Mmene Mungakhalire Bwenzi la Mulungu
Mmene Mungakhalire Bwenzi la Mulungu
▪ Zimenezo n’zimene kabuku ka masamba 32 kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! kamatiphunzitsa. Mitu ina yosangalatsa m’kabukuka ndi monga yakuti “Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake” ndi “Mulungu Ndiye Bwenzi Labwino Koposa, Limene Mungakhale Nalo.” Kabukuka anakalemba m’njira yoti kathandize munthu amene akuwerengayo kudziwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo.
M’mutu wakuti “Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso,” kabukuka kamafotokoza momveka bwino cholinga cha Mulungu cha dziko lathu lino. Komabe, kuti tidzasangalale ndi Paradaiso amene Baibulo likulonjeza, tiyenera kudziwa kuti kodi Mulungu amafuna tizimutumikira bwanji. Mitu ngati yakuti “Mmene Mungapezere Chipembedzo Choona” ndi “Kanani Chipembedzo Chonyenga!” idzakuthandizani kuti mukhale bwenzi la Mulungu ndiponso kuti Mulunguyo azisangalatsidwa nanu. Tikukhulupirira kuti mupindula kwambiri mukawerenga kabuku kameneka.
Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.