Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kufuna Kutchuka N’kulakwa?

Kodi Kufuna Kutchuka N’kulakwa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kufuna Kutchuka N’kulakwa?

“KODI n’kulakwa kufuna kutchuka, kulemera, ndi mphamvu?” Funso limeneli linalembedwa mu lipoti la bungwe linalake lachipembedzo pa mutu wakuti: “N’zovuta Kudziwa Khalidwe Loyenera ndi Losayenera.” Nkhaniyo inathirirapo ndemanga pa mawu amene Mulungu anauza Abrahamu akuti: “Ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako.”—Genesis 12:2.

Ngakhale kuti nkhaniyo inafotokoza kuti “sitiyenera kupweteketsa ena chifukwa chofuna kutchuka,” inanenapo mawu a rabi wotchuka wa m’zaka 100 zoyambirira akuti: “Fumbi ndiwe mwini” ndipo inamaliza n’kunena kuti: “Ngati ifeyo patokha sitiyesetsa kukwanitsa zinthu zomwe tingathe, palibe amene angatichitire zimenezo.” Kodi nkhani yofuna kutchuka ndi vutonso kwa anthu amene amafuna kutumikira Mulungu? Kodi tingatani kuti tikwanitse kuchita zinthu zonse zomwe tingathe pa moyo wathu? Kodi kufuna kutchuka n’kulakwa? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

Kodi Abrahamu Ankafuna Kutchuka?

Baibulo limatchula Abrahamu ngati munthu mmodzi amene anali ndi chikhulupiriro cholimba zedi. (Ahebri 11:8, 17) Pamene Mulungu analonjeza Abrahamu kuti adzamusandutsa mtundu waukulu ndi kutchukitsa dzina lake sankamulimbikitsa kukhala ndi mtima wofuna kutchuka. Mulungu ankafotokoza cholinga chake choti adzadalitsa anthu onse kudzera mwa Abrahamu, ndipo cholinga chimenechi chinali chofunika kwambiri kuposa zolakalaka za munthu aliyense.—Agalatiya 3:14.

Chifukwa cha kudzipereka kwake kwa Mulungu, Abrahamu anasiya moyo umene uyenera kuti unali wabwino ndiponso wapamwamba ku Uri. (Genesis 11:31) Kenaka, chifukwa chokonda mtendere, Abrahamu mwakufuna kwake sanaumirire mphamvu ndi udindo koma anapatsa Loti, mwana wa mchimwene wake, mbali yabwino kwambiri ya dzikolo kuti azikhalamo. (Genesis 13:8, 9) Baibulo silisonyeza paliponse kuti Abrahamu anali munthu wofuna kutchuka. M’malo mwake, chikhulupiriro, kumvera, ndi kudzichepetsa kwake n’zimene zinachititsa Mulungu kuti azimukonda ngati “bwenzi” lake lenileni.—Yesaya 41:8.

Kuona Udindo, Kudziwika, ndi Mphamvu M’njira Ina

Tanthauzo la kufuna kutchuka ndilo “chilakolako chachikulu chofuna udindo, kudziwika, kapena mphamvu.” Kale, Mfumu Solomo inali ndi udindo, inali yodziwika, yamphamvu, ndiponso yolemera kwambiri. (Mlaliki 2:3-9) Koma n’zochititsa chidwi kuti Solomo sikuti anali ndi chilakolako chachikulu chofuna kukhala ndi zinthu zimenezi. Solomo atakhala mfumu, Mulungu anamuuza kuti apemphe chilichonse chomwe akufuna. Solomo modzichepetsa anapempha mtima womvera ndiponso nzeru zoti athe kulamulira anthu osankhidwa a Mulungu. (1 Mafumu 3:5-9) Kenaka, atafotokoza kuchuluka kwa chuma ndi mphamvu zomwe anali nazo, Solomo anati “zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 2:11.

