Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndimacheza ndi Anthu Olakwika?

N’chifukwa Chiyani Ndimacheza ndi Anthu Olakwika?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

N’chifukwa Chiyani Ndimacheza ndi Anthu Olakwika?

“Ndinkadziwa kuti sibwino kuti ndizolowerane naye kwambiri, koma sindinadziletse. Ndinaona ngati kutulo kuti mnyamata angafune kumacheza nane.”—Anatero Nancy. *

“Ndinkapita kokasewera pa chipale chofewa ndekha, ndipo pasanapite nthawi yaitali ndinayamba kucheza ndi anzanga amene ndinadziwana nawo kumeneko. Kenaka ndinayamba kuchita zachiwerewere.”—Anatero Dan.

DAN ndi Nancy anali olimba mwauzimu poyamba. Nancy anakulira m’banja loopa Mulungu ndipo anayamba kuuza anthu ena za chikhulupiriro chake ali ndi zaka nayini. Dan anayamba utumiki wa nthawi zonse asanakwanitse zaka 20. Koma awiri onsewa anakumana ndi mavuto auzimu aakulu pamoyo wawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa ankacheza ndi anthu olakwika.

Kodi zinakuchitikiranipo kuti mwadzidzidzi munayamba kufuna kumacheza ndi munthu amene pansi pa mtima munkadziwa kuti angakubweretsereni mavuto? N’kutheka kuti munthuyo anali mnzanu wa ku sukulu amene ankakonda zinthu zomwe inunso mumakonda, kapena anali mnyamata kapena mtsikana amene munkafuna mutakhala naye pa chibwenzi.

Mosakayikira munakumbukira malangizo a m’Baibulo oti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Koma kodi anthu onse amene salambira Yehova ndi mayanjano oipa? Bwanji ngati ali ndi makhalidwe ena abwino, ngakhale osiririka kumene? Nanga bwanji munthu amene ali wokhulupirira mnzanu koma akupereka chitsanzo choipa mwauzimu? Tisanayankhe mafunso amenewa, tiyeni tione zifukwa zimene zingakuchititseni kuti mufune kucheza ndi anthu otero, ndi momwe zimenezi zingachitikire.

Kodi N’chiyani Chimachititsa Munthu Kucheza ndi Anthu Olakwika?

Popeza anthu onse anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, tingayembekezere kuti anthu ena amene sadziwa Yehova angakhale ndi khalidwe labwino. Chifukwa cha zimenezi, mungaone kuti anthu ena amakhala olemekezeka, ngakhale osangalatsa kucheza nawo kumene, ngakhale kuti salambira Mulungu woona. Kodi anthu oterowo mumafunika kuwapeweratu chifukwa choti sadziwa zinthu zoona za m’Baibulo? Ayi. Pamene Baibulo limatilimbikitsa kuti “tichitire onse chokoma,” zimenezi zikuphatikizapo anthu amene amakhulupirira zinthu zosiyana ndi zimene inuyo monga Mkristu mumakhulupirira. (Agalatiya 6:10) Choncho zoti muzisamala posankha anthu ocheza nawo sizitanthauza kuti muzichita zinthu ngati kuti inuyo ndinu apamwamba kuposa ena. (Miyambo 8:13; Agalatiya 6:3) Khalidwe loterolo lingachititse kuti ena asakopeke ndi zikhulupiriro zanu zachikristu.

Koma Akristu ena achinyamata amakhala aubwenzi monkitsa m’malo mongokhala ochezeka chabe. Iwo amakhala anzawo apamtima a anthu amene ali ndi chidwi chochepa ndi zinthu zauzimu kapena alibe nazo chidwi n’komwe. Dan, amene tinamutchula kale uja, anakhala katswiri pa masewera a pa chipale chofewa. Anthu amene ankacheza nawo nthawi zambiri kumalo kumene ankasewerera sanali Akristu. Pomalizira pake, Dan pamodzi ndi anthu amene ankawaona ngati anzake atsopanowo anayamba kuchita zachiwerewere ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo osiyanasiyana. Ataona kuti moyo umene amakhala sunalinso wogwirizana ndi Chikristu, Dan anasiya utumiki wake ndipo anasiyanso kupita ku misonkhano ya mpingo. Zinamutengera zaka zingapo kuti athe kusintha n’kubwereranso ku chipembedzo choona.

