Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kupeza Chibwenzi pa Intaneti Kungakhaledi Koopsa?

Kodi Kupeza Chibwenzi pa Intaneti Kungakhaledi Koopsa?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kupeza Chibwenzi pa Intaneti Kungakhaledi Koopsa?

“Pa Intaneti, sungadziwe kuti munthu amene ukulemberana naye makalatayo ndi ndani kwenikweni.”​—Anatero Dan, wa zaka 17. *

“Anthu amatha kunama pa Intaneti. N’zosavuta kunamizira kukhala ngati munthu winawake.”​—Anatero George, wa zaka 26.

ANTHU amene akupeza zibwenzi pa Intaneti akuchulukirachulukira padziko lonse. Monga momwe nkhani yomaliza ya nkhani zino inafotokozera, chikondi cha pa Intaneti chikhoza kukula mwamsanga, koma nthawi zambiri chimatha anthuwo akadziwana bwinobwino. * Komabe, pali china chodetsa nkhawa kwambiri kuposa kukhumudwitsidwa chabe. Kupeza chibwenzi mwanjira imeneyi kungakupezetseni mavuto aakulu, kuphatikizapo a m’maganizo, kapenanso auzimu.

Kodi zingatheke bwanji kuti kompyuta ya m’nyumba mwanu momwe, yomwe imaoneka yosaopsa ndiponso yoti singakubweretsereni vuto lililonse, ikulowetseni m’mavuto? Ena mwa mavuto ake akukhudzana ndi mfundo inayake yofunika kwambiri ya m’Baibulo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Timafuna kuchita zonse mwachilungamo.” (Ahebri 13:18, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Apa sitikutanthauza kuti n’chinyengo kugwiritsa ntchito Intaneti, kapenanso kuti munthu akayamba kugwiritsa ntchito Intaneti amasanduka wachinyengo. Koma, tiyenera kudziwa kuti anthu ena nthawi zambiri amachita zinthu mwachinyengo ndiponso kuti monga momwe ena afotokozera poyambirira pankhani ino, zikuoneka kuti kugwiritsa ntchito Intaneti kumachititsa kuti chinyengo china chikhale chosavuta kuchita ndiponso chikhale chovuta kuchitulukira. Ndipotu pankhani ya chibwenzi, pamatha kukhala mavuto aakulu pakachitika zachinyengo.

Mwachitsanzo, taonani mtundu wachinyengo womwe wafotokozedwa m’vesi ili la m’Baibulo: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu othyasika.” (Salmo 26:4) Kodi mawu akuti “anthu othyasika” akutanthauzanji? M’mabaibulo ena pa mawu amenewa pali mawu akuti “anthu achiphamaso.” Malingana ndi zimene buku lina limafotokoza, mawu amenewa angagwiritsidwe ntchito pofotokoza “anthu amene amabisira anzawo zolinga zawo, kapena amene amabisa khalidwe ndiponso maganizo awo enieni.” Kodi chinyengo chimenechi chimachitika motani pa Intaneti? Ndipo kodi zimenezi zingadzetse mavuto otani kwa amene akufuna munthu woti akhale naye pachibwenzi?

Afisi Ovala Zovala Zankhosa

Bambo wina, dzina lake Michael, anadabwa kumva pamaphunziro enaake omwe anachita kuti ana ambiri samvera malangizo a makolo awo oti asamaone malo ena a pa Intaneti omwe amakhala ndi zinthu zoopsa. Bamboyu anati: “Chomwe chinandidetsa nkhawa kwambiri chinali kumva kuti anthu ogona ana angathe kugwiritsa ntchito Intaneti pofuna kunyengerera ana kuti achite nawo zachiwerewere.” Achinyamata akamagwiritsa ntchito Intaneti pocheza ndi anthu osawadziwa, akhoza kudziika pangozi yaikulu kwambiri kuposa momwe angaganizire.

Zoonadi, pakhala pakumveka malipoti akuti anthu akuluakulu omwe cholinga chawo ndi kufuna kugona ana amanyengezera kuti ndi achinyamata pamene akufufuza pa Intaneti ana ang’onoang’ono oti awagone. Malinga ndi zimene anapeza pa kafukufuku wina, “mwana mmodzi pa ana asanu alionse amene amagwiritsa ntchito Intaneti anapemphedwapo ndi anthu ena kuti agone nawo.” Nyuzipepala ina inanenanso kuti mwana mmodzi pa ana 33 alionse a zaka zapakati pa 10 ndi 17 “anakhala akuvutitsidwa kwambiri” ndi anthu amene ankawatumizira mauthenga pakompyuta.

