Kodi Masoka Achilengedwe Akuwonjezeka?
Kodi Masoka Achilengedwe Akuwonjezeka?
“Tiyenera kuyembekezera kuti zinthu zoopsa kwambiri zomwe zikuoneka kuti zikuchitika chifukwa cha kusintha kwa nyengo zidzakhala ndi zotsatirapo zoipa kwambiri m’tsogolomu. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kulimbana ndi mitundu yatsopano ya mavuto amene amabwera chifukwa cha kuipa kwa nyengo. Tiyeneranso kulimbana ndi kuwonongeka kwakukulu kwa katundu ndi miyoyo ya anthu. . . . Choncho tingachite bwino titakonzekereratu panopa kusintha kwakukulu kumeneko kusanafike, chifukwatu muvi woyang’anira suchedwa kulowa m’maso.” —Zachokera M’magazini Yotchedwa Topics Geo, Pa Mutu Wakuti “Kuona Zochitika Pa Chaka: Masoka Achilengedwe M’chaka Cha 2003.”
MADERA ena ku Ulaya anatentha kwambiri m’chilimwe cha mu 2003. Chifukwa cha kutentha kwambiri kumeneko, anthu pafupifupi 30,000 anafa ku Belgium, Britain, France, Italy, Netherlands, Portugal, ndi ku Spain. Ndipo anthu okwana 1,500 anafa ku Bangladesh, ku India, ndi ku Pakistan chifukwa choti kunatentha kwambiri nyengo ya mvula itangotsala pang’ono kuyamba. Ndiponso chilala ndi kutentha koopsa ku Australia kunayambitsa moto wa m’tchire umene unawononga dera lokwana mahekitala mamiliyoni atatu.
Bungwe loona za nyengo padziko lonse lotchedwa World Meteorological Organization linati, “ku madera akufupi ndi nyanja ya Atlantic, pa nyengo ya mphepo za mkuntho ya mu 2003 panachitika mphepo za mkuntho zodziwika mayina ake zokwana 16. Mphepo zimenezi ndi zambiri kuposa mphepo za mkuntho zomwe zinakhala zikuchitika chaka chilichonse pa zaka zapakati pa 1944 ndi 1996 zokwana pafupifupi 10 pachaka. Komabe, mphepo za mkunthozi zikugwirizana ndi momwe mphepo za mkuntho za m’madera otentha zakhala zikuwonjezekera kuyambira pakati pa zaka za m’ma 1990.” Mphepo za mkunthozi zinapitirizabe kuwonjezeka m’chaka cha 2004. M’chakachi, m’mayiko ozungulira nyanja ya Caribbean ndi ku Gulf of Mexico,
munachitika mphepo za mkuntho zoopsa zimene zinapha anthu pafupifupi 2,000 ndi kuwononga zinthu zambiri.Mu 2003, ku Sri Lanka kunagwa mvula yamkuntho imene inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri, ndipo anthu pafupifupi 250 anafa. Mu 2004, kumadzulo kwa nyanja ya Pacific kunachitika mphepo za mkuntho pafupifupi 23. Mphepo za mkuntho 10 mwa zimenezi zinachitika m’dziko la Japan, kumene zinawononga kwambiri katundu ndi kupha anthu oposa 170. Kummwera kwa Asia, makamaka ku Bangladesh, kunasefukira madzi chifukwa cha kuchuluka kwa mvula ndipo zimenezi zinabweretsera mavuto anthu pafupifupi 30 miliyoni. Anthu mamiliyoni ambiri nyumba zawo zinagwa, anthu pafupifupi mamiliyoni atatu anakakamizika kuthawa m’nyumba zawo, ndipo oposa 1,300 anafa.