Melanie anayamba kucheza ndi wokhulupirira mnzake amene sanali kuchita bwino mwauzimu. Melanie anafotokoza kuti: “Ndinamva zoti mtsikanayo ankafunika kumulimbikitsa, choncho ndinayamba kucheza naye.” N’zoona kuti Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti ‘achirikize ofooka.’ (1 Atesalonika 5:14) Koma Melanie anayamba kupitira limodzi ndi mnzake watsopanoyo ku malo omwera mowa, ndipo anzawo ena amene anakumana nawo kumeneko anawachititsa kuti ayambe khalidwe loipa.

Zimene Mungayambe Kuchita Chifukwa cha Zochitika za M’banja Mwanu

Zochitika m’banja mwanu zingakuchititseni kuyamba kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Michelle ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani amakonda kukopeka ndi anyamata amene sankamukonda ndiponso sankamusamala. Iye pomalizira pake anazindikira kuti anyamatawo ankamukumbutsa bambo ake, amene sankagwirizana nawo ndipo sankapeza nthawi yocheza naye. Iye akukhulupirira kuti chifukwa choti nthawi zonse ankafunitsitsa kuti bambo ake azicheza naye koma iwo sankapezeka, mosadziwa anayamba kukopeka ndi anthu a khalidwe lofanana ndi la bambo akewo.

Mosiyana ndi zimenezi, mnyamata kapena mtsikana amene analeredwa ndi makolo achikristu akhoza kufuna kudziwa momwe anthu ena amakhalira, ndipo angamaone ngati makolo ake amamuletsa zambiri. Kaya munthu akhale ndi maganizo amenewo kapena ayi, kodi n’chinthu chanzeru kusamvera makolo n’kumacheza ndi ‘mabwenzi a dziko lapansi’? (Yakobo 4:4) Taganizirani zomwe zinachitikira Bill.

Ngakhale kuti kuyambira ali mwana anaphunzitsidwa Malemba ndi mayi ake, Bill sanadzipereke kwa Yehova, poganiza kuti kuchita zimenezo kudzamuchepetsera ufulu wake. Pofuna kudziwa payekha momwe moyo wa anthu amene si Akristu oona umakhalira, anayamba kucheza ndi gulu la zigawenga lomwe linamuchititsa kuyamba kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, chiwawa, ndi umbanda. Panthawi inayake anayendetsa galimoto mothamanga kwambiri pothawa apolisi, ndipo anachita ngozi n’kuvulala. Anakhala miyezi yambiri ali chikomokere. Madokotala ankakhulupirira kuti amwalira. Koma n’zosangalatsa kuti Bill anachira. Koma tsopano ndi wakhungu ndiponso wolumala. Anamva nkhwanga ili m’mutu ndipo tsopano ndi Mkristu wodzipereka. Koma Bill wazindikiranso kuti kumva nkhwangwa ili m’mutu kukhoza kukhala ndi zotsatirapo zoipa, zomwe zingakupweteke moyo wako wonse.

Zinanso Zimene Zimachititsa

Nthawi zina wachinyamata angaganize kuti mnzake wabwino ayenera kukhala wochita zinthu zakutizakuti potengera zomwe asangalatsi amaonetsa pa TV, m’mafilimu ndi m’mabuku. Mwachitsanzo si zachilendo kuti mabuku, mapulogalamu a pa TV, mafilimu, ndi mavidiyo a nyimbo azionetsa munthu amene amaoneka wankhanza kapena wosaganizira ena poyamba koma amene kenaka amadzasintha n’kukhala wokoma mtima ndi wachifundo. Choncho zimaoneka ngati kuti anthu amene amaoneka ngati ankhanza ndi odzikonda, kwenikweni amakhala anthu achifundo ndi osamala ena. Kuwonjezera apo, amasonyeza kuti ngati munthuyo ali mwamuna, kupeza mnzake wamkazi, kapena ngati ali mkazi, kupeza mnzake wamwamuna nthawi zambiri n’kumene kungamuthandize kuti ayambe kusonyeza makhalidwe abwinowa. N’zoona kuti anthu amafuna kugula mabuku kapena mafilimu okamba nkhani ngati zimenezi. Koma kodi mukuganiza kuti ndi nthawi zingati pamene nkhani zachikondi zoterezi zimachitikadi? N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ena anakhulupirira nkhani zimenezi zoti sizichitikadi, ndipo anayamba kucheza ndi anthu olakwika, ngakhale kumanga nawo mabanja kumene. Anthuwo anali odzikonda ndiponso achiwawa koma achinyamatawo ankayembekezera kuti adzasintha n’kukhala achifundo ndiponso osamala, koma sanasinthe.

