Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Mukhalitse Pantchito

Zimene Mungachite Kuti Mukhalitse Pantchito

Zimene Mungachite Kuti Mukhalitse Pantchito

“Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu.”—Miyambo 22:29.

MONGA momwe vesi la m’Baibulo lili pamwambali likusonyezera, antchito odziwa bwino ntchito yawo amaonedwa kuti ndi ofunika kwambiri. Kodi ndi luso ndi makhalidwe ena ati amene mabwana amafuna kuti antchito awo akhale nawo? George, bwana woyang’anira antchito pa kampani inayake imene ili ndi antchito 700 anafotokozera a Galamukani! kuti: “Zimene timafuna kwambiri mwa antchito athu n’zoti azitha kulankhula bwino ndi kugwira bwino ntchito ndi anthu ena.” M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kuchita bwino zimenezi, zomwe zingakuthandizeni kukhalitsa pantchito yanu. Taonani zitsanzo zingapo.

Muzilankhula Bwino ndi Anthu Ena

Mlembi wa Baibulo Yakobo anasonyeza kuti ntchito ya munthu wolankhula bwino imayamba asanatsegule pakamwa pake. Yakobo analemba kuti munthu ayenera kukhala “wotchera khutu, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) N’chifukwa chiyani malangizo amenewa ali othandiza? Solomo analemba kuti: “Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.” (Miyambo 18:13) Zoonadi, kumvetsera mwachidwi abwana anu ndiponso antchito anzanu akamalankhula kungakuthandizeni kuti mupewe kusamvana ndi kulakwitsalakwitsa zinthu.

Mukamalankhula, m’pofunikanso kwambiri kuganizira mmene mumalankhulira. Mukamalankhula momveka bwino ndiponso mokweza bwino mawu, mwachidziwikire anthu angamvetse zimene mukunenazo ndipo angazigwiritsire ntchito. Brian, munthu wothandiza anthu kupeza ntchito amene tinamutchula mu nkhani yapita ija, anati: “Mungadabwe kuona kuti anthu ambiri amachotsedwa ntchito, osati chifukwa choti saidziwa bwino ntchitoyo, koma chifukwa choti satha kulankhula bwino ndi anthu ena.”

Muzigwirizana ndi Antchito Anzanu

Popeza mumakhala nthawi yaitali muli ndi antchito anzanu, mosakayikira mungathe kuwadziwa bwino. Chifukwa cha zimenezi mwina zingakhale zosavuta kuti muziwajeda, n’kukulitsa zolakwitsa ndi zophophonya zawo. Koma Baibulo limatilangiza kuti ‘tiyesetse kukhala chete ndi kuchita za ife eni.’ (1 Atesalonika 4:11) Mukachita zimenezi simudzakhala ndi mbiri yoti ndinu ‘wolowerera za eni.’ (1 Petro 4:15, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kuwonjezera apo, mudzapewa kuwononga nthawi ndi kukangana za zii ndi antchito anzanu.

Mukauzidwa kuti mugwire ntchito inayake, kumbukirani malangizo anzeru a Yesu akuti: “Akakukakamiza kum’perekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.” (Mateyu 5:41) Yesu anali kunena zoperekeza anthu amene ali ndi udindo m’boma, koma mfundo yomweyi imathandizanso kuntchito. Ngati muli ndi mbiri yoti ndinu wolimbikira ntchito, wokonzeka kuchita ngakhale zinthu zomwe sanakuuzeni kuti muchite, mosakayikira mudzakhalitsa pantchitopo. Koma pali zinthu zina zimene bwana wanu sayenera kukupemphani kuti muchite. Yesu anati tizipereka “kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Mfundo ya mawu a Yesuwa ndi yoti anthu audindo sayenera kuloledwa kulowerera pa nkhani zofunika kwambiri pamoyo wanu, monga kulambira Mulungu.

Muzichita Zinthu Mwachilungamo

Pa kafukufuku wina wa makampani opitirira 1,400 anapeza kuti mabwana ambiri “amaona kuti kuchita zinthu mwachilungamo ndi kukhulupirika ndi makhalidwe ofunika kwambiri kuti anthu ofunsira ntchito akhale nawo.” Mwachidziwikire, kuchita zinthu mwachilungamo kumatanthauza kuti musamabe ndalama ndi katundu wa abwana anu. Kumatanthauzanso kuti musamabe nthawi. Pa kafukufuku amene bungwe linalake lothandiza anthu kupeza ntchito linachita anapeza kuti pa avareji, wantchito aliyense ankaba maola 4 ndi mphindi 15 pa mlungu. Mwa zina, anthu oba nthawiwa ankabwera mochedwa ku ntchito nthawi zonse, ankaweruka nthawi isanakwane, ndipo ankacheza ndi antchito anzawo nthawi ya ntchito.

Baibulo limalangiza kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.” (Aefeso 4:28) Kuwonjezera apo, Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akristu kugwira ntchito mwakhama, ngakhale abwana awo atakhala kuti sakuwaona. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mverani m’zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, osati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuwopa Ambuye.” (Akolose 3:22) Ngati muli ndi mbiri yoti mumagwira bwino ntchito, ngakhale pasakhale munthu aliyense amene akukuonani, ndiye kuti ndinu wantchito wokhulupirika.

Musayembekezere Zinthu Zosatheka

Baibulo molondola linaneneratu kuti masiku athu ano adzakhala owawitsa. (2 Timoteo 3:1) Chifukwa cha zimenezo, ndale ndi zochitika za anthu zimakhala zosadalirika, zimene zimachititsa kuti nkhani zachuma zikhalenso zosadalirika. (Mateyu 24:3-8) Choncho, ngakhale mutatsatira malangizo ali pamwambawa, mukhozabe kuchotsedwa ntchito.

Komabe, kutsatira mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kuchepetsa nkhawa imene munthu amakhala nayo akakhala lova. Yesu anati: “Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.”—Mateyu 6:30-32.

Mofanana ndi anthu ambiri padziko lonse lapansi, Ericka, amene tinamutchula mu nkhani yapita uja, waona kuti mawu amenewa ndi oona. Iye anafotokoza maganizo ake motere: “Ntchito yomwe ndili nayo panopa ndimaikonda kwambiri. Koma, poona zomwe zinandichitikirapo, ndikudziwa kuti zinthu zikhoza kusintha. Ngakhale zili choncho, chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo ndi kukhulupirira Yehova, ndaphunzira momwe ndingachepetsere nkhawa ndikakhala kuti sindili pantchito ndi momwe ndingakhalire wokhutira ndi ntchito yomwe ndapeza.”

[Chithunzi patsamba 10]

Kusamvetsera pa misonkhano kungakuthetsereni ntchito