Mu 2003 munachitika zivomezi zingapo zamphamvu. Pa May 21, ku Algiers, m’dziko la Algeria, chivomezi chinavulaza anthu 10,000 ndipo anthu 200,000 nyumba zawo zinagwa. Pa December 26, pa nthawi ya 5:26 m’mawa, m’dera lomwe lili pa mtunda wa makilomita 8 kummwera kwa mzinda wa Bam m’dziko la Iran kunachitika chivomezi choopsa. Chivomezi chokwana 6.5 pa sikelo yoyezera mphamvu ya zivomezi chimenecho chinawononga pafupifupi mzinda wonsewo. Chinaphanso anthu 40,000, ndipo anthu oposa 100,000 nyumba zawo zinagwa. Chivomezicho chinali tsoka limene linapha anthu ambiri m’chaka chimenecho. Chinawononganso mbali yaikulu ya nyumba yotchuka ya mumzindawo yomwe inamangidwa zaka 2,000 zapitazo, yotchedwa Arg-e-Bam. Zimenezi zinachititsa kuti deralo lisiye kupeza ndalama zomwe zinkachokera kwa anthu odzaona nyumbayo.
Patatha chaka chimodzi chenicheni, chivomezi cha mphamvu zokwana 9.0 chinachitika panyanja chakumadzulo kwa gombe la kumpoto kwa chilumba cha Sumatra m’dziko la Indonesia. Chivomezichi chinayambitsa mafunde aakulu kwambiri, kapena kuti matsunami oopsa kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Mafunde akuluakulu oopsawo anapha anthu oposa 200,000 ndipo anavulaza anthu ambiri ndi kuwononga nyumba zambiri. Matsunami akuphawo anafika mpaka ku gombe lakummawa kwa Africa, pa mtunda wa makilomita oposa 4,500 kumadzulo kwa malo omwe kunachitika chivomezicho.
Kodi Tiyembekezere Masoka Oopsa Kwambiri?
Kodi masoka omwe akhala akuchitikawa akutisonyeza zinthu zomwe zichitike m’tsogolomu? Ponena za masoka ochitika chifukwa cha nyengo, asayansi ambiri akukhulupirira kuti kusintha kwa mpweya wa m’mlengalenga chifukwa cha zochita za anthu kukusintha nyengo ya dzikoli ndipo kukubweretsa nyengo yoipa kwambiri. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti m’tsogolo muno zinthu sizikhala bwino. Kuwonjezera pa vutoli, anthu ambiri masiku ano akukhala m’madera momwe mumachitikachitika masoka. Akukhala m’maderawa chifukwa chofuna, kapena chifukwa choti kulibenso kwina komwe angakhale.
Kafukufuku wasonyeza kuti anthu ambiri amene amafa chifukwa cha masoka amakhala m’mayiko osauka. M’mayiko olemera anthu safa kwambiri koma katundu wa ndalama zambiri amawonongeka. Anthu ena omwe ali ndi makampani a inshuwalansi akuda nkhawa kuti mwina makampani awo angagwe chifukwa choti zinthu zowonongeka zomwe akufunika kulipira zikungochulukirachulukira.
Mu nkhani yotsatirayi, tiona zinthu zina zachilengedwe zomwe zimayambitsa masoka, ndi zinthu zina zomwe anthu akuchita zomwe zikuwonjezera mavutowa. Tionanso ngati anthu ali ndi mphamvu ndi mtima wofuna kusintha zochita zawo kuti dzikoli likhale malo otetezeka oti mibadwo yomwe ikubwera m’tsogolomu idzakhalepo.
[Chithunzi patsamba 19]
FRANCE 2003 Kutentha kwambiri m’chilimwe ku Ulaya kunaphetsa anthu 30,000; ku Spain kunatentha mpaka kufika pa 44.8°C.
[Mawu a Chithunzi]
Alfred/EPA/Sipa Press
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
IRAN 2003 Chivomezi cha ku Bam chinapha anthu 40,000; azimayi akulira maliro azibale awo pa manda oikamo anthu ambiri
[Mawu a Chithunzi]
Background and women: © Tim Dirven/Panos Pictures