Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Tonsefe Tingachite Kuti Pakhomo Pazikhala Paukhondo

Zomwe Tonsefe Tingachite Kuti Pakhomo Pazikhala Paukhondo

Zomwe Tonsefe Tingachite Kuti Pakhomo Pazikhala Paukhondo

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Mexico

MALO aukhondo, opanda zoipa zilizonse amasangalatsa kwambiri kukhalapo. Komabe, chifukwa cha kuchuluka kwa zinyalala m’mizinda, kukhala ndi panyumba ndiponso malo aukhondo komanso osamalidwa bwino kukuvuta kwambiri.

Boma limayesetsa kuyeretsa misewu polemba ntchito anthu kuti azichotsa zinyalala, komabe zinyalala zimaunjikana m’malo ena, n’kunyansitsa malowo ndiponso zimatha kuyambitsa matenda. Zinyalala zikaunjikana, makoswe, mphemvu, ndi tizilombo tina totere, zimachulukana. Kodi pali chilichonse chomwe mungachitepo? Inde chilipo. Muzionetsetsa kuti panyumba panu komanso malo ozungulira nyumba yanu azikhala aukhondo ndiponso osamalidwa bwino.

Ukhondo Umayambira M’maganizo

Anthu ena amaganiza kuti panyumba pa anthu osauka ndiponso madera ozungulira panyumbapo sangakhale aukhondo. Koma zimenezi si zoona. Inde, chifukwa chosowa ndalama mukhoza kumavutika kuti pakhomo panu pazikhala poyera. Koma mwambi wina wa Chisipanya umati, “umphawi ndi ukhondo sizikangana.” Komanso, ngati munthu ali ndi ndalama zokwanira sizitanthauza kuti pakhomo pake pazikhala paukhondo.

Kuti munthu akhale ndi pakhomo paukhondo amafunika kuti ukhondowo uziyambira m’maganizo ndipo kenaka uzionekera pa zochita zake. Ndipo kuti pakhomo pakhale paukhondo mbali yaikulu zimadalira maganizo a banja lonselo. Pachifukwa chimenechi ndi bwino kuti aliyense wa ife aone zomwe angachite kuti pakhomo pathu, kuphatikizapo kumadera kumene timakhala, kukhale kwaukhondo.

Ndondomeko Yokonzera Pakhomo

Zimaoneka ngati kuti ntchito ya mayi yokonza pakhomo siitherapo. Kuwonjezera pa kukonza chakudya ndi kuwakonzekeretsa ana kuti azipita kusukulu, mayi amafunikanso kugwira ntchito kuti m’nyumba ndi panja pakhale poyera. Mwina mukudziwa kuti nthawi zambiri mayi ndi amene amatola zovala zakuda kapena zinthu zina zomwe ana ake amasiya m’zipinda mwawo. Kukhala ndi ndondomeko yabwino yokonzera pakhomo, yoti aliyense m’banjamo azichita nawo ntchitoyi, kungawapeputsire ntchito amayi.

Amayi ena amaona kuti pali zinthu zina panyumba zimene zimafunika kuzikonza tsiku lililonse, pamene zina zimafunika kuzikonza mlungu uliwonse, ndiponso zina mwezi uliwonse. Ndipotu, pali zinthu zina zimene mungamazikonze kamodzi pachaka. Mwachitsanzo, pa nthambi za Mboni za Yehova m’dziko lililonse, kapena kuti pa Beteli, chaka chilichonse amayeretsa malo amene amaikamo zovala m’zipinda zogona. Imeneyi imakhala nthawi yochotsa zinthu zimene sagwiritsa ntchito ndi kukonza zinthu mwadongosolo m’malo oika zovalawo. Pamakhalanso ndondomeko yotsukira makoma nthawi ndi nthawi.

M’nyumba muli malo ena, monga kubafa ndi kuchimbudzi, amene amafunika kukhala aukhondo kwambiri kuti anthu akhale ndi thanzi labwino. Malo amenewa muziwatsuka tsiku lililonse ndipo pakatha mlungu uliwonse muziwatsuka mosamala kwambiri kuti tizilombo toyambitsa matenda tisachulukane. Anthu ena amaganiza kuti n’zosatheka kuti m’kati mwa chimbudzi cha m’nyumba mukhale mosathimbirira, ndiponso kuti n’zosatheka kuti muzikhala moyera bwino nthawi zonse. Izi si zoona chifukwa pali anthu ena amene m’nyumba zawo zimbudzi zimakhala zoyera kwambiri ndiponso zosathimbirira. Pamangofunika kutsukamo nthawi zonse ndi kugwiritsa ntchito mankhwala otsukira oyenera.

