Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pa Chilankhulo Chathu Palibe Mawu Otukwana”

“Pa Chilankhulo Chathu Palibe Mawu Otukwana”

“Pa Chilankhulo Chathu Palibe Mawu Otukwana”

KODI mawu otukwana ndi otani? Ndi “mawu achipongwe, olaula, kapena opanda ulemu.” (The American Heritage Dictionary) Mtanthauzira mawu wina amamasulira mawu akuti “kutukwana” motere: “Kuchitira chipongwe, mwano, kapena kunyoza (chinthu cholemekezeka).” Koma n’zomvetsa chisoni kuti m’mayiko ochuluka, anthu ambiri amatukwana. Kale amuna ndi amene ankakonda kutukwana nthawi zambiri, koma masiku ano mochulukirachulukira tikumva akazi akutukwana. Komabe, pakati pa anthu a zikhalidwe zina, kale anthu sankatukwana. Mwachitsanzo, tamvani zomwe ananena Mmwenye wina wa mtundu wa Apache dzina lake James Kaywaykla.

James anabadwa pafupifupi mu 1873 ku New Mexico, m’dziko la United States. Kumapeto kwa moyo wake, ali ndi zaka pafupifupi 90, anafotokoza nkhani yotsatirayi:

“M’mawa wina nditadzuka ndinamva mawu a agogo anga aamuna. Anakhala m’kanyumba kopangidwa ndi udzu kapakhomo pathu akuyang’ana dzuwa likutuluka, ndipo ankaimba Nyimbo ya M’mawa. Imeneyi ndi nyimbo imene timaimbira Ussen . . . kumuthokoza chifukwa cha imodzi mwa mphatso zake zabwino kwambiri, yomwe ndi chikondi cha mwamuna ndi mkazi, chomwe chili chopatulika kwa Apache. * Apache sanena nthabwala zachipongwe ponena za kugonana, ndipo samvetsetsa chifukwa chomwe Maso Oyera [azungu] amaonera kuti kutenga mimba ndi kubereka n’zinthu zoseketsa. Kwa iwo, kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi kutchula dzina la Mulungu pachabe. Ndimanyadira kwambiri kuti pa chilankhulo chathu palibe mawu otukwana. Chifukwa chokhala ndi mwayi wotha kulenga nawo moyo watsopano, timathokoza Mlengi wa Moyo.”—Zachokera m’buku lotchedwa Native Heritage, lolembedwa ndi Arlene Hirschfelder.

Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.” Analembanso kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.”—Aefeso 4:29; 5:3, 4.

Kodi munthu angachotse bwanji kutukwana ndi nthabwala zachipongwe mu mtima mwake, m’maganizo mwake, ndi m’kamwa mwake? Malangizo amene Paulo anapatsa Afilipi angatithandize tonsefe. Iye anati: “Abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Pa chikhulupiriro cha Apache, Ussen ndiye mlengi wa moyo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

All photos: Library of Congress, Prints & Photographs Division; Apache symbol: Dover Publications, Inc.