Taganiziraninso chifukwa china chomwe anthu amayambira kucheza ndi anthu olakwika. Amaona kuti anthu ena sangawakonde, choncho amalola chibwenzi munthu aliyense amene akuoneka kuti wakopeka nawo. Nancy, amene tinamutchula kale uja, ankadziwa zomwe Baibulo limanena zoti ayenera kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Koma kuyambira kale ankadziona kuti ndi wosakongola, choncho anasangalala kwambiri pamene mwamuna wina wa ku ntchito kwawo, amene anali wa chipembedzo chosiyana ndi chake, anayamba kusonyeza kuti akumufuna. Anachita naye chibwenzi ndipo anangotsala pang’onong’ono kuti achite chiwerewere.

Monga momwe zochitika zomwe tafotokozazi zikusonyezera, pali zifukwa zambiri zimene zingachititse Mkristu wachinyamata kufuna kucheza ndi anthu olakwika. Zikuonekanso kuti pali zifukwa zambiri zomwe munthu angadzikhululukire nazo poyamba kucheza ndi anthu oterowo. Komabe, maubwenzi oterowo nthawi zonse amabweretsera munthu mavuto aakulu. Chifukwa chiyani?

Anzanu Akhoza Kukusinthani

Zoona zake n’zakuti, munthu amayamba kufanana zochita ndi anthu amene amacheza nawo. Pachifukwa chimenechi, anthu amene timacheza nawo amakhala ndi mphamvu yaikulu yotha kusintha khalidwe lathu. Lemba la Miyambo 13:20 limasonyeza kuti anzathu akhoza kutisintha kuti tikhale anthu abwino kapena oipa. Lembali limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” Anthu amene ali mabwenzi okondana kwambiri, monga momwe amachitira anthu amene akwera galimoto imodzi, mosachita kufunsa amalowera kumodzi ndipo amakafika ku malo amodzi. Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi njira imene mnzangayu watenga ikupita kumene ineyo ndikufuna kupita? Kodi indifikitsa kufupi ndi zolinga zanga zauzimu?’

N’zoona kuti kudziona monga momwe tililidi kukhoza kukhala kovuta, chifukwa mtima wathu ukhoza kutiuza zina. Koma kodi kungotsatira zomwe mukumva mumtima mwanu ndi njira yodalirika yosankhira anzanu? Anthu ambiri masiku ano amaona kuti ndi bwino kuchita zimene inuyo panokha mukuona kuti n’zabwino. Koma lemba la Miyambo 28:26 limati: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa.” N’chifukwa chiyani limatero? Chifukwa choti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9; Numeri 15:39) Kukhala wonyenga kumatanthauza kukhala wosakhulupirika kapena wachiphamaso kapenanso kukhala mthirakuwiri. Kodi mungakhulupirire munthu amene amadziwika kuti ndi wachinyengo ndiponso wosakhulupirika? Mtima wathu wophiphiritsira ukhoza kukhala wonyenga. Choncho ngati tikuona kuti ubwenzi wathu ndi munthu winawake ukuoneka kuti ndi wabwino sizitanthauza kuti ndi wabwinodi.

Mawu a Mulungu ndi odalirika kwambiri kuposa mtima wathu ndipo akhoza kutitsogolera. Mosiyana ndi mtima wanu wopanda ungwiro, mfundo za m’Baibulo sizingakukhumudwitseni kapena kukugwiritsani fuwa lamoto. Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji kudziwa ngati munthu winawake angakhale mnzanu wabwino? Ndipo kodi mungatani kuti mupewe kusankha molakwika munthu amene adzakhale mnzanu wa moyo wanu wonse, mkazi kapena mwamuna woti mukwatirane naye? Mafunso amenewa adzayankhidwa mu nkhani ya m’tsogolo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 12]

Mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV angatilepheretse kudziwa bwino munthu amene angakhale mnzathu wabwino