M’khitchini mumafunikanso kutsukamo mosamala. Ngakhale kuti mumatsuka mbale, sitovu, ndi pamalo pokhazika zinthu tsiku lililonse, mufunika kuyeretsamo mosamala kwambiri nthawi ndi nthawi, mwina kamodzi pamwezi, monga kutsuka kuseri kwa sitovu ndi firiji ndiponso pansi pa sinki. Kuyeretsa m’chipinda chosunga zinthu ndi m’makabati pafupipafupi kumathandiza kuti musakhale mphemvu ndi tizilombo tina.

Aliyense M’banjamo Azithandiza Nawo

Makolo ena amapatsa ana awo malamulo ndipo amawaphunzitsa kuti akamachoka m’chipinda chawo m’mawa popita kusukulu, azionetsetsa kuti ayala pabedi, aika zovala zakuda pamalo oyenera, ndipo katundu wawo yense amusiya mwadongosolo. Lamulo lofunika kuti aliyense azitsatira n’loti “Chilichonse chizikhala pamalo pake.”

Ndiponso anthu ena m’banjamo akhoza kukhala ndi ntchito yapadera yoti azigwira kapena mbali ya nyumbayo yoti aziyeretsa. Mwachitsanzo, kwa anthu amene ali ndi magalaja, kodi bambo ndi amene amaonetsetsa kuti zinthu zikhale mwadongosolo m’galajamo ndi kutsukamo bwinobwino mwina kamodzi pachaka? Kodi mwana wawo wina angawathandize kuchita zimenezi? Kodi ndani amalimirira ndiponso kutchetcha udzu kumaso kwa nyumba? Kodi zimenezi ziyenera kuchitika pafupipafupi bwanji kuti panja pa nyumba pazioneka polongosoka? Kodi m’nyumbamo muli chipinda chosungira katundu chofunika kumakonzamo nthawi ndi nthawi kuti musadzadze katundu wosafunikira ndiponso kuti mukhale mwaukhondo? Ngati ndi choncho, ndani azigwira ntchito imeneyi? Makolo ena amapatsa ana ntchito ngati zimenezi, ndipo anawo amazigwira mosinthanasinthana.

Choncho khalani ndi ndondomeko yabwino yokonzera pakhomo panu. Kaya mumakonza nokha panyumbapo kapena mumathandizana ndi anthu a m’banja lanu, kapena mumafunika wantchito kuti akuthandizeni, m’pofunika kukhala ndi ndondomeko yabwino. Mayi wina amene nyumba yake ili yaukhondo kwambiri ananena momwe banja lake lonse limathandizirana kuti nyumbayo ikhale yoyera. Iye anati: “Ine ndi ana anga aakazi atatu timagawana ntchito zapakhomo. Norma Adriana amakonza pabalaza, m’zipinda zogona ziwiri, pakhonde, ndi pamsewu wapanja. Ana Joaquina amakonza kukhitchini. Ine ndimachapa zovala ndi kugwira ntchito zina, pamene María del Carmen amatsuka mbale.”

Panja Pazioneka Bwino

Nanga bwanji panja? Kaya m’makhala m’chinyumba chachikulu chokongola kapena mumakhala m’nyumba yaing’ono, m’pofunika kukhala ndi ndondomeko yabwino yokonzera panja kuti pazioneka bwino. Mwachitsanzo, geti la mpanda wa nyumbayo likhoza kugwejemuka mbali imodzi. Monga mukudziwa, getilo silingaoneke bwino mukangolisiya osalikonza mpaka ligwe. Zimakhalanso chimodzimodzi mukangosiya zinyalala kuti ziunjikane polowera kunyumbako kapena panjira yapafupi ndi nyumbayo. Ndiponso nthawi zina anthu amasiya zitini, zida zogwirira ntchito, ndi zinthu zina kuti ziunjikane panja pa nyumba, ndipo pamenepa pakhoza kumabisala makoswe ndi tizilombo tina.

Mabanja ena anaganiza zoti tsiku lililonse kapena mlungu uliwonse, monga momwe pangafunikire, azisesa ndi kukonza panja pa nyumba yawo, kuphatikizapo kanjira kopita kunyumba kwawo ngakhale msewu womwe uli kumaso kwa nyumba yawo. N’zoona kuti m’madera ena aboma ali ndi anthu amene amakonza maderawo kuti azioneka bwino, koma m’madera ena mulibe ndondomeko ya boma yoteroyo. Mosakayikira, malo amene timakhala angaoneke bwino ndiponso angakhale aukhondo aliyense akamachitapo mbali yake.

