Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Munthu Angasiyire Kuba M’masitolo

Mmene Munthu Angasiyire Kuba M’masitolo

Mmene Munthu Angasiyire Kuba M’masitolo

“Kuchepetsa umbava si ntchito yanu yokha, ndi ntchito ya aliyense m’dera lanulo. Aliyense amapindula umbava ukatha.”—LINATERO BUKU LOTCHEDWA “EVERY RETAILER’S GUIDE TO LOSS PREVENTION.”

KUBA m’masitolo, mofanana ndi makhalidwe ena oipa, kumapotoza maganizo a munthu, ndipo kumamuchititsa kuti azidzilungamitsa. Choncho, mofanana ndi momwe mlimi amazulira udzu m’munda mwake, anthu amene akufuna kusiya kuba m’masitolo ayenera kuchotsa muzu wa vuto lawolo, womwe ndi maganizo oipa. Pa Aroma 12:2, Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘mukonzenso mitima yanu.’ Ndipo pa 1 Petro 1:14, limatilimbikitsa kuti ‘tisadzifanizitsenso ndi zilakolako zakale.’ Mfundo zisanu zotsatirazi zingathandize munthu woba m’masitolo kuti asinthe maganizo ake pa nkhani ya kuba.

Mfundo Zothandiza Munthu Kuganiza Bwino

▪ Choyamba, kuba m’masitolo n’kuphwanya malamulo a dziko. Kuba m’masitolo kukhoza kukhala kofala kudera lomwe munthuyo amakhala, ndipo akhoza kupulumuka osagwidwa, koma wakubayo akuphwanyabe lamulo.—Aroma 13:1.

Kodi n’chiyani chimachitika anthu ambiri akamaphwanya malamulo? Malinga ndi zimene Baibulo limanena, ‘chilamulo chimalekeka.’ (Habakuku 1:3, 4) Kapena tingati phindu lotsatira malamulo silionekanso, ndipo zotsatirapo zake n’zoti m’dziko mumayamba chisokonezo. Nthawi iliyonse imene munthu akuba m’sitolo, amafooketsa anthu amene amatsatira malamulo m’dzikomo. Zimenezi zikachitika, aliyense amavutika.

▪ Chachiwiri, kuba m’masitolo kumathetsa kukhulupirirana. Kusakhulupirirana koteroko kumawononga maubwenzi a anthu, ndipo kumachititsa kuti zikhale zovuta kuti anthu amvetsetsane ndi kuchitirana zinthu mwachilungamo.—Miyambo 16:28.

Mayi wina amene anali ndi sitolo yogulitsa zovala ndipo anatseka sitoloyo italowa pansi chifukwa cha akuba anati: “Vuto langa lalikulu linali loti ndinkakhulupirira kwambiri anthu.” Kale ankakhulupirira kuti makasitomala ndiponso antchito ake sangamubere. Panopa amaona kuti analakwa kuwakhulupirira choncho.

Munthu mmodzi akhoza kunama kwa mnzake ndipo mnzakeyo angayambe kumamuona kuti ndi munthu wabodza. Koma anthu oba m’masitolo amachititsa kuti aliyense amene akulowa m’sitolomo imene anabamoyo azikayikiridwa. Amachititsa kuti anthu oona mtima azioneka ngati anthu oti akhoza kuba. Kodi n’chilungamo kuti munthu winawake aipitse mbiri ya anzake moteremu?

▪ Chachitatu, khalidwe loba m’masitolo lingachititse munthu kuyamba kuchita umbanda wina woopsa. Pakapita nthawi, anthu oba m’masitolo angayambe kumachita zaumbanda zina zikuluzikulu.—2 Timoteo 3:13.

Kuba M’masitolo Kudzatheratu

▪ Chachinayi, ndiponso chofunika kwambiri, munthu amene amaba ndiye kuti akusemphana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Mawu Ake amauza wakuba kuti “asabenso” ndipo amachenjeza kuti amene samvera Mulungu adzaweruzidwa. (Aefeso 4:28; Salmo 37:9, 17, 20) Koma Yehova amakhululukira mbava zimene zasintha. Zikhoza kukhalanso pamtendere ndi Mulungu.—Miyambo 1:33.

▪ Chachisanu, kuba m’masitolo, mofanana ndi umbanda wina wonse, posachedwapa sikudzakhalaponso. Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padziko lapansi monga momwe Baibulo linalonjezera, anthu azidzachitirana zinthu mokhulupirika ndiponso moona mtima. Zimenezi zikutanthauza kuti tidzapuma ku mavuto aakulu amene kuba m’masitolo kumabweretsa.—Miyambo 2:21, 22; Mika 4:4.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

NJIRA ZOSALIRA NDALAMA ZAMBIRI ZOPEWERA KUBEREDWA

Mabizinesi ena ang’onoang’ono mwina sakhala ndi ndalama zokwanira zoti agulire zida zodzitetezera zokwera mtengo. Koma zimenezi sizitanthauza kuti palibe chilichonse chomwe angachite kuti asaberedwe. Nthawi zambiri mabizinesi angateteze katundu wawo pochita zinthu zingapo zosavuta.

M’buku limene apolisi awiri ofufuza milandu, Michael Brough ndi Derek Brown, analembera limodzi, anatsindika kufunika koyang’anitsitsa makasitomala anu. Iwo anati: “Muziyang’anitsitsa munthu aliyense. . . . Inuyo ndi antchito anu ndi amene muli chitetezo chachikulu.” Iwo anati mungapite kwa munthu amene mukumukayikira kuti angabe m’sitolomo n’kumufunsa kuti: “Kodi mwapeza zimene mukufuna? Zisiyeni polipirirapo kuti akuwonkhetsereni.” “Kodi mukufuna kuti ndikukulungireni?” “Kodi juziyo ndi ya saizi imene mukufuna?” “Kodi ndikubweretsereni basiketi?” Apolisiwo anati: “Zimenezi zimauza makasitomala achilungamo kuti mukufuna kuwathandiza ndiponso mbava kuti mukuziona.”

Ponena za kulongedza bwino katundu, iwo anati: “Maalumali oikamo zinthu zogulitsa azikhala odzaza ndiponso olongedzedwa bwino. Kuyang’ana pafupipafupi mmene katundu alili pa alumali kumakuthandizani kumudziwa bwino katunduyo, ndipo ngati ali wolongedzedwa bwino, n’zosavuta kudziwa kuti chinachake chasunthidwa kapena chachotsedwa.”—Zachokera m’buku lotchedwa Every Retailer’s Guide to Loss Prevention.

Munthu wina wofufuza milandu dzina lake Russell Bintliff anati: “Kukhala ndi njira zosatchingidwa ndi chilichonse ndiponso maalumali odzaza kumathandiza anthu ogwira ntchito m’sitolomo kuona zomwe makasitomala akuchita. Mwa kuyenda m’njira imene munthu wokayikitsa ali, wogwira ntchito m’sitolomo angaone chomwe chikusowa pa alumali ndiyeno, ponamizira kuona katundu pa alumalipo, angaone zomwe munthuyo waika m’basiketi yake. . . . Anthu oba m’masitolo angadziwe zomwe zikuchitika, pamene makasitomala achilungamo sangadziwe n’komwe kuti wogwira ntchito m’sitoloyo akuwayang’ana.” Ponena za momwe muyenera kusanjira maalumali ndi njira za m’sitolomo, iye anati: “Ayenera kuzisanja m’njira yoti [mwini sitolo] ndi antchito ake azitha kuona bwinobwino zomwe makasitomala akuchita.”—Zachokera m’buku lotchedwa Crimeproofing Your Business—301 Low-Cost, No-Cost Ways to Protect Your Office, Store, or Business.

[Chithunzi patsamba 25]

Chilungamo chimalimbikitsa kukhulupirirana ndi ubwenzi wabwino