere ndi anthu.—Yesaya 9:6, 7; 11:6-9; 33:24; 35:5, 6; 65:17-25.

Kodi mungakonde kukhala ndi moyo kosatha mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, pamene zinthu zidzakhale zosangalatsa choncho? Yesu anafotokoza zomwe muyenera kuchita pamene anapemphera kwa atate ake kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kupitiriza kuphunzira zinthu zimenezi, zomwe zingakupatseni moyo.

[Chithunzi patsamba 23]

Izi n’zimene Mulungu walonjeza kuti zidzachitika padziko lapansi