Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kuopa Armagedo?

Kodi Muyenera Kuopa Armagedo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Muyenera Kuopa Armagedo?

KODI “Armagedo” n’chiyani? Mwachidule, mawuwa amaimira zochitika panthawi imene olamulira a dziko akusonkhanitsidwa kuti atsutsane ndi Mulungu ndi Ufumu wake wolamulidwa ndi Yesu Kristu. M’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza olamulira atasonkhanitsidwa pamodzi akutsutsana ndi Mulungu pamalo ophiphiritsira otchedwa Armagedo.

Mawu oti “Armagedo” amapezeka kamodzi kokha m’Malemba, koma m’zinenero zina masiku ano amagwiritsidwa ntchito kwambiri pophiphiritsira zinthu zinazake. Mawuwa agwiritsidwa ntchito kuimira masoka aakulu ndi aang’ono omwe, monga kupululuka kwa mafuko ndi zida za nyukiliya, zinthu zowononga makompyuta, ndi zina zotero. Mabuku angapo otchuka alembedwa onena za nthawi imene amaitcha nthawi ya mapeto, kapena pamene Armagedo idzakhala itangotsala pang’ono kuyambika. Mabuku enaake onena za nkhani imeneyi agulitsidwapo okwana 60 miliyoni pa zaka teni zapitazi.

Anthu ena amaopa Armagedo. Amaganiza kuti zigawenga, nkhondo zapakati pa mayiko, kapena masoka omwe anthu sangathe kuwaletsa zidzabweretsa chisokonezo chachikulu, moti dziko lapansi lidzafika poti anthu sangathenso kukhalapo. Ena amakhulupirira kuti pa nthawi inayake yoikika, Mulungu mokwiya adzawononga dziko lathuli ndi zonse zomwe zilimo. Zimenezo n’zochititsadi mantha kuziganizira! Koma kodi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” ya Armagedo ndi chiyani kwenikweni?—Chivumbulutso 16:14, 16.

Kodi Dziko Lapansili Lidzawonongedwa?

Pa Armagedo sikuti anthu onse adzafa. Tikudziwa bwanji zimenezi? Baibulo limatitsimikizira kuti: “Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” (2 Petro 2:9) Choncho tingakhulupirire kuti Mulungu adzadziletsa pogwiritsa ntchito mphamvu yake yaikulu. Anthu amene adzalangidwe pa Armagedo ndi okhawo amene sagonjera ulamuliro wa Mulungu. Sipadzakhala anthu ophedwa mwangozi.—Salmo 2:2, 9; Genesis 18:23, 25.

Baibulo limatiuza kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Choncho n’zachionekere kuti cholinga cha Yehova Mulungu si kuwononga dziko lathuli. M’malo mwake, adzachotsa anthu oipa amene amatsutsana ndi ulamuliro wake. Izi n’zofanana ndi zomwe anachita pa nthawi ya Chigumula cha m’tsiku la Nowa.—Genesis 6:11-14; 7:1; Mateyu 24:37-39.

‘Tsiku Loopsa’

N’zoona kuti maulosi angapo a m’Baibulo onena za chiwonongeko chomwe chikubweracho ndi ochititsa mantha. Mwachitsanzo, mneneri Yoweli ananenapo za ‘tsiku la Yehova lalikulu loopsa.’ (Yoweli 2:31) Zida zimene Mulungu adzagwiritse ntchito zikuphatikizapo chipale chofewa, matalala, zivomezi, matenda opatsirana, mvula yambiri yochititsa madzi kusefukira, mvula ya moto ndi sulfure, chisokonezo chomwe chidzaphetse anthu, ziphaliwali, ndi nthenda yowoletsa minofu. * (Yobu 38:22, 23; Ezekieli 38:14-23; Habakuku 3:10, 11; Zekariya 14:12, 13) Ndipo Baibulo limafotokoza momveka bwino za nthawi imene matupi a anthu akufa adzakuta dziko lonse lapansi, atasiyidwa kuti akhale manyowa kapena zakudya za mbalame ndi zinyama zina. (Yeremiya 25:33, 34; Ezekieli 39:17-20) Adani a Mulungu adzachita mantha kwambiri pankhondo imeneyo.—Chivumbulutso 6:16, 17.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti olambira Mulungu omvera ayenera kuopa zinthu zochititsa mantha zomwe zidzachitike pa Armagedo? Ayi, chifukwa atumiki a Mulungu padziko lapansi sadzamenya nawo nkhondo imeneyi. Kuwonjezera apo, Yehova adzawateteza. Komabe, olambira oona adzachita chidwi kwambiri poona momwe Mulungu adzagwiritsire ntchito mphamvu zake zochititsa mantha.—Salmo 37:34; Miyambo 3:25, 26.

Komabe, tisaiwale kuti mtumwi Yohane anauziridwa kutilimbikitsa kuti: “Wodala iye amene asunga mawu a chinenero cha buku ili,” kuphatikizapo chenjezo la Armagedo. (Chivumbulutso 1:3; 22:7) Koma kodi zingatheke munthu kusangalala poganizira za Armagedo?

Chenjezo la Mulungu

Kukakhala kuti kukubwera chimphepo kapena mvula yamkuntho yoopsa, akuluakulu a boma amapereka machenjezo kuti ateteze moyo wa anthu. Pofuna kuonetsetsa kuti aliyense amve chenjezolo, angatumize apolisi kwa anthu ndi zida zochenjezera anthuwo kapena angawatumize ku khomo ndi khomo. Cholinga chochitira zonsezi si kuchititsa anthu mantha, koma kuwathandiza kuchitapo kanthu kuti apulumutse moyo wawo. Anthu ozindikira amasangalala kumva machenjezowo, ndipo amene amachitapo kanthu pambuyo pake amakhala osangalala kwambiri.

N’chimodzimodzinso ndi chenjezo la Mulungu la “kavumvulu” amene watsala pang’ono kubwera wa Armagedo. (Miyambo 10:25) Yehova watiuza zomwe zidzachitike pa nkhondo yake m’Mawu ake olembedwa. Cholinga chake si kuchititsa anthu mantha koma kuwachenjeza ndi kuwathandiza kutembenuka mtima ndi kuyesetsa kumutumikira. (Zefaniya 2:2, 3; 2 Petro 3:9) Anthu amene amachita zimenezi adzapulumuka. Choncho sitiyenera kuopa nkhondo ya Mulungu yomwe ikubwerayo. M’malo mwake tikhoza kuyembekezera m’tsogolo tili ndi chidaliro ndiponso chikhulupiriro kuti “aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.”—Yoweli 2:32.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Tiyenera kukumbukira kuti mbali zina za Baibulo zinalembedwa m’mawu ophiphiritsira, kapena zizindikiro. (Chivumbulutso 1:1) Choncho sitingadziwe kuti kodi ndi zinthu ziti zotchulidwa m’maulosi amenewa zomwe zidzagwiritsidwedi ntchito, ndiponso zimene zili zophiphiritsira chabe.

[Chithunzi patsamba 12]

Mphepo yambiri kapena mvula ya mkuntho yoopsa ikayandikira, akuluakulu a boma amachenjeza anthu kuti ateteze moyo wawo

[Chithunzi patsamba 13]

Uthenga wa Mulungu wochenjeza za Armagedo cholinga chake n’choti anthu achitepo kanthu kuti apulumutse moyo wawo