“Muzinyadira Zimenezi”
“Muzinyadira Zimenezi”
ATUMIKI oona a Mulungu amazindikira kuti kuona mtima n’kofunika. Iwo amakhala oona mtima chifukwa chokonda Mlengi wawo. Mwachitsanzo, taganizirani zomwe zinachitikira Lázaro. Kale m’mbuyomu pamene ankagwira ntchito pa hotela inayake ku Huatulco, ku Mexico, anatola ndalama zokwana madola 70 zomwe munthu wina anataya pamalo ofikira alendo. Iye nthawi yomweyo anakapereka ndalamazo kwa abwana ake. Patapita nthawi anatolanso kachikwama kandalama m’bafa. Iye anapereka kachikwamako pamalo ofikira alendo, ndipo munthu amene anataya kachikwamako anasangalala kwambiri kuti kapezeka.
Bwana wamkulu pa hotelapo anamva za nkhani zimenezi, ndipo anafunsa Lázaro chomwe chinamuchititsa kuti abweze ndalama ndi kachikwama kaja. Lázaro anayankha kuti satenga chinthu chomwe sichake chifukwa amatsatira mfundo zomwe anaphunzira m’Baibulo. Bwana wamkuluyo anamulembera Lázaro kalata yomuthokoza ndipo anati: “Masiku ano n’zovuta kupeza anthu a khalidwe labwino. Tikuthokoza kwambiri mtima umene uli nawo. Wasonyeza kuti ndiwe munthu wakhalidwe labwino, woti antchito anzako ayenera kukutsanzira. Iweyo ndi anthu a m’banja mwako muzinyadira zimenezi.” Lázaro anam’patsa ulemu wapadera pomutchula kuti ndiye anali wantchito amene wachita bwino kwambiri mwezi umenewo.
Poyamba anzake ena a Lázaro a kuntchitoko ankaganiza kuti Lázaro analakwitsa pobweza zinthu zija. Koma ataona momwe abwana awo anamuyamikirira, nawonso anamuthokoza Lázaro chifukwa cha khalidwe lake labwino kwambiri.
Baibulo limalimbikitsa otsatira okhulupirika a Yesu kuti ‘azichitira anthu onse chokoma’ ndipo ‘azikhala ndi makhalidwe abwino.’ (Agalatiya 6:10; Ahebri 13:18) Mosakayikira, Akristu akakhala oona mtima, Yehova, Mulungu “wolungama ndi wolunjika” wotchulidwa m’Baibulo, amalemekezeka.—Deuteronomo 32:4.