Kodi Nyenyezi Zingakuthandizeni Kudziwa Tsogolo Lanu?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Nyenyezi Zingakuthandizeni Kudziwa Tsogolo Lanu?
KODI mungatani kuti moyo wanu ukhale wabwinopo ndiponso kuti zinthu zizikuyenderani bwino pankhani ya chikondi ndi ndalama? Anthu ambiri amadalira nyenyezi kuti ziwathandize kudziwa zam’tsogolo. Tsiku lililonse anthu ambiri amawerenga zomwe openda nyenyezi amalemba m’manyuzipepala pokhulupirira kuti zingawathandize. Ngakhale atsogoleri a mayiko ena akuti asanachite zinthu zina amayamba aona zomwe zizindikiro zawo za nyenyezi zikunena.
Kodi tingadaliredi zimene openda nyenyezi amanena? Kodi openda nyenyeziwo amadziwa bwanji za m’tsogolo? Kodi Akristu ayenera kutsatira zomwe nyenyezi zikunena pochita zinthu pamoyo wawo?
Kodi Amapenda Bwanji Nyenyezizo?
Malinga ndi buku la The World Book Encyclopedia, kupenda nyenyezi “kwagona pa chikhulupiriro choti nyenyezi zimayenda m’njira imene ingasonyeze khalidwe la munthu kapena tsogolo lake.” Openda nyenyezi amati mmene nyenyezi zakhalira panthawi imene munthu akubadwa zingakhudze moyo wake wonse wa munthuyo.
Kukhulupirira nyenyezi kunayamba kalekale. Zaka pafupifupi 4,000 zapitazo, Ababulo anayamba kuneneratu za m’tsogolo poona momwe dzuwa, mwezi, ndi mapulaneti asanu amene amaoneka bwino kwambiri kumwamba akhalira. Iwo ankati nyenyezi zimenezi zili ndi mphamvu inayake imene imakhudza khalidwe la munthu. Kenaka anayamba kumagwiritsa ntchito zizindikiro za nyenyezi poneneratu za m’tsogolo.
Zinayamba Kalekale Kulephera
Baibulo limasonyeza kuti mu mzinda wa Babulo munali anthu openda nyenyezi, ndipo nthawi zingapo limatchula za openda nyenyezi a ku Babulo. (Danieli 4:7; 5:7, 11) Pa nthawi ya mneneri Danieli, kupenda nyenyezi kunali kofala kwambiri m’dziko la Kasidi (madera ozungulira mzinda wa Babulo) moti kunena kuti “Akasidi” kunali ngati kunena kuti openda nyenyezi.
Danieli anaona momwe kupenda nyenyezi kunafalira ku Babulo komanso momwe openda nyenyezi kumeneko analepherera kuneneratu za kugwa kwa mzindawo. (Danieli 2:27) Taonani zomwe mneneri Yesaya ananeneratu molondola zaka 200 zinthuzo zisanachitike. Iye analemba monyogodola kuti: “Aimirire tsopano openda zam’mwamba, oyang’ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera. . . . Sadzadzipulumutsa okha.”—Yesaya 47:13, 14.
Zikuoneka kuti openda nyenyezi a ku Babulo analephera kuneneratu kuti mzinda wawo ugwa ngakhale kutangotsala maola ochepa kuti zimenezi zichitike. Ndipo pamene chiweruzo cha Mulungu chinaoneka pa khoma la nyumba ya Mfumu Belisazara, openda nyenyeziwo analephera kumasulira malembo achilendowo.—Danieli 5:7, 8.
Masiku ano, openda nyenyezi amalepheranso chimodzimodzi akamaneneratu zochitika zikuluzikulu. Asayansi awiri ochita kafukufuku, omwe ndi R. Culver ndi Philip Ianna, atafufuza zinthu zimene openda nyenyezi ananeneratu zokwana 3,000, anapeza kuti ndi zochitika 300 zokha zomwe zinachitikadi ngati momwe ananeneramo. Komatu katswiri aliyense wodziwa ntchito yake, yemwe amaneneratu za m’tsogolo mwa kungoonetsetsa mmene zinthu zikuyendera panopa, akhoza kuneneratu molondola kuposa pamenepo.
N’zosemphana ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Si kuti aneneri achihebri ankatsutsa kupenda nyenyezi pa chifukwa chokha chakuti nthawi zambiri opendawo ankalephera kunena molondola zomwe zidzachitike m’tsogolo ayi. Koma lamulo limene Mulungu anapatsa Mose linaletseratu Aisrayeli kuti asamaombeze. Lamulolo linati: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo [woombeza maula, NW], . . . kapena wanyanga. . . . Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10, 12.
Ngakhale kuti lemba limenelo silichita kutchuliratu kupenda nyenyezi, n’zoonekeratu kuti lamulolo linaletsanso zimenezo. Buku la Encyclopædia Britannica limati kupenda nyenyezi ndi “mtundu wa kuombeza umene umaphatikizapo kuneneratu zochitika za m’tsogolo za padziko lapansi ndi za anthu mwa kupenda ndi kumasulira nyenyezi, Dzuwa, Mwezi, ndi mapulaneti.” Kuombeza kwa mtundu uliwonse, kaya kukhale kogwiritsa ntchito nyenyezi kapena zinthu zina, n’kuphwanya malamulo a Mulungu. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa zabwino.
M’malo monena kuti timapambana kapena kulephera pa zochita zathu chifukwa cha nyenyezi, Baibulo limanena momveka bwino kuti, “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Popeza tili ndi ufulu wochita zomwe tikufuna, aliyense wa ife ayenera kuyankha kwa Mulungu pa zimene amachita. (Deuteronomo 30:19, 20; Aroma 14:12) N’zoona kuti tikhoza kuchita ngozi kapena kudwala chifukwa cha zinthu zomwe sitikanatha kuziletsa. Koma Malemba amafotokoza kuti masoka oterowo amabwera chifukwa cha ‘zotigwera m’nthawi mwake,’ osati chifukwa cha nyenyezi.—Mlaliki 9:11.
Pa nkhani ya maubwenzi athu ndi anthu ena, Baibulo limatilimbikitsa kuti tivale makhalidwe monga chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, kuleza mtima, ndi chikondi. (Akolose 3:12-14) Makhalidwe amenewa ndi amene ali ofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi anzake okhalitsa ndi ukwati wolimba. Kusankha wokwatirana naye pogwiritsa ntchito zizindikiro za nyenyezi n’kosathandiza. Katswiri wina wa zamaganizo, dzina lake Bernard Silverman, anafufuza zizindikiro za nyenyezi za mabanja 3,500. Mwa mabanja amenewo, mabanja 595 pambuyo pake anatha. Komano pakafukufuku wakeyo, anapeza kuti anthu amene anakwatirana chifukwa chokhala ndi zizindikiro za nyenyezi zogwirizana, mabanja awo anali kutha mofanana ndi mabanja omwe zizindikiro zawo zinali zosagwirizana.
N’zachionekere kuti kupenda nyenyezi n’kosadalirika ndiponso n’kosocheretsa. Kungatichititse kuti tiziimba mlandu nyenyezi mmalo modziimba mlandu tokha tikalakwitsa zinthu. Koposa zonse, Mawu a Mulungu amaletseratu mosapita m’mbali kuchita zimenezi.