Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwakonzeka Kukapezekako?

Kodi Mwakonzeka Kukapezekako?

Kodi Mwakonzeka Kukapezekako?

▪Kukapezeka kuti? Ku Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa mutu wakuti “Kumvera Mulungu.” Misonkhano yachigawo imeneyi, yomwe inayamba ku United States mlungu womaliza wa mu May, m’miyezi ikubwerayi ichitika m’malo ambirimbiri padziko lonse lapansi. Mosakayikira ku malo akufupi ndi kwanu kudzachitikanso msonkhano woterewu.

M’malo ambiri misonkhanoyi idzayamba ndi nyimbo nthawi ya 9:30 m’mawa. Mutu wa Lachisanu ndi wakuti “Mverani Mawu Anga, Ndipo Ndidzakhala Mulungu Wanu.” (Yeremiya 7:23) Nkhani za m’mawa, zomwe zili ndi mitu yakuti “Tinapangidwa Modabwitsa” ndi “Chifukwa Chake Muyenera Kukhulupirira Kuti Chiyembekezo Chakuti Akufa Adzauka Ndi Chenicheni,” zikadzatha, nkhani yaikulu yakuti “Tsatirani Chitsanzo Chathu, Kristu, mwa Kumvera Mulungu,” idzamalizitsa chigawo cham’mawa.

Chigawo chamasana Lachisanu chili ndi nkhani zakuti “Pitirizani ‘Kusamalira Mzimu’ Kuti Mukhale ndi Moyo,” “Mudzisungire Kupewa Msiriro Uliwonse,” ndi “Musatsate ‘Miyambi Yachabe.’” Kenaka nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali ziwiri idzafotokoza mfundo zazikulu za m’mabuku a m’Baibulo a Hagai ndi Zekariya. Nkhani za tsiku limeneli zidzatha ndi nkhani yakuti “Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa.”

Mutu wa Loweruka ndi wakuti ‘Kumvera ndi Mtima’ “M’zonse,” kuchokera pa lemba la Aroma 6:17 ndi 2 Akorinto 2:9. Chigawo cham’mawa chili ndi nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali zitatu ya mutu wakuti “Mabanja Otsatira Mfundo za m’Baibulo Amakhala Mosangalala.” Nkhaniyi ili ndi zitsanzo ndi mbali yofunsa mafunso ndipo ikusonyeza momwe mwamuna, mkazi, ndi ana m’banja angathandizire kuti banjalo likhale losangalala. Chigawo cham’mawa chidzatha ndi nkhani yakuti “Inde Wanu Akhaledi Inde,” ndipo pambuyo pake anthu oyenerera adzabatizidwa.

Loweruka masana kudzakhala nkhani zina monga yakuti “Musapenye Zachabe” ndi “Bwererani kwa Mbusa wa Moyo Wanu.” Kenaka padzabwera nkhani yosiyirana yakuti “Mverani Atsogoleri Anu” yomwe idzakhale ndi mbali ziwiri. Nkhani yomaliza yamasana, yakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?ndi yofunika kwambiri pamsonkhano umenewu.

Chigawo cham’mawa Lamlungu chidzakhala ndi mutu wakuti “Mverani Mawu Awa Onse . . . Kuti Chikukomereni,” kuchokera pa lemba la Deuteronomo 12:28. Nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali zitatu ya mutu wakuti “Thandizani Ena Kumvera Zimene Baibulo Limaphunzitsa” ili ndi mfundo zothandiza poyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo oyenda bwino.

Chigawo cham’mawa chidzatha ndi sewero lokhala ndi zovala zapadera lakuti “Yesetsani Kukwaniritsa Zolinga Zimene Zimalemekeza Mulungu.” Seweroli lisanayambe padzakhala nkhani yakuti “Achinyamata—Kodi Zolinga Zanu Zingakuthandizeni Kudzakhala ndi Moyo Wabwino?” Nkhani imeneyi idzakhala kalambulabwalo wa sewerolo, lomwe n’lonena za Timoteo, yemwe ali mnyamata anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri potumikira ena modzipereka. Achinyamata masiku ano akulimbikitsidwa kutsatira chitsanzo chimenecho. Chigawo chomaliza cha msonkhanowu Lamlungu masana chili ndi nkhani ya onse yakuti “Kodi Tiyenera Kumvera Ndani?”

Konzekerani panopa kukapezekako. Kuti mudziwe komwe kudzakhale msonkhano wapafupi kwambiri ndi kumene mumakhala, funsani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kapena lemberani amene amafalitsa magazini ino. Mu magazini yathu ina ya Nsanja ya Olonda ya March 1, muli mndandanda wa malo onse omwe kudzachitikire misonkhanoyi ku Malawi.