Kuyesera Kudyetsa Anthu Wani Biliyoni
Kuyesera Kudyetsa Anthu Wani Biliyoni
TSIKU lililonse, anthu wani biliyoni amadya chakudya chosakwanira moti sakhuta. Komabe, zinthu zoipa zimenezi siziyenera kuchitika, malinga ndi zomwe linanena bungwe la United Nations.
“Mwanena kuti cholinga chanu choyamba ndicho kuthetsa umphawi wadzaoneni.” Mawu amenewa ananena ndi Kofi Annan, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations pa September 8, 2000, pa msonkhano wa atsogoleri amphamvu kwambiri padziko lonse lapansi. Anali atakumana pa msonkhano wotchedwa United Nations Millennium Summit, ndipo pamsonkhanowu anthu angapo ananena mwatchutchutchu za mavuto amene anthu osauka padziko lapansi akukumana nawo. Wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko la Brazil anati: “Umphawi wadzaoneni n’chinthu choti ifeyo tiyenera kuchita nacho manyazi.” Nduna yaikulu ya dziko la Great Britain inanena zoposa pamenepa pamene inati: “Mayiko olemera alephereratu kuthandiza anthu a ku Africa ndipo zimenezi n’zochititsa manyazi kwambiri kwa anthu amene timadziona ngati otukukafe.”
Atsogoleri awiriwa ananena mosapita m’mbali kuti mayiko ayenera kuchita manyazi chifukwa cholephera kuchitapo kanthu kuti adyetse anthu amene akufa ndi njala. Monga umboni woti anali kufunitsitsadi kuthandiza anthu onse ovutika padziko lapansi, anthu amene anabwera pamsonkhanowo analonjeza kuti adzachitapo kanthu ndipo analemba chikalata chokhala ndi mfundo eyiti zomwe analonjeza kuti adzakwanitsa. Zina mwa mfundozo zinali zoti: “Tidzachita zonse zomwe tingathe kuti tilanditse amuna, amayi ndi ana, ku mavuto oopsa kwambiri obwera chifukwa cha umphawi wadzaoneni, umene ukuvutitsa anthu opitirira wani biliyoni panopa. . . . Tikulonjezanso kuti: Podzafika chaka cha 2015, tidzachepetsa ndi theka chiwerengero cha anthu apadziko lapansi amene amapeza ndalama zosakwana dola imodzi patsiku ndi chiwerengero cha anthu amene akuvutika ndi njala.”
Kodi kuyambira mu September 2000, pachitika zotani pokwaniritsa zolinga zapamwamba zimenezo?
Alonjeza Zambiri Koma Osachitapo Kanthu
Mu 2003, bungwe lotchedwa Global Governance Initiative of the World Economic Forum linayamba kuona zomwe zachitika pofuna kukwaniritsa zolinga zimene zinalembedwa m’chikalata cha Millennium Declaration pa msonkhano wa bungwe la United Nations uja. Chikalata chimene bungweli linatulutsa pa January 15, 2004, chinati: “Pa malonjezo ake onse ofunika kwambiri, dziko likulephereratu kuchitapo kanthu kuti likwanitse malonjezowo.” Ponena za njala, chikalatacho chinati: “Vuto limene lilipo si kuchepa kwa zakudya padziko pano.
Zakudya zilipo zoti zikhoza kukwanira aliyense. Koma vuto n’loti chakudya chomwe chilipo sichifika kwa anthu amene alibe ndalama.”Pa vuto la umphawi, chikalatacho chinati: “Maboma, olemera ndi osauka omwe, ndi amene achititsa kuti pasachitike chilichonse mpaka pano. Koma ndondomeko yoyendetsera ndalama padziko lonse yokonzedwa ndi anthu olemera nthawi zambiri imaipira anthu osauka kwambiri. Mayiko olemera, ngakhale kuti akhala akunena zambiri, alibe chidwi chokwanira chofuna kusintha ndondomeko imeneyo kapena chofuna kuwonjezera ndalama zimene amathandizira anthu osauka kwambiri.” Ngakhale kuti adzudzulidwa chonchi, anthu andalewo akupitirizabe kukambirana m’malo mochitapo kanthu, ndipo maboma osiyanasiyana akupitirizabe kuyendetsa zinthu n’cholinga choti ziwakomere. Pamene akuchita zimenezi, anthu osauka akupitirizabe kugona ndi njala.
