Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinakopeka ndi Mlengi Chifukwa cha Kukongola kwa Choonadi

Ndinakopeka ndi Mlengi Chifukwa cha Kukongola kwa Choonadi

Ndinakopeka ndi Mlengi Chifukwