Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito

Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito

Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito

KODI ndi ndani amene amapeza ntchito yabwino kwambiri? Kodi nthawi zonse amakhala munthu wofunsira ntchito amene ali woyenerera kwambiri? “Ayi,” anatero Brian, munthu wothandiza anthu kupeza ntchito. “Amene amapeza ntchito nthawi zambiri amakhala munthu amene ali wodziwa bwino kufuna ntchito.” Kodi mungatani kuti muzitha kufuna bwino ntchito? Tiyeni tione mfundo zisanu zothandiza.

Chitani Zinthu Mwadongosolo

Ngati ntchito yabwino yakutherani kapena mwakhala lova kwa nthawi yaitali, n’zosavuta kutaya mtima. Katharina, telala wa madiresi wa ku Germany anati: “Ntchito itangondithera kumene, ndinkakhulupirira kuti ndipeza ina. Koma nditaona kuti miyezi ikutha ndipo sindikupezabe ntchito ina, ndinakhumudwa. Kenaka ndinafika poti zinkandivuta kukamba nkhani imeneyi ndi anzanga.”

Kodi mungatani kuti musakhale wokhumudwa? Buku lothandiza anthu kupeza ntchito lotchedwa Get a Job in 30 Days or Less linati: “M’pofunika kwambiri kuti mukhale ndi ndondomeko yanuyanu, ngati kuti muli pantchito, kuti m’mawa uliwonse muzidziwa zomwe muyenera kuchita tsiku limenelo.” Olemba bukuli anati ndi bwino “kukhala ndi zolinga za tsiku lililonse n’kumalemba zomwe mwachita.” Kuwonjezera apo, anati “m’mawa uliwonse muyenera kuvala zovala zimene mungavale popita kuntchito.” Chifukwa chiyani? “Mukavala bwino mumakhala wodzidalira ngakhale mukamalankhula pa foni.”

Indedi, ntchito yanu ikhale yoti mupeze ntchito, kaya zikutengereni nthawi yaitali bwanji. Katharina, amene tamutchula kale uja, anachita zinthu mwadongosolo chotero. Iye anati: “Ndinakatenga ma adiresi ndi manambala a mafoni a anthu omwe angandilembe ntchito ku ofesi ya boma yothandiza anthu kupeza ntchito. Ndinalemba makalata kapena kuimba foni kwa anthu amene analengeza ntchito zawo mu nyuzipepala. Ndinayang’anitsitsa buku la manambala a mafoni n’kulemba m’ndandanda wa makampani amene angakhale ndi ntchito zomwe anali asanazilengeze, kenaka ndinawaimbira mafoni. Ndinalembanso kalata yofotokoza za maphunziro anga, ntchito zimene ndagwirapo, ndi mbiri yanga, imene mwachidule amaitcha CV, n’kuitumiza ku makampani amenewa.” Chifukwa chofunafuna ntchito mwadongosolo chonchi, Katharina anapeza ntchito yabwino.

Fufuzani Ntchito Zimene Sizinalengezedwe

Msodzi amene ali ndi ukonde waukulu kwambiri mwachidziwikire ndi amene angagwire nsomba zambiri kuposa ena onse. Choncho, nanunso mukadziwa momwe mungakulitsire “ukonde” wanu pofunafuna ntchito zingakuthandizeni kupeza ntchito mosavuta. Ngati mukufuna ntchito mwa kufunsira ntchito zokhazo zomwe azilengeza mu nyuzipepala ndi pa Intaneti, ntchito zambiri zikhoza kumasemphana ndi ukonde wanu. Ntchito zambiri sazilengeza n’komwe. Kodi mungatani kuti muzitulukire ntchito zoterezi?

Kuwonjezera pa kufunsira ntchito zimene azilengeza, mofanana ndi Katharina muyenera kupatula nthawi mlungu uliwonse kuimba mafoni kapena kupita ku makampani amene mukuganiza kuti angakhale ndi ntchito zomwe mungathe kugwira. Musadikire kuti ntchitozo azilengeze kaye. Ngati bwana mmodzi wanena kuti alibe ntchito, m’funseni ngati akudziwa kwina kumene mungakafunsireko ntchito ndi amene muyenera kukalankhula naye. Akakutchulirani kampani inayake, konzani zopita ku kampaniko, ndipo mukatchule dzina la munthu amene anakuuzani za kampaniyo.

Tony, amene tinamutchula mu nkhani yapita ija, anapeza ntchito mwanjira imeneyi. Iye anafotokoza kuti: “Ndinayamba ndine kupita ku makampani ngakhale kuti anali asanalengeze ntchito iliyonse. Kampani ina inandiuza kuti analibe ntchito iliyonse panthawi imeneyo koma anandiuza kuti ndidzayesenso pakatha miyezi itatu. Ndinachita zimenezo, ndipo anandilemba ntchito.”

Primrose, mayi amene akulera yekha ana wa ku South Africa, anachita zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Panthawi imene ndinali kuchita maphunziro othandiza anthu ovulala asanapite kuchipatala, ndinaona kuti kutsidya lina la msewu anali kumangako nyumba yatsopano ndipo ndinamva kuti nyumbayo idzakhala yosamalirako anthu okalamba. Ndinayesera kambirimbiri kuti ndilankhulane ndi bwana wa pamalopo. Pamapeto pake anandiuza kuti analibe ntchito iliyonse panthawi imeneyo. Komabe, ndinkabwerabwera kudzafunsa ngati ndingathe kugwirako ntchito, ngakhale mongodzipereka. Pomalizira pake anandilemba ntchito ya kanthawi kochepa basi. Ndinalimbikira ntchito iliyonse yomwe ankandipatsa kuti ndigwire. Chifukwa cha zimenezi, ndinapeza mapepala ena oyenera ndipo anandilemba ntchito yokhalitsa.”

Mungafunsenso anzanu, achibale anu, ndi anthu ena odziwana nawo kuti akuthandizeni kutulukira ntchito zomwe sizinalengezedwe. Jacobus, munthu wophunzitsa anthu ndi makampani momwe angapewere ngozi wa ku South Africa, anapeza ntchito mwanjira imeneyi. Iye anati: “Kampani imene ndinkagwirako ntchito itatsekedwa, ndinauza anzanga ndi achibale kuti ndikufunafuna ntchito. Tsiku lina mnzanga wina anamva anthu awiri akucheza ali pa mzere wokalipirira zinthu m’sitolo. Mayi mmodzi ankafunsa mayi wina ngati akudziwa munthu aliyense amene anali kufuna ntchito. Mnzangayo analowerera nkhaniyo ndipo anauza mayiyo za ine. Tinagwirizana zokumana ndi mayiyo, ndipo anandilemba ntchitoyo.”

Khalani Okonzeka Kugwira Ntchito Iliyonse

Kuti musavutike kupeza ntchito, muyenera kukhala okonzeka kugwira ntchito iliyonse. Jaime, amene tinamutchula mu nkhani yapita ija, anati: “N’zokayikitsa kuti mungapeze ntchito yokhala ndi zonse zomwe mukufuna. Muyenera kuphunzira kukhutira ndi ntchito yomwe si yabwino kwenikweni kwa inu.”

Kukhala wokonzeka kugwira ntchito iliyonse kungatanthauze kuti muyenera kusintha kaonedwe kanu ka ntchito zinazake. Taganizirani zomwe anachita Ericka, amene amakhala ku Mexico. Iye anaphunzira ntchito yokhala mlembi wa bwana wamkulu, koma poyamba sanathe kupeza ntchito imene amafunayo. Iye anati: “Ndinaphunzira kuvomera ntchito ya mtundu uliwonse. Kwa kanthawi, ndinagwira ntchito yogulitsa zinthu m’sitolo. Ndinkagulitsanso masamusa pamsewu ndi kukolopa m’nyumba za anthu. Pamapeto pake ndinatha kupeza ntchito yogwirizana ndi maphunziro anga.”

Mary, amene tinamutchula mu nkhani yapita ija, atachotsedwa ntchito ya mu ofesi, nayenso anaona kuti afunika kukhala wokonzeka kugwira ntchito iliyonse. Iye anafotokoza kuti: “Sindinaumirire kupeza ntchito ngati yomwe ndinali nayo kale. Ndinafuna kudziwa za ntchito iliyonse yomwe ndinamvapo, ngakhale ntchito zimene ena angaone ngati zonyozeka. Chifukwa cha zimenezi, ndinapeza ntchito imene inandithandiza kusamalira ana anga awiri.”

Lembani CV Yabwino

Kwa anthu amene akufunsira ntchito kuti akhale mabwana, kulemba ndi kutumiza CV yolembedwa mwaluso n’kofunika kwambiri. Koma kaya mukufuna ntchito yotani, kukhala ndi CV yolembedwa bwino kungakuthandizeni kwambiri. Nigel, munthu wothandiza anthu kupeza ntchito wa ku Australia anati: “CV imauza olemba ntchitowo kuti inuyo ndi ndani komanso zomwe mwachitapo ndiposo chifukwa chake ayenera kukulembani ntchito.”

Kodi mungalembe bwanji CV? Lembani dzina lanu lonse, adiresi yanu, nambala yanu ya foni, ndi adiresi yanu ya e-mail. Lembani cholinga chanu. Lembani maphunziro amene mwachita, ndipo gogomezerani maphunziro ndi luso lililonse lomwe muli nalo logwirizana ndi ntchito imene mukufunayo. Fotokozani ntchito zimene munagwirapo kale. Musangolemba zimene munachita basi koma muperekenso zitsanzo za zolinga zimene munakwaniritsa ndi phindu limene munabweretsera mabwana anu akale. Gogomezeraninso mbali za ntchito yanu yakale zomwe zikukuchititsani kuti mukhale woyenerera ntchito imene mukuifuna panoyi. Lembani zinthu zokhudza inuyo zofotokoza khalidwe lanu, zokonda zanu, ndi zimene mumakonda kuchita panthawi yanu yopuma. Popeza zofuna za makampani zimasiyana, mungafunike kusintha CV yanu pofunsira ntchito ku makampani osiyanasiyana.

Kodi muyenera kulemba CV ngati mukufunsira ntchito koyamba? Inde! Pakhoza kukhala zinthu zambiri zomwe munachitapo zomwe munganene kuti zili ngati ntchito zomwe munagwirapo kale. Mwachitsanzo, kodi muli ndi zimene mumakonda kuchita panthawi yanu yopuma, monga zosemasema kapena mwina kukonza magalimoto akale? Mukhoza kutchula zinthu zimenezi pa CV yanu. Kodi munagwirapo ntchito iliyonse mongodzipereka? Tchulani mtundu wa ntchito yongodzipereka yomwe mwachitapo ndi zolinga zomwe munakwaniritsa.—Onani bokosi lakuti “Chitsanzo cha CV ya Anthu Omwe Sanagwirepo Ntchito.”

Ngati bwana winawake sanafune kukulembani ntchito, siyani kakhadi kakang’ono, kakakulu masentimita 10 m’lifupi ndi masentimita 15 m’litali, kokhala ndi dzina lanu, adiresi yanu, nambala yanu ya foni, ndi adiresi yanu ya e-mail, komanso mfundo zachidule zonena za luso lanu ndi zimene munachitapo. Kuseri kwa khadilo mungaikeko chithunzi chanu kapena chithunzi cha inuyo muli ndi anthu a m’banja lanu, ngati zimenezi zili zoyenera. Patsani khadi limeneli anthu onse amene angakuthandizeni kupeza ntchito, ndipo muwapemphe kuti azilipereka kwa aliyense amene akufuna munthu woti adzagwire ntchito imene inuyo mukufuna. Munthu wolemba anthu ntchito akaona khadi limeneli, akhoza kukuitanani kuti akakufunseni mafunso olowera ntchito, ndipo mwina angakulembeni ntchitoyo.

Kulemba CV kumakuthandizani kuti musamade nkhawa kwambiri pamene mukufunafuna ntchito. Nigel, amene tamutchula kale uja, anati: “Kulemba CV kumakuthandizani kuganiza bwino ndi kusanja zolinga zanu bwinobwino. Kumakuthandizaninso kudzidalira, chifukwa kumakuthandizani kukonzekera mafunso amene angakufunseni polowa ntchito.”—Onani bokosi pa tsamba 7.

Konzekerani Bwino Mafunso Olowera Ntchito

Kodi pokonzekera kukayankha mafunso olowera ntchito mungachite chiyani? Zingakhale bwino mutafufuza za kampani imene mukufuna kukagwirako ntchitoyo. Ngati mukudziwa zambiri za kampaniyo, pokufunsani mafunso olowera ntchito mungaoneke kuti ndinu munthu wodziwa zambiri. Kafukufuku wanuyo angakuthandizeninso kudziwa ngati kampaniyo ilidi ndi ntchito imene mukufuna, ndiponso ngati mungakonde kugwira ntchito pakampaniyo.

Kenaka, ganizirani zomwe mudzavale pokafunsidwa mafunsowo. Ngati ntchito imene mukufunayo ndi yamanja, valani zovala zoyenera zochapa ndi zosita bwino. Kuvala zovala zochapa ndi zosita bwino kumamuuza bwanayo kuti mumaona kuti kuoneka bwino n’kofunika, choncho mwachidziwikire mudzaonanso kuti kugwira bwino ntchito n’kofunika. Ngati mukufuna ntchito ya mu ofesi, valani zovala zoyenera zomwe mabwana amavala popita ku ofesi kudera komwe mumakhalako. Nigel anati: “Sankhani zovala zanu tsiku lomwe mukufunika kupita kokafunsidwa mafunsolo likadali kutali kuti musadzagwire njakata nthawi itakutherani n’kudziwonjezera dala nkhawa mutangotsala pang’ono kukafunsidwa mafunsowo.”

Nigel anatinso ndi bwino kufika kumalo ofunsira mafunsowo pafupifupi mphindi 15 nthawi yake isanakwane. N’zoona kuti kufika msanga kwambiri si chinthu chanzeru. Koma kufika mochedwa kungakuwonongereni mwayi wanu wolembedwa ntchitoyo. Akatswiri amati masekondi atatu oyambirira pamene akukufunsani mafunso ndi ofunika kwambiri. Pakanthawi kochepa kameneko, wofunsa mafunsoyo amaona momwe mukuonekera ndiponso khalidwe lanu, zomwe zingamuchititse kukuganizirani zabwino kapena zoipa. Ngati mwafika mochedwa, adzakuganizirani zoipa kwambiri. Kumbukirani kuti simudzakhalanso ndi mwayi wina wokonza zomwe munalakwitsa poyamba.

Kumbukiraninso kuti wofunsa mafunsoyo si mdani wanu. Zili choncho chifukwa mwina nayenso anafunika kufunsira ntchito yakeyo, choncho akudziwa momwe mukumvera. Ndipo akhoza kukhala ndi mantha, chifukwa mwina anangophunzitsidwa pang’ono chabe, kapena sanaphunzitsidwe n’komwe momwe ayenera kufunsira mafunso. Kuwonjezera apo, ngati wofunsa mafunsoyo ali mwiniwake wa kampaniyo, akhoza kudzipweteketsa ngati atalemba ntchito munthu wosayenerera ntchitoyo.

Kuti zonse ziyambike bwino akamakufunsani mafunsowo, mwetulirani ndipo mugwireni chanza champhamvu bwino wofunsa mafunsoyo ngati zimenezo n’zomwe anthu amachita kudera kwanu. Pamene akukufunsani mafunso, nenani zimene bwana wanuyo akufuna basi, ndi zimene inuyo mungathe kuchita. Ponena za zinthu zimene muyenera kupewa, Nigel anati: “Musamasunthesunthe pampando kapena kukhala mothifuka msana. Munthu akakhala moongoka bwino amasonyeza kuti ndi wodzidalira. Musamalankhule momasuka kwambiri ndipo musamachulutse zonena, ndiponso musayerekeze dala kutukwana. Ndiponso musamanene zoipa za abwana anu akale ndi antchito anzanu akale. Ngati mukuwanenera zoipa, wofunsa mafunsoyo angaganize kuti simudzasangalalanso ndi ntchito imene mwafunsirayi.”

Ponena za zinthu zimene muyenera kuchita ndi kunena akamakufunsani mafunso, akatswiri amapereka malangizo otsatirawa: Muzimuyang’ana kumaso wofunsa mafunsoyo, muziyendetsa manja anu mwachibadwa mukamalankhula, ndipo muzitchula bwino mawu. Muziyankha mafunso mwachidule ndiponso mwachilungamo, ndipo muzifunsa mafunso ogwirizana ndi kampaniyo ndi ntchito imene mukufunayo. Nthawi yokufunsani mafunsoyo ikatha, ngati mukuifunabe ntchitoyo, funsani ngati angakulembeni ntchitoyo. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti mukuifunitsitsadi.

Mukatsatira malangizo ali pamwambawa, mukhoza kupeza ntchito mosavuta. Zikatero, kodi mungatani kuti mukhalitse pantchitopo?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

Chitsanzo cha CV ya Anthu Omwe Sanagwirepo Ntchito

Dzina Lanu:

Adiresi Yanu:

Nambala Yanu ya Foni ndi Adiresi Yanu ya E-Mail:

Cholinga: Kufunsira ntchito ya munthu wongoyamba kumene pa kampani yopanga zinthu.

Maphunziro: Ndinamaliza maphunziro a ku sekondale pa Kumudzi Sekondale Sukulu mu 2004.

Maphunziro Amene Ndinatenga: Zinenero, masamu, makompyuta, zosemasema.

Luso: Ndimagwira bwino ntchito zamanja. Ndimakonza galimoto yakwathu nthawi ndi nthawi. Ndinapangapo mipando yamatabwa ndi tebulo kunyumba kwathu. Ndimakonda kugwiritsa ntchito masamu ndikamapanga zinthu zamatabwa za m’nyumba. Ndinakhoma denga pa ntchito yomanga nyumba mongodzipereka. Ndimatha kugwiritsa ntchito makompyuta osiyanasiyana ndipo ndimakonda kuphunzira mapulogalamu atsopano a makompyuta.

Zokhudza Ineyo: Ndine wokhulupirika—sindinapite kusukulu masiku awiri okha chaka changa chomaliza ku sekondale. Ndine wachilungamo—ndinabweza kachikwama kotayika muli ndalama. Ndine wochezeka—ndimagwira ntchito mongodzipereka kudera kwathu nthawi ndi nthawi ndipo ndimasangalala kuthandiza anthu okalamba. Masewera—ndimakonda kusewera mpira. Zomwe ndimakonda kuchita panthawi yanga yopuma—ndimakonda kukonza magalimoto ndi kusema zinthu.

Amene Mungawafunse za Ine: Ndikhoza kukupatsani mayina awo mutawafuna. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 41 Anthu amene angawafunse za inu akhoza kukhala mphunzitsi amene amakudziwani bwino kapena munthu amene amadziwana ndi banja lanu amene ali ndi bizinesi yake. Pouza abwanawo kuti mungawapatse mayinawo atawafuna, mungadziwe msanga ngati akufuna kukulembani ntchito. Muonetsetse kuti muyambe kaye mwawapempha anthu amene mukufuna kuti adzanene za inuwo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

Mafunso Amene Mungafunsidwe Polowa Ntchito

❑ N’chifukwa chiyani mwafunsira ntchito imeneyi?

❑ N’chifukwa chiyani mukufuna kugwira ntchito pa kampani ino?

❑ Kodi mukudziwapo chiyani za ntchito/kampani/ bizinesi imeneyi?

❑ Kodi munagwirapo ntchito yotereyi?

❑ Kodi mumadziwa kuyendetsa makina otani?

❑ Kodi munagwirapo ntchito yotereyi zaka zingati?

❑ Kodi muli ndi luso lotani lomwe lingakhale lothandiza pantchito imeneyi?

❑ Tandiuzani za inuyo.

❑ Kodi ndi mawu asanu ati amene mungadzifotokoze nawo bwino?

❑ Kodi mumatha kugwira ntchito muli pampanipani?

❑ Kodi n’chifukwa chiyani munasiya ntchito yanu yakale?

❑ N’chifukwa chiyani mwakhala nthawi yaitali muli lova?

❑ Kodi abwana anu akale ankakuonani bwanji?

❑ Kodi simunapite kuntchito kangati pa ntchito yanu yakale?

❑ Kodi zolinga zanu za m’tsogolo n’zotani?

❑ Kodi mungayambe liti ntchitoyi?

❑ Kodi mumadziwa kwambiri kuchita zinthu ziti?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Kodi Muyenera Kugwiritsa Ntchito Makampani a pa Intaneti Othandiza Anthu Kupeza Ntchito?

Malo a pa Intaneti a kampani inayake yaikulu ya ku United States yothandiza anthu kupeza ntchito ali ndi ma CV a anthu 17 miliyoni amene mabwana ofuna kupeza antchito angaone. Malowa alinso ndi ntchito zokwana 800,000 zomwe anthu ofuna kupeza ntchito angaone ngati akuzifuna. Kafukufuku akusonyeza kuti anthu 96 pa anthu 100 alionse m’mayiko ena amafuna ntchito pa Intaneti. Komabe, pa kafukufuku amene anachita pakati pa anthu okhala ndi maphunziro antchito apamwamba ochokera m’mayiko 40 anapeza kuti ndi anthu 5 okha pa anthu 100 alionse amene amapezadi ntchito pa Intaneti.

Mukaika CV yanu pa Intaneti, anthu ambiri olemba anthu ntchito angadziwe kuti mukufuna ntchito, koma m’pofunika kusamala. Mukatero zimatanthauzanso kuti anthu ambiri akhoza kukuberani mwachinyengo. Kuti mudziteteze, akatswiri odziwa za zimenezi akupereka malangizo otsatirawa:

1. Werengani malamulo oteteza nkhani zachinsinsi za munthu amene kampani yothandiza anthu kupeza ntchito pa Intanetiyo imatsatira musanaike CV yanu pa malo awo a pa Intaneti. Makampani ena othandiza anthu kupeza ntchito pa Intaneti amagulitsa nkhani zachinsinsi zokhudza inuyo kwa makampani ena kapena kwa anthu ena amene angazifune.

2. Muziika CV yanu pa malo ochepa okha a makampani othandiza anthu kupeza ntchito pa Intaneti, odziwika kuti ndi odalirikadi. M’pofunika kwambiri kuteteza nkhani zanu zachinsinsi kuti wina asazigwiritse ntchito molakwika. Mu CV yanu musamalembemo zinthu zimene mbala ingagwiritse ntchito kunamizira kuti iyoyo ndi inuyo n’kukubweretserani mavuto ambiri azachuma. Anthu achilungamo ofuna kukulembani ntchito safunikira kudziwa nambala ya akaunti yanu ya ku banki, nambala ya khadi lanu logulira zinthu pangongole, kapena tsiku limene munabadwa.

3. Samalani ndi ntchito zosadziwika bwinobwino zimene zalengezedwa. Pam Dixon, amene amagwira ntchito yochita kafukufuku ku bungwe loteteza nkhani zachinsinsi za anthu lotchedwa World Privacy Forum anati, ngati ntchito imene ikulengezedwa sanaifotokoze bwinobwino kuti ndi yotani, ndiye kuti mwina si ntchito yeniyenidi. Iye anati: “Mawu okokomeza ngati akuti ‘Tili ndi ntchito masauzande ambiri’ kapena ‘Timagwira ntchito ndi makampani akuluakulu’ muyenera kusamala nawo.” Iye anawonjezeranso kuti: “Akakupemphani kuti mutumizenso CV ina zingatanthauzenso kuti mwina kampaniyo ndi ya anthu akuba.”

Kumbukirani kuti ngakhale makampani achilungamo othandiza anthu kupeza ntchito pa Intaneti palibe chomwe angachite CV yanu ikatengedwa ndi bwana wofuna kulemba anthu ntchito kapena munthu wina amene ali nayo chidwi.

[Chithunzi patsamba 5]

NCHITO

Konzekerani bwino mafunso olowera ntchito

Lembani CV yabwino

Khalani okonzeka kugwira ntchito iliyonse

Fufuzani ntchito zimene sizinalengezedwe

Chitani zinthu mwadongosolo

[Chithunzi patsamba 7]

Kuti munthu apeze ntchito amafunika kuchita khama ndi kufufuza bwino

[Chithunzi patsamba 8]

Kuchita zinthu ngati momwe amachitira anthu apantchito kungakuthandizeni pamene akukufunsani mafunso