Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziwani Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Dziwani Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Dziwani Zimene Baibulo Limaphunzitsa

▪ Kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kali ndi masamba 32 ndipo saizi yake kali ngati magazini inoyo. Cholinga chake n’kuthandiza anthu kumvetsetsa mfundo zazikulu za m’Baibulo. Kabukuka kamafotokoza momveka bwino cholinga cha Mulungu kwa anthu ndiponso kamasonyeza kuchokera m’Baibulo zomwe tiyenera kuchita kuti tisangalatse Mulungu. Ina mwa mitu yake yochititsa chidwi ndi monga “Kodi Mulungu Ndani?,” “Kodi Yesu Kristu Ndani?,” “Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?,” ndi “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”

Tikukupemphani kuti muitanitse kabuku kanu kapena mukatenge pa Intaneti pa adiresi yathu yakuti www.pr418.com. Kabukuka kalipo m’zinenero zopitirira 250.

Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.