Chikalata chochokera ku bungwe lotchedwa World Economic Forum lija, cha mutu wakuti: “M’pofunika Kuchitapo Kanthu, Osamangolakalaka,” chinachenjeza kuti “anthu ambiri padziko lapansi adzavutika ndi njala yowonjezereka pokhapokha ngati malamulo a malonda a padziko lonse atasinthidwa. M’pofunikanso kuti mayiko azilimbikitsa kuchepetsa njala, ndiponso anthu awonjezere zomwe amachita kuti adzithandize okha.” Ndipo kodi ndani amene akufunika kukhazikitsa malamulo abwino ndi kuthandiza anthu kuti “awonjezere zomwe amachita kuti adzithandize okha”? Ndi maboma omwewo amene m’chaka cha 2000 analengeza kuti akufunitsitsa kuchepetsa mavuto a anthu onse.
Munthu akaphwanya lonjezo limodzi anthu amakhumudwa, koma akaphwanya malonjezo angapo anthu amasiya kumukhulupirira. Chifukwa choti maboma a padziko lapansi sanakwaniritse lonjezo lawo loti adzasamalira anthu osauka, anthu asiya kuwakhulupirira. Mayi wina yemwe ali ndi ana asanu amene amakhala m’dziko linalake losauka, kufupi ndi nyanja ya Caribbean, amangotha kudyetsa banja lake kamodzi kokha patsiku. Iye anati: “Ndimangoda nkhawa n’zoti kaya lero tidya kapena ayi. Sindida nkhawa n’zoti ndani amene akulamulira panopa. Palibe wolamulira aliyense amene anatithandizapo.”
Yeremiya, wolemba Baibulo, anati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kulephera kwa maboma a anthu kuthetsa mavuto a anthu osauka kukutsimikizira kuti mfundo ya m’Baibulo imeneyi ndi yoona.
Koma alipo Mtsogoleri wamphamvu ndiponso wofunitsitsa kuthetsa mavuto a anthu, ndipo Baibulo limatiuza kuti mtsogoleri ameneyu ndi ndani. Mtsogoleriyu akadzayamba kuchitapo kanthu, palibenso amene adzakhale ndi njala.
Zinthu Zopatsa Chiyembekezo
“Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chawo m’nyengo zawo.” (Salmo 145:15) Kodi Ameneyu ndani, amene amafuna kuti munthu aliyense akhale ndi chakudya? Ndi Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Ngakhale kuti anthu avutika ndi njala ndi mavuto ena kwa zaka zambiri, Yehova nthawi zonse wakhala ndi chidwi chofuna kuthandiza anthu. Iye waona momwe maboma a anthu alepherera, ndipo Baibulo, lomwe ndi Mawu ake omwe sanama, limasonyeza kuti posachedwapa adzawachotsa n’kukhazikitsa boma lake.
Yehova anati: “Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” (Salmo 2:6) Chilengezo chimenechi n’chopatsa chiyembekezo chifukwa n’chochokera kwa amene ali ndi mphamvu yaikulu m’chilengedwe chonse. Ngakhale kuti anthu olamulira nthawi zambiri alephera kuthandiza anthu awo, Yesu Kristu, monga Mfumu yokhazikitsidwa ndi Mulungu, adzathandiza anthu osauka kwambiri padziko lapansi m’njira yomwe sanaionepo.
Kudzera mwa Mfumu imeneyi, Yehova adzadyetsa anthu onse anjala. Lemba la Yesaya 25:6 limati: “Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona.” Mu Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu, anthu sadzasowanso chakudya chabwino, kaya akhale kuti akukhala kuti. Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.”—Salmo 145:16.
[Mawu Otsindika patsamba 15]
“Mayiko olemera alephereratu kuthandiza anthu a ku Africa ndipo zimenezi n’zochititsa manyazi kwambiri kwa anthu amene timadziona ngati otukukafe.” —Anatero Tony Blair, Nduna Yaikulu ya dziko la Britain
[Chithunzi patsamba 14]
ETHIOPIA: M’dziko limeneli, anthu pafupifupi 13 miliyoni amadalira chakudya chochita kupatsidwa. Mwana ali pamwambayo ndi mmodzi mwa iwo
[Chithunzi patsamba 14]
INDIA: Ana a sukuluwa amalandira chakudya ku sukulu
[Mawu a Chithunzi patsamba 14]
Top: © Sven Torfinn/Panos Pictures; bottom: © Sean Sprague/Panos Pictures