Achinyamata ena amadzidzimuka akazindikira kuti munthu amene anali kunyengezera kuti ndi wachinyamata, yemwe iwo anayamba naye chibwenzi kudzera pa Intaneti ndi mkaidi ndipo ndi wachikulire. Achinyamata ena mosadziwa ayamba chibwenzi ndi anthu omwe cholinga chawo ndi kungofuna kugona ana. Poyamba, anthu oipawa amayamba n’kunyengerera mwana amene akufuna kum’gonayo, ndipo amachita izi pom’tumizira mauthenga abwino pa Intaneti. Mauthengawo amachititsa mwanayo kuwakhulupirira anthu amenewa. Koma m’kupita kwanthawi, iwo amayamba kufuna kuonana naye mwanayo n’cholinga choti achite zolinga zawo zachiwerewerezo. N’zachisoni kuti izi zachititsa kuti achinyamata amenyedwe, agwiriridwe, ndipo mwinanso aphedwe kumene.

Kunena zoona, pa Intaneti anthu oipa amadzibisadi n’cholinga choti apeze anthu amene angawachite chipongwe. Mwina anthu oterewa akukukumbutsani fanizo la Yesu la aneneri onyenga omwe ‘amadza kwa munthu ndi zovala zankhosa,’ koma kwenikweni ali “afisi olusa.” (Mateyu 7:15) Zingakhale zovuta kwambiri kuzindikira chinyengo chimenechi mukamalemberana makalata pa Intaneti ndi munthu amene simukumudziwa. George, amene ananena mawu amene talemba koyambirira aja, anati: “Munthu ukamalankhula ndi wina pamaso ndi pamaso, ungazindikire zinthu zina poona nkhope yake ndiponso pomva momwe akulankhulira. Koma pa Intaneti n’zosatheka kutero, choncho n’zosavuta kukupusitsa.”

Ndithudi, langizo la m’Baibulo, lakuti, “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa” ndi lanzeru kwambiri. (Miyambo 22:3) Inde, sikuti munthu aliyense amene mungacheze naye pa Intaneti ndi wofuna kugona ana. Komabe, pali njira zinanso zimene anthu amadzibisira.

Kuopsa kwa Chinyengo ndi Kuchita Zinthu Mwakabisira

N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amene akufuna chibwenzi pa Intaneti amakonda kunamizira kapena kukokomeza kuti iwo ndi anthu amakhalidwe abwino ndipo amachepetsa kapena kubisa mavuto awo akuluakulu. Kuwonjezera apa, nyuzipepala ya The Washington Post inanena mawu a wolemba mabuku wina, yemwe anati: “Kupeza chibwenzi pa Intaneti kungakhale koopsa chifukwa chakuti anthu amapusitsidwa.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Nthawi zambiri munthu amatha kunamizira kuti ndi wamwamuna kapena wamkazi. . . . Kawirikawiri pamatenga nthawi yaitali kuti aulule za ndalama zimene amapeza, . . . mafuko awo, milandu imene anapalamulapo kuboma, za matenda alionse okhudza ubongo amene angakhale nawo ndiponso ngati anakwatirapo kapena ayi.” Pofuna kuchenjeza ena, anthu ambiri akhala akufotokoza za mavuto amene akumanapo nawo chifukwa chopusitsidwa ndi zibwenzi za pa Intaneti.

Kodi anthu angathe kunama pa zinthu zofunika kwambiri monga pankhani ya moyo wawo wauzimu? N’zomvetsa chisoni kuti ena amatero. Amatha kunama kuti iwo ndi Akristu oona. Kodi n’chifukwa chiyani amanama choncho? Apanso, chimodzi mwa zifukwa zake n’chakuti pa Intaneti kumakhala kosavuta kuchita zimenezi. Mnyamata wina wa ku Ireland, dzina lake Sean, anavomereza kuti: “Munthu ukamalemba zinthu pakompyuta, n’zosavuta kuti uname.”

