Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Mwamantha

Kukhala Mwamantha

Kukhala Mwamantha

ROXANA * akuchita mantha kuti auze mwamuna wake kuti akufuna kuyamba kugwira ntchito ya maola ochepa patsiku. Panthawi ina pamene anapempha mwamuna wakeyo kuti amupatse ndalama zokwerera basi kuti akaone amayi ake, anamumenya kwambiri moti mpaka anapita kuchipatala. Roxana amakhala mwamantha nthawi zonse.

Rolando kale ankalola mkazi wake kubwerera kunyumba usiku pa basi, koma masiku ano amakamutenga pa galimoto. M’dera mwawomo mwachitika zinthu zachiwawa zambiri moti amaopa kuti mkazi wakeyo akhoza kuvulazidwa.

Haidé amagwira ntchito pakatikati pa mzinda waukulu wa m’dziko lawo. Tsiku lina akupita kunyumba, anakumana ndi gulu la anthu ochita chionetsero, amene kenaka anayamba kuchita zachiwawa. Masiku ano, nthawi iliyonse akamva anthu ochita zionetsero akudutsa, amachita mantha. Iye anati: “Ndimaopa kuti akhoza kundivulaza. Sindikufunanso kumagwira ntchito kunoko. Koma kulibenso kwina komwe ndingagwireko ntchito.”

Roxana, Rolando, ndi Haidé amakhala mwamantha, ndipo amatero osati pakangogwa zinthu zadzidzidzi. Iwo amakhala mwamantha nthawi zonse. Anthu akamakhala mwamantha, amamva kuti alibenso mphamvu zilizonse. Mantha angawachititse kuti asamasangalale chifukwa angamalephere kuchita zinthu zimene akufuna kuchita. Mantha angachititse munthu kumangoganizira zinthu zomwe amaopazo ndipo angamulepheretse kuika maganizo ake pa zinthu zina.

Kukhala mwamantha kumachititsa munthu kukhala wopanikizika kwambiri m’maganizo. Nthawi zambiri kumayambitsa matenda a maganizo ndipo kungawononge thanzi la munthu. Magazini ina yonena za thanzi inati: “Kukhala wopanikizika m’maganizo kumafooketsa mphamvu yoteteza thupi ku matenda ndipo kumayambitsa matenda ambiri. Thupi limayamba kukhala ndi zizindikiro zoti likuwonongeka, makamaka ziwalo zimene zikukhudzidwa. Matenda monga matenda a BP, matenda a mtima, a impso, a m’mimba, zilonda za m’mimba, mutu, kusowa tulo, kuvutika maganizo, ndi nkhawa zikhoza kuyamba. Munthu akakhala nthawi yaitali ali wopanikizika maganizo amakhala wotopa kwambiri.”

Masiku ano si zachilendo kuona anthu akukhala mwamantha. Kodi idzafika nthawi imene anthu azidzakhala mopanda mantha padziko pano?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.