Kupirira ndi Khansa Yapakhungu
Kupirira ndi Khansa Yapakhungu
JEREMIAH ndi munthu wa zaka 51 wa ku Australia, amene makolo ake anachokera ku Ireland, ndipo ali ndi tsitsi lofiira ndi khungu loyera kwambiri, zomwe ena amaona ngati ndi temberero. Iye anafotokoza kuti: “Mofanana ndi anthu ambiri a ku Australia, banja lathu nthawi zambiri linkakhala panja kumapeto kwa mlungu ndiponso tikakhala pa tchuthi m’chilimwe. Ndili mwana, ndinkatha maola ambiri ndikusambira m’dziwe lomwe linali panyumba pathu kapena kusewera ndi mafunde m’nyanja, kapenanso kusewera mpira m’mphepete mwa nyanja mu mzinda wa Gold Coast, kummwera kwa mzinda wa Brisbane. Nthawi zambiri ndinkangovala kabudula yekha basi.”
Jeremiah akupitiriza kuti: “Pamene ndinali mnyamata, anali asanayambebe kupanga mafuta abwino oteteza khungu kuti lisapse ndi dzuwa. M’masiku amenewo anthu otsatsa malonda ankalimbikitsa anthu kudzola mafuta a kokonati othandiza khungu kuda likakhala padzuwa. Anthu ambiri ankafuna azioneka ngati mmene ankaonekera anthu a ku Australia ogwira ntchito yoteteza anthu kuti asamire m’nyanja posambira. Anthu ogwira ntchito imeneyi ankakhala ndi khungu lakuda chifukwa chopsa ndi dzuwa. Panthawi imeneyo sitinkadziwa bwinobwino kuti dzuwa lingawononge kwambiri khungu. Chomwe chinandichititsa kuti ndiyambe kupewa kukhala padzuwa kwambiri ndi ululu womwe ndinkamva nthawi ndi nthawi ndikapsa kwambiri ndi dzuwa.” Komatu apa n’kuti khungu la Jeremiah litawonongeka kale. Iye anati: “Chifukwa choti kwa zaka zambiri ndinkakhala padzuwa, msana ndi chifuwa changa zili pamtunda, ndinatuluka ziphuphu zambiri zomwe zinayamba kuda ndi kukhuthala, makamaka pachifuwa panga.”
Kuyambira nthawi imeneyo, Jeremiah amuchotsapo ziphuphu zitatu za khansa yapakhungu yoopsa kwambiri, ndi zina za khansa yapakhungu yamtundu wina. Chifukwa cha zimenezi, iye anasintha mmene amachitira zinthu. Iye anati: “Tsiku lililonse, ndisanatuluke panja ndimadzola mafuta
ofewetsa khungu. Kenaka ndimadzola mafuta oteteza khungu kuti lisapse ndi dzuwa. Masiku ano ndimavala chipewa masiku ambiri m’chilimwe kuyambira 9 koloko m’mawa mpaka 4 koloko madzulo.” Iye amapitanso kukayezedwa ndi dokotala wodziwa za matenda a pakhungu miyezi itatu iliyonse.Jeremiah anafotokoza zomwe zamuthandiza kupirira ndi matenda akewo. Iye anati: “Yehova Mulungu wandithandiza kukhulupirira ndi mtima wonse kuti ndikhoza kuchira ngakhale kuti anthu ena ankaganiza kuti ndikhoza kufa chaka china chilichonse. Chifukwa chakuti zaka pafupifupi 20 zapitazo anthu odwala khansa yapakhungu yoopsa kwambiri ankayembekezeka kukhala ndi moyo zaka zochepa chabe, ena amandiona ngati ndikuyenda wofaifa. Ndaona kuti mawu amene Mfumu Davide ananena ndi oona, akuti: ‘Yehova adzandigwiriziza pa kama wodwalira; podwala ine mukonza pogona panga.’”—Salmo 41:3.
Munthu wina amene wavutika ndi khansa yapakhungu ndi Maxine. Ali mtsikana, Maxine, yemwe ndi woyera kwambiri, anatumizidwa ku madera otentha kukakhala mmishonale. Poyamba anapita ku Dominican Republic ndipo kenaka anapita ku Puerto Rico. Kwa zaka 20, ankapita khomo ndi khomo mu utumiki kuli dzuwa lambiri pogwira ntchito yake yaumishonale. Kuwonjezera apo, ankakonda kuothera dzuwa panthawi yake yopuma. Kenaka mu 1971, anapeza kuti kumaso kwake kwatuluka chiphuphu chakhansa. Analandira chithandizo cha magetsi kenaka anachitidwa opaleshoni. Atatero, pamene panali khansapo anamatapo khungu lina. Komabe maselo ena a khungu lake anapitirizabe kugwidwa ndi khansa.
Maxine anafotokoza kuti: “Vuto linalipo linali loti nthawi zambiri maselo ogwidwa ndi khansa sankawaona, choncho ankapitirizabe kukula. Ndavutika kwa nthawi yaitali, pafupifupi zaka 30, ndipo zaka zonsezi ndimangokhalira kupita kwa madokotala ndiponso ku zipatala. Ndachitidwa maopaleshoni pafupifupi 10 kumaso kwanga, komanso ndapita kangapo kuchipatala kukafuna chithandizo chamtundu wina.” Maxine tsopano ali ndi zaka 80 ndipo opaleshoni imene wachitidwa posachedwapa ndi yodula maselo mosamala, ndipo yatha kuchotsa maselo ambiri akhansa.
Chifukwa cha khansa yake yapakhungu yomwe sitherapoyo, Maxine wasintha momwe amachitira utumiki wake waumishonale, ndipo tsopano amalalikira madzulo popewa dzuwa. Kodi n’chiyani chomwe chathandiza Maxine kupirira? “Chinthu chimodzi chomwe chandithandiza ndicho kuganizira zinthu zabwino. Ndikudziwa kuti khansa siitha, ndiponso kuti ndidzafunikabe kukaonana ndi adokotala. Zimenezo sindidandaula nazo. Ndimayesetsa kuti ndisamadzimvere chisoni ndiponso ndisamadandaule ndi mavuto anga. Ndimasangalalabe ndi utumiki wanga ngakhale kuti ndili ndi mavuto oterewa. Mpaka pano ndimathabe kulankhula ndi anthu ena za Ufumu wa Yehova. Ndipo ndili ndi chiyembekezo choti ndidzachiriratu posachedwapa m’dziko latsopano. Panthawi imeneyo ndidzakhala ndi nkhope yokongola ya mtsikana.”
Zoonadi, anthu odwala khansa yapakhungu ndi matenda ena angayembekezere tsiku limene mawu olembedwa m’buku la Yobu adzakwaniritsidwe. Mawuwo amati: “Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.” (Yobu 33:25) Podikira nthawi imeneyo, tiyeni tonsefe tizikumbukira kuti kukhala padzuwa nthawi yaitali n’koopsa, ndipo tiziyesetsa kwambiri kuteteza khungu lathu.
[Zithunzi patsamba 9]
Jeremiah wachotsedwapo ziphuphu zingapo zakhansa, kuphatikizapo ziphuphu zitatu za khansa yoopsa kwambiri yapakhungu. Komabe, iye sadandaula kwambiri ndipo akuyembekezera zabwino m’tsogolo
[Zithunzi patsamba 10]
“M’dziko latsopano . . . ndidzakhala ndi nkhope yokongola ya mtsikana.” —Maxine