Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzitetezeni Kuti Musafe ndi Utsi

Dzitetezeni Kuti Musafe ndi Utsi

Dzitetezeni Kuti Musafe ndi Utsi

ANTHU akupululuka mosaneneka. Tsiku lililonse, pa mphindi imodzi yokha anthu atatu amafa m’nyumba zawo. Kodi amafa ndi chiyani? Amafa ndi utsi wa nkhuni.

Kodi ndi zinthu zotani zimene anthu amagwiritsa ntchito ngati nkhuni? Zikhoza kukhala ndowe zouma, mitengo youma, matsatsa, udzu, kapena mapesi. Nyuzipepala inayake ya ku Nepal yotchedwa The Kathmandu Post inati munthu mmodzi pa anthu atatu alionse padziko lonse lapansi, kapena kuti anthu opitirira mabiliyoni awiri, amaphikira nkhuni. Nthawi zambiri anthu osauka sangachitire mwina koma kuphikira nkhuni basi.

Koma kuipa kwake n’koti nkhuni zikamayaka zimatulutsa mpweya wakupha. Choncho kodi anthu angadziteteze bwanji? Bungwe linalake lomwe likuthandiza anthu m’mayiko ambiri kuti atukule miyoyo yawo lotchedwa Intermediate Technology Development Group (ITDG), linati: “Kupewa mpweya wakupha m’nyumba n’kosavuta. Pamangofunika kuonetsetsa kuti utsi usalowe m’nyumba, apo ayi, kuonetsetsa kuti utsi uzituluka m’nyumbamo.”

Njira yoyamba yothandiza ndiyo kuphikira panja. Koma bwanji ngati zimenezi sizingatheke kapena si zabwino? Bungwe la ITDG linati muzionetsetsa kuti nyumba yanu ili ndi motulukira utsi mokwanira. Pali njira ziwiri zochitira zimenezi. Njira imodzi ndiyo kuboola mabowo kufupi ndi kudenga (neti yamawaya ingathandize kuti tizinyama ting’onoting’ono tisamalowe m’nyumbamo). Njira ina ndiyo kukhala ndi mawindo (kuika chophimba pawindopo kungathandize kuti anthu asamaone m’kati). Zimenezi zimathandiza kuti mpweya uzizungulira ndipo utsi uzituluka. Koma ngati mwayatsa nkhunizo kuti m’nyumba muzitentha, kubowola zibowo m’makoma n’kosathandiza kwenikweni, choncho pali njira ina yosavuta yomwe ingakuthandizeni.

Bungwe la ITDG linati kukhala ndi chotulutsira utsi ndi imodzi mwa njira zosavuta ndiponso zothandiza kwambiri zotulutsira utsi m’nyumba. Ndi ndalama zochepa, mukhoza kupanga zotulutsira utsi zamalata kapena ngakhale za zidina. Moto amauyatsa pansi pa zotulutsira utsi zimenezi ndipo zimakhala ndi chumuni chofika kudenga kwa nyumba chotulutsira utsi. Akatswiri amati mukabowola zibowo kufupi ndi denga n’kukhalanso ndi zotulutsira utsi, mumatulutsa pafupifupi utsi wonse wakupha m’nyumba. Anthu amene ali ndi zotulutsira utsi amanena kuti tsopano ali ndi thanzi labwino, ndi aukhondo, akhoza kugwira ntchito zambiri, ndipo amakonda kukhala m’nyumba zawo. Umenewu ndi umboni wakuti zinthu zosavuta kupanga zikhoza kusintha moyo kuti ukhale wabwinopo.

[Chithunzi patsamba 14]

Khitchini la m’nyumba ku Kenya lokhala ndi chotulutsira utsi, mpata waukulu bwino pakati pa khoma ndi denga, ndiponso mawindo

[Mawu a Chithunzi]

Dr. Nigel Bruce/www.itgd.org