Kodi Solomo ananenapo chilichonse pa nkhani ya kukwanitsa zonse zomwe munthu ungathe? Inde anatero, ngakhale kuti sananene zimenezi mwachindunji. Atafotokoza zinthu zonse zomwe anakumana nazo pamoyo wake, pomaliza anati: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13) Anthu amakwanitsa zonse zomwe angathe, osati pokhala ndi udindo, chuma, kudziwika, kapena mphamvu, koma pokwanitsa kuchita chifuniro cha Mulungu.

Kudzichepetsa Kumakweza Munthu

N’zoona kuti sikulakwa kudzikonda wekha munthu. Baibulo limatiuza kuti tizikonda anzathu monga momwe timadzikondera tokha. (Mateyu 22:39) Anthu mwachibadwa amafuna kukhala ndi moyo wabwino ndiponso wosangalala. Koma Malemba amatilimbikitsanso kugwira ntchito mwakhama, kudzichepetsa, ndi kudziwa zinthu zomwe sitingathe kukwanitsa. (Miyambo 15:33; Mlaliki 3:13; Mika 6:8) Anthu oona mtima ndi odalirika ndiponso amene amagwira ntchito mwakhama nthawi zambiri amaonedwa, amapeza ntchito zabwino, ndipo amalemekezedwa. Ndithudi kuchita zinthu mwanjira imeneyi n’kwabwino kusiyana ndi kupondereza anthu ena kuti zathu zitiyendere kapena kupikisana ndi anthu ena kuti tipeze maudindo.

Yesu anachenjeza omvera ake kuti asamasankhe malo abwino kwambiri akapita ku phwando la ukwati. Iye anawalangiza kuti azipita pamalo otsika kwambiri ndiyeno zizikhala kwa mwini phwandolo kuwaika pamalo ena abwino. Pofotokoza momveka bwino mfundo imeneyi, Yesu anati: “Munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”—Luka 14:7-11.

Akristu Oona Amapewa Mtima Wofuna Kutchuka

Baibulo limasonyeza kuti anthu amafuna kutchuka ndipo amadzikuza chifukwa cha kupanda ungwiro. (Yakobo 4:5, 6) Mtumwi Yohane panthawi inayake anali ndi mtima wofuna kutchuka. Iye ankafunitsitsa kwambiri udindo, moti ali limodzi ndi mchimwene wake, analimba mtima kumupempha Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu. (Marko 10:37) Koma m’tsogolo mwake Yohane anadzasintha mtima wake. Ndipo mu kalata yake yachitatu, iye anadzudzula kwambiri Diotrefe, yemwe anati anali “wofuna kukhala wamkulu wa iwo.” (3 Yohane 9, 10) Akristu masiku ano amamvera mawu a Yesu ndipo amadzichepetsa, ndiponso amatsatira chitsanzo cha mtumwi wokalamba, Yohane, amene anaphunzira kupewa mtima wofuna kutchuka.

Koma tiyenera kuzindikira kuti munthu akhoza kukhala waluso, wogwira bwino ntchito, ndiponso wakhama, koma zimenezi sizitanthauza kuti anthu ena angayamikire zimene munthuyo amachita. Nthawi zina anthu ena angamuyamikire, koma nthawi zina mwina sangatero. (Miyambo 22:29; Mlaliki 10:7) Nthawi zina anthu osadziwa zinthu ndiwo angapatsidwe udindo winawake, pamene anthu odziwa bwino zinthuzo sapatsidwa udindowo. M’dziko lopanda ungwiroli, si anthu onse amene amapeza maudindo ndiponso mphamvu amene amakhaladi oyenerera zimenezi.

Akristu oona amadziwa zoyenera kuchita pa nkhani yofuna kutchuka. Chifukwa chophunzira Baibulo, chikumbumtima chawo chimawathandiza kupewa mtima wofuna kutchuka. Iwo amangoyesetsa kuchita zonse zomwe angathe nthawi zonse, kuti Mulungu alemekezeke, ndipo akatero zonse amazisiya m’manja mwake. (1 Akorinto 10:31) Akristu amayesetsa kukwanitsa zonse zomwe angathe pochita zinthu moopa Mulungu ndiponso posunga malamulo ake.

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Kodi Mulungu analimbikitsa Abrahamu kukhala ndi mtima wofuna kutchuka?