Anthu ambiri saona ngati chinyengo chimenechi ndi nkhani yaikulu, ndipo amangoti munthu ukapeza kumene chibwenzi sizachilendo kunamako pang’ono. Komabe, kumbukirani kuti Mulungu amadana ndi kunama. (Miyambo 6:16-19) Ndipo pali chifukwa chomveka chomwe amachitira zimenezi. Mavuto ambiri amene anthu akusautsika nawo m’dzikoli anayamba chifukwa cha bodza. (Yohane 8:44) Chinyengo ndi maziko oipa kwambiri a mgwirizano uliwonse, makamaka mgwirizano womwe cholinga chake ndi choti mudzakhale limodzi moyo wanu wonse. Choopsa kwambiri n’chakuti chinyengo chimatha kudzetsa mavuto mwauzimu chifukwa chimawononga ubwenzi wa munthu wonamayo ndi Yehova Mulungu.

N’zachisoni kuti achinyamata ena atengeka ndi chinyengo chamtundu winanso. Apeza zibwenzi pa Intaneti ndi kumabisira makolo awo za chibwenzicho. Mwachitsanzo, makolo a mnyamata wina anadzidzimuka tsiku lina pakhomo pawo patafika mwadzidzidzi mtsikana wina amene si wachipembedzo chawo ndipo anali atayenda ulendo wa makilomita oposa 1,500. Mwana wawo anali atakhala pachibwenzi cha pa Intaneti ndi mtsikanayo kwa miyezi sikisi, koma iwo sanadziwepo chilichonse mpaka panthawi imeneyo.

Makolowo anafunsa kuti, “Zatheka bwanji zimenezi?” Mumtima ankati, ‘Mwana wathu sangachite chibwenzi ndi munthu amene sanakumanepo naye.’ Koma mfundo ndi yakuti, mwana wawoyo anali kuwanyenga, tingati ankawabisira khalidwe lake lenileni. Kodi simukuvomereza kuti chinyengo chimenechi ndi maziko olakwika a chibwenzi?

Munthu Womuona Ali Bwino Kusiyana ndi Wongom’dziwira pa Intaneti

Pali mavuto enanso amene angabwere chifukwa chopeza chibwenzi pa Intaneti. Nthawi zina, zimatheka kuyamba kuganiza kuti mnzanu wa pa Intaneti ndiye wofunika kwambiri kuposa anthu amene mumaonana nawo tsiku ndi tsiku. Banja lanu, anzanu, ndiponso maudindo anu amabwera pambuyo. Mtsikana wina wa ku Austria, dzina lake Monika, anati: “Ndinayamba kunyalanyaza anzanga ofunika kwambiri chifukwa choti ndinkatha nthawi yambiri ndikucheza ndi anthu ena pa Intaneti.” Mtsikanayu anavutika maganizo kwambiri atazindikira zimenezi, motero anaganiza zosiya kugwiritsa ntchito Intaneti mwanjira imeneyi.

Ndi zoona kuti anthu ambiri amatha kugwiritsa ntchito Intaneti bwinobwino. Kulemberana makalata kudzera pa kompyuta kungakhale njira yabwino kwambiri yolankhulirana ndi anzanu ndiponso anthu amene mumawakonda. Komabe, mungavomereze kuti palibe chimene chingalowe m’malo mwa kuonana pamaso m’pamaso. Ngati ‘mwapitirira pa unamwali,’ nthawi imene chilakolako chogonana chimakhala champhamvu kwambiri, ndipo mukufuna kulowa m’banja, muyenera kuchita zinthu mwanzeru, chifukwa imeneyi ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu pamoyo wa munthu. (1 Akorinto 7:36) Musachite zimenezi mwachibwana.

Baibulo limalangiza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) M’malo mokhulupirira chilichonse chimene munthu wina, amene simunakumanepo naye, wakulemberani, ganizirani mofatsa zoti muchite. N’chinthu chanzeru kwambiri kukonza zoti mukumane naye munthuyo musanayambe kugwirizana naye. Onani ngati ndinu woyenereranadi, makamaka pankhani ya zolinga ndi zokonda zanu zauzimu. Chibwenzi chotero chingakuthandizeni kuti mudzakhale ndi banja losangalaladi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ‘Kodi Ndipeze Chibwenzi pa Intaneti?’” m’magazini ya Galamukani! ya May 8, 2005.

[Zithunzi patsamba 28]

Kodi mukum’dziwadi munthu amene akulemba mauthenga pa Intaneti?

[Chithunzi patsamba 30]

Pankhani ya chibwenzi, palibe chomwe chingalowe m’malo mwa kuonana maso ndi maso