Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzuwa Lingawale Bwanji Pakati pa Usiku?

Kodi Dzuwa Lingawale Bwanji Pakati pa Usiku?

Kodi Dzuwa Lingawale Bwanji Pakati pa Usiku?

“KODI zingatheke bwanji kuti dzuwa lisalowe?” Pokhala mmishonale wochokera ku Finland amene ndinali kutumikira m’dziko la Papua New Guinea, nthawi zambiri ndinkamva mafunso ngati amenewa. M’madera otentha, maola amene dzuwa limawala sasiyana kwenikweni mwezi uliwonse. Choncho zoti ku dera lakumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi dzuwa sililowa kwa miyezi ingapo, n’zovuta kumvetsa kwa anthu okhala m’madera otentha. Ndipo pamene ndinayesera kufotokoza kuti m’nyengo ya chisanu dzuwa silituluka n’komwe, anthu ambiri anangopitirira kudabwa.

Choncho, kodi zimatheka bwanji kuti dzuwa liziwala pakati pa usiku? Zodabwitsa zimenezi zimatheka chifukwa chakuti dziko lapansi likamayenda mozungulira dzuwa, ulendo umene umatenga chaka chathunthu, limakhala lopendekeka pang’ono nthawi zonse. Motero, ku Chigawo Chakumpoto cha dziko lapansi, m’chilimwe dera lakumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi limapendekekera kufupi ndi dzuwa, pamene m’nyengo ya chisanu limapendekekera kutali ndi dzuwa. Popeza dziko lapansi limatenga tsiku limodzi kuti lizungulire palokha, kudera la kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi usiku umodzi pachaka, cha m’ma June 21, dzuwa sililowa. Mofanana ndi zimenezi, tsiku limodzi pachaka, cha m’ma December 21, dzuwa silituluka, ngakhale kuti nthawi imene dzuwa limayenera kukhala pa liwombo kunja kukhoza kuwalako pang’ono ngati mmene kumawalira kukatsala pang’ono kukwana mbandakucha.

Ndipo mukamayandikira kwambiri pakati penipeni pa dera la kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi, kumakhala mausiku ambiri a m’chilimwe amene dzuwa sililowa, ndi masiku ambiri a m’nyengo ya chisanu amene dzuwa silituluka. Pakati penipeni pa dera la kumpoto ndiponso dera la kummwera kwenikweni kwa dziko lapansi, dzuwa sililowa kwa miyezi sikisi ndipo silituluka kwa miyezi sikisi. *

Kodi anthu okhala m’madera a kummwera kapena kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi amagona bwanji m’chilimwe pamene dzuwa sililowa, ndipo amatani m’nyengo ya chisanu pamene dzuwa siliwala? Kale, pakati pa mitundu ina ya anthu, ena ankagona nthawi yowirikiza kawiri m’nyengo ya chisanu kuposa nthawi imene amagona m’chilimwe. Koma moyo wamakono wachititsa kuti anthu ambiri asamagone maola osiyana kwambiri chonchi. Komabe, nthawi imene dzuwa limawala mpaka usiku imachititsabe anthu okhala ku dera la kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi kukhala ndi mphamvu zowonjezereka. Patrick, amene amakhala ku Alaska, anati: “Kunja kukakhala kuti dzuwa likuwalabe nthawi ya 11 koloko usiku, sindifuna kugona. Nthawi zina ndimapita panja n’kumakatchetcha kapinga kapena ndimagwira ntchito zina.”

Komabe, kukhala masiku ambirimbiri kunja kuli dzuwa kapena kuli mdima kukhoza kufooketsa thupi kapena kutopetsa maganizo. Choncho, m’chilimwe anthu ena amayesera kutchinga zipinda zawo zogona kuti mukhale mdima, ndipo m’nyengo ya chisanu amakhala pa malo pamene pali magetsi owala kwambiri, pofuna kuthandiza matupi awo kuti azitha kugona bwinobwino ndiponso kuti asamatope kapena asamangokhala ndwii chifukwa cha mdima. Ngakhale kuti pali mavuto ngati amenewa, anthu okhala ku madera amenewa komanso alendo amavomereza kuti kuona dzuwa likuwala pakati pa usiku n’chinthu chosaiwalika.—Munthu wina anatitumizira nkhaniyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Ku dera la kummwera kwenikweni kwa dziko lapansi kumachitikanso zomwezi, koma nthawi yake imasemphana. Kumpoto kukakhala kuti ndi nyengo ya yachisanu, kummwera kumakhala chilimwe.

[Chithunzi patsamba 31]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kupendekeka kwa dziko lapansi kumachititsa kuti ku madera a kumpoto kapena kummwera kwenikweni kwa dziko lapansi dzuwa lisamalowe m’chilimwe ndipo lisamatuluke m’nyengo ya chisanu (Chitsanzo chimene chasonyezedwa pano n’cha ku Chigawo Chakumpoto cha dziko lapansi)

Phukuto ←

● ● ● ● ●

Chisanu ● ◯ ● Chilimwe

● ● ● ● ● Dziko limazungulira

palokha kamodzi

→ Masika patsiku

[Chithunzi patsamba 31]

Chithunzi chosonyeza zithunzi zojambulidwa nthawi zosiyanasiyana ataziika pamodzi. Zithunzizi zikusonyeza dzuwa likuwala pakati pa usiku

[Mawu a Chithunzi]

© Paul Souders/WorldFoto