Kukhala Lova Mwadzidzidzi
Kukhala Lova Mwadzidzidzi
“Ntchito itandithera, ndinamva mu nkhongono mwanga monsemu kuti zii. Ndinadziona kuti ndine wosanunkha kanthu n’komwe.” —Anatero Tony, wa ku Germany.
“Mutu unandikulira kwambiri. Popeza ndikulera ndekha ana anga, ndinada nkhawa kuti ana anga awiri ndiwadyetsa bwanji ndiponso ndalama zolipirira magetsi, madzi, ndi zina zotero ndizipeza kuti.”—Anatero Mary, wa ku India.
“Ndinakhumudwa kwambiri ntchito itandithera, ndipo ndinkada nkhawa kuti kaya ndipezanso ina.”—Anatero Jaime, wa ku Mexico.
PADZIKO lonse lapansi, anthu ambiri akukumana ndi mavuto amene Tony, Mary, ndi Jaime anakumana nawo. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000 zino, anapeza kuti anthu pafupifupi 10 pa anthu 100 alionse oyenera kukhala pa ntchito ku Ulaya ndi pakati pa Asia, omwe ndi anthu okwana pafupifupi 23 miliyoni, anali kufunafuna ntchito. M’mayiko ena osauka, anthu oposa munthu mmodzi pa anthu anayi alionse oyenera kukhala pantchito, ali pa ulova. Nyuzipepala ya The New York Times mu July 2003 inati, ku United States, “anthu pafupifupi 2.6 miliyoni achotsedwa ntchito m’miyezi 28 yapitayi.”
M’mayiko ambiri, zimakhala zovuta kwambiri kuti munthu apeze ntchito. Mwachitsanzo, chaka chilichonse anthu ambirimbiri omaliza maphunziro ku sekondale ndi ku koleji nawonso amayamba kufuna ntchito. Kuwonjezera apo, munthu akakhala kuti ali ndi digiri kapena anaphunzitsidwa ntchito inayake sizitanthauza kuti apeza ntchito imene anaphunzirayo. Choncho masiku ano si zachilendo kuona anthu akusintha ntchito kangapo pamoyo wawo. Ena mpaka asintha ntchito imene anaphunzira.
Ngati ntchito yakutherani, kodi mungatani kuti zikuyendereni bwino pamene mukufunafuna ntchito ina? Ndipo mukapeza ntchito, kodi mungatani kuti mukhalitse pantchitopo?