Mabanja ena amakhala ndi ndondomeko yogwirira ntchito zomwe tazitchula pamwambazi, komanso amazilemba papepala n’kuziika poti aliyense m’banjamo angazione ndi kuzitsatira. Zimenezi zingathandize kwambiri. N’zoona kuti sitinafotokoze zinthu zonse zomwe muyenera kudziwa zokhudza kuyeretsa panyumba. Mwachitsanzo, muyenera kudziwa kuti kodi ndi mankhwala ati oyeretsera m’nyumba amene ali oyenererana kwambiri ndi dera lanulo, ndiponso zinthu zosiyanasiyana zokonzera m’nyumba zimene mungathe kugula malinga ndi ndalama zimene mumapeza.

Mosakayikira, malangizo achidulewa athandiza banja lanu lonse kudziwa kuti kusamalira nyumba yanu ndi dera lomwe mumakhala n’kofunika. Kumbukirani kuti kuyeretsa m’nyumba ndi panja kumadalira maganizo anu, osati ndalama zimene mumapeza.

[Bokosi pamasamba 16, 17]

Ndondomeko Yabwino Yokonzera Panyumba

Malo otsalawo lembanipo mfundo zanu zowonjezera pa ndondomekoyi

Zofunika kudziwa: Kusakaniza mankhwala a mitundu yosiyana otsukira zinthu n’koopsa kwambiri

Tsiku Lililonse

Kuchipinda: Yalani pabedi ndi kuika zinthu m’malo mwake

M’khitchini: Tsukani mbale ndi pasinki. Pamatebulo ndi pamalo pokhazikapo zinthu pasamakhale zinthu zambirimbiri. Sesani kapena kolopani pansi ngati pakufunika kutero

Kubafa ndi kuchimbudzi: Tsukani sinki ndi chimbudzi. Ikani zinthu m’malo mwake

Pabalaza ndi m’zipinda zina: Ikani zinthu m’malo mwake. Pukutani mipando patalipatali. Sesani kapena kolopani pansi ngati pakufunika kutero

Nyumba yonse: Tayani zinyalala kumalo koyenera

Mlungu Uliwonse

Kuchipinda: Chapani nsalu zofunda. Sesani kapena kolopani pansi ngati pakufunika kutero. Pukutani mipando

M’khitchini: Tsukani sitovu, ndi zida zina za kukhitchini zoyendera magetsi, ndiponso sinki ndi katundu wina wa kukhitchini. Kolopani pansi

Kubafa ndi kuchimbudzi: Tsukani makoma a m’bafa, bafa, ndi sinki. Tsukani chimbudzi, makabati, ndi malo ena ndi mankhwala opha majeremusi. Chapani matawelo opukutira. Sesani kapena kolopani pansi

Mwezi Uliwonse

Kubafa ndi kuchimbudzi: Tsukani bwinobwino makoma onse

Nyumba yonse: Tsukani maferemu a zitseko. Pukutani bwinobwino mipando

Panja ndi m’galaja: Sesani ndi kutsuka pamene pakufunika kutero. Muonetsetse kuti zinyalala ndi zinthu zina zosafunika zisamaunjikane

Miyezi Sikisi Iliyonse

Kuchipinda: Chapani zoyala pamwamba pabedi motsatira malangizo a kachapidwe kake

M’khitchini: Chotsani zinthu zonse m’firiji ndi kuitsuka bwinobwino

Kubafa ndi kuchimbudzi: Chotsani zinthu zonse m’mashelufu ndi m’madilowo. Tayani zinthu zosafunika kapena zotha mphamvu

Nyumba yonse: Tsukani nyali, mafani, ndi mababu amagetsi. Tsukani zitseko. Tsukani maneti a m’mawindo, mawindo, ndi maferemu a mawindo

Chaka Chilichonse

Kuchipinda: Chotsani zinthu zonse mu wodilopu n’kutsukamo bwinobwino. Tayani zinthu zosafunika. Chapani mabulangete. Kunthani kwambiri matiresi. Chapani mapilo motsatira malangizo a kachapidwe kake

M’khitchini: Chotsani zinthu zonse m’mashelufu, m’makabati, ndi m’madilowo n’kutsukamo bwinobwino. Tayani zinthu zosafunika. Sunthani katundu kuti mutsuke pamwamba kapena pansi pake

Nyumba yonse: Tsukani makoma onse. Chapani mipando ndi makatani motsatira malangizo a kachapidwe kake

Galaja ndi zipinda zosungako katundu: Sesani bwinobwino. Longedzani katundu bwino kapena tayani katundu wosafunika

[Zithunzi patsamba 18]

“Chilichonse chizikhala pamalo pake”

[Zithunzi patsamba 18]

Ndi bwino kupatsa ena zinthu zomwe simuzigwiritsanso ntchito