Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinafunitsitsa Kukwanitsa Cholinga Changa

Ndinafunitsitsa Kukwanitsa Cholinga Changa

Ndinafunitsitsa Kukwanitsa Cholinga Changa

YOSIMBIDWA NDI MARTHA CHÁVEZ SERNA

Tsiku lina ndili ndi zaka 16, ndikugwira ntchito kunyumba ndinakomoka. Mmene ndimatsitsimuka, ndinapezeka kuti ndili pabedi. Zimenezi ndinazunguzika nazo maganizo, ndiponso mutu unali ukundipweteka kwambiri. Kwa mphindi zingapo, sindinathe kuona kapena kumva. Ndinali ndi mantha kwambiri. Kodi n’chiyani chinandichitikira?

MAKOLO anga anada nkhawa kwambiri, ndipo anandipititsa kwa dokotala, amene anandipatsa mavitamini. Dokotalayo anati ndinakomoka chifukwa chogona mochedwa. Patatha miyezi yochepa ndinakomokanso kachiwiri, ndipo kenaka ndinakomoka kachitatu. Tinapita kwa dokotala wina, amene anaganiza kuti ndinali kukomoka chifukwa chochita phuma, ndipo anandipatsa mankhwala okhazika mtima pansi.

Komabe, ndinayamba kukomoka pafupipafupi. Nthawi zambiri ndinkagwa pansi n’kuvulala. Nthawi zina ndinkadziluma lilime ndiponso mkamwa. Ndikatsitsimuka, mutu unkandipweteka kwambiri ndiponso ndinkachita nseru. Thupi langa lonse linkapweteka ndipo nthawi zambiri sindinkakumbukira chomwe chinachitika ndisanakomoke. Kuti ndichire, ndinkafunika kugona tsiku lathunthu, kapena masiku awiri. Ngakhale zinali choncho, ndinkakhulupirira kuti vuto limeneli linali losakhalitsa, ndiponso kuti pakapita kanthawi ndikhalanso bwino.

Mmene Matendawa Anasokonezera Zolinga Zanga

Ndili mwana, makolo anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Aphunzitsi athu anali apainiya apadera awiri, kapena kuti atumiki a nthawi zonse amene amatha maola ambiri mwezi uliwonse akuphunzitsa anthu ena mfundo zoona za m’Baibulo. Ndinkatha kuona kuti apainiya awiriwo anali kusangalala chifukwa cha utumiki wawo. Nditayamba kulankhula ndi aphunzitsi anga ndi anzanga a kusukulu za malonjezo a m’Baibulo, nanenso ndinayamba kusangalala ngati apainiya aja.

Patapita nthawi yochepa, anthu ambiri a m’banja mwathu anakhala Mboni za Yehova. Ndinkakonda kwambiri kulalikira uthenga wabwino. Nditakwanitsa zaka seveni, ndinakhala ndi cholinga choti ndidzakhale mpainiya wapadera. Nditakwanitsa zaka 16, ndinabatizidwa, zomwe zinali zofunika kwambiri kuti ndidzathe kukwanitsa cholinga changa chija. Koma apa m’pamene ndinayamba kumakomoka.

Utumiki Waupainiya

Ngakhale kuti ndinkakomoka choncho, ndinaganizabe kuti ndikhoza kukhala mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova. Koma popeza ndinkakomoka mwina kawiri pamlungu, anthu ena mumpingo mwathu anaganiza kuti sichinthu chanzeru kuti ndiyambe utumiki wanthawi zonse, womwe ndi ntchito yovuta. Ndinakhumudwa kwambiri kumva zimenezi. Koma patapita nthawi, munthu wina ndi mkazi wake omwe anali kutumikira pa nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico anabwera ku mpingo kwathu. Anamva zoti ndinkafuna kuchita upainiya ndipo anandilimbikitsa kwambiri. Ananditsimikizira kuti ndikhoza kukwanitsa kuchita upainiya ngakhale ndinali kudwala.

Choncho pa September 1, 1988, ndinaikidwa kukhala mpainiya wokhazikika m’tauni yakwathu ya San Andrés Chiautla, ku Mexico. Mwezi uliwonse ndinkatha maola ambiri ndikulalikira uthenga wabwino. Ndikakhala kuti sindingathe kulalikira panja chifukwa choti ndinakomoka, ndinkalemba makalata ofotokoza zinthu za m’Malemba kwa anthu a m’dera lathu. Choncho ndinkatha kuwalimbikitsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo.

Matenda Anga Anawatulukira

Panthawi imeneyi, makolo anga anandipititsa kwa dokotala wodziwa za matenda a ubongo, ngakhale kuti zinawathera ndalama zambiri kuti achite zimenezi. Dokotala ameneyu anatulukira kuti matenda angawo anali khunyu. Chifukwa cha chithandizo chimene ndinalandira nthawi imeneyi, matenda anga sanandivutitsenso kwa zaka zinayi. Panthawi imeneyi ndinapita ku Sukulu ya Utumiki Waupainiya, ndipo zomwe ndinaphunzira kumeneko zinandichititsa kuti ndizifuna kwambiri kutumikira kudera kumene kumafunika alaliki owonjezereka.

Makolo anga ankadziwa kuti ndinkafunitsitsa kuchita zambiri pa utumiki wanga. Popeza matenda anga sanali kundivutitsanso chifukwa cha mankhwala amene ndinali kumwa, anandilola kupita ku Zitácuaro, ku chigawo cha Michoacán, komwe kunali mtunda wa makilomita 200 kuchokera kwathu. Kudziwana ndi apainiya ena pamene ndinali kutumikira kumeneko kunandithandiza kukonda kwambiri utumiki wa nthawi zonse kuposa kale.

Koma nditatha zaka ziwiri ku Zitácuaro, ndinayambiranso kukomoka. Ndinabwerera kunyumba kwa makolo anga ndili wokhumudwa, komanso ndinkafunikira kukaonana ndi dokotala. Ndinapita kwa dokotala wa matenda a ubongo amene anandiuza kuti mankhwala amene ndinali kumwa anali kundiwononga chiwindi. Ndinayamba kufunafuna chithandizo cha mtundu wina, popeza sitikanakwanitsanso kuonana ndi dokotala wa ubongo uja. Matenda anga anali kuipiraipira, ndipo ndinasiya upainiya. Nthawi iliyonse yomwe ndakomoka ndinkaona kuti ndikutalikirana ndi cholinga changa chija. Koma ndikawerenga Masalmo n’kupemphera kwa Yehova, ndinkamva kuti wanditonthoza ndiponso wandipatsa mphamvu.—Salmo 94:17-19.

Ndinakwanitsa Cholinga Changa

Panthawi imene matenda anga anafika poipa kwambiri, ndinkakomoka kawiri patsiku. Koma kenaka zinthu zinasintha. Dokotala winawake anandipatsa mankhwala enaake a khunyu, ndipo ndinayamba kupeza bwino kwa nthawi yotalikirapo. Choncho pa September 1, 1995, ndinayambiranso upainiya. Thanzi langa linakhalabe bwinobwino, choncho nditatha zaka ziwiri osakomoka, ndinafunsira kuti ndikhale mpainiya wapadera. Kuchita upainiya wapadera kukanafuna kuti ndizitha maola ochuluka mu utumiki kuposa mmene ndinali kuchitira, ndiponso kuti ndiyenera kukhala wokonzeka kupita kukatumikira kulikonse komwe ndingafunike. Tangoganizirani momwe ndinamvera atandiika kukhala mpainiya wapadera! Ndinakwanitsa cholinga chomwe ndinakhala nacho kuyambira ndili mwana.

Pa April 1, 2001, ndinayamba utumiki wanga watsopano m’dera lamapiri la ku chigawo cha Hidalgo. Panopa ndikutumikira m’tauni yaing’ono m’chigawo cha Guanajuato. Ndimafunika kumwa mankhwala anga mosamala kwambiri ndiponso kupuma mokwanira. Ndimadyanso mosamala, ndipo ndimapewa zakudya zamafuta, zakumwa ngati khofi kapena tiyi, ndi zakudya zam’chitini. Ndimayesetsanso kupewa kukwiya kapena kuda nkhawa kwambiri. Ndipo kuchita zinthu mosamala kotereku kwandithandiza. Panthawi yonse yomwe ndakhala ndikuchita upainiya wapadera, ndinakomokako kamodzi kokha.

Popeza ndine wosakwatiwa ndiponso ndilibe achibale oti ndiziwasamalira, ndine wosangalala kwambiri kupitiriza kuchita upainiya wapadera. Ndimasangalala podziwa kuti Yehova ‘sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yathu ndi chikondicho tidachionetsera ku dzina lake.’ Iye ndi wachikondi kwambiri, chifukwa safuna kuti timuchitire zinthu zomwe sitingathe. Kuzindikira mfundo yoona imeneyi kwandithandiza kuganiza bwino, chifukwa ngati matenda atadzandisiyitsanso upainiya, ndikudziwa kuti Yehova adzakhalabe wosangalala ndi utumiki wanga wochokera pansi pamtima.—Ahebri 6:10; Akolose 3:23.

Kunena zoona, kuuza anthu ena chikhulupiriro changa tsiku lililonse kumandilimbikitsa. Kumandithandizanso kuti ndisamaiwale madalitso amene Mulungu adzatipatse m’tsogolo. Lonjezo la m’Baibulo n’loti m’dziko latsopano simudzakhalanso matenda, “ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo [zidzakhala zitapita].”—Chivumbulutso 21:3, 4; Yesaya 33:24; 2 Petro 3:13.

[Zithunzi patsamba 14]

Ndili ndi zaka pafupifupi 7 (pamwambapa); ndili ndi zaka pafupifupi 16, nditangobatizidwa kumene

[Chithunzi patsamba 15]

Kulalikira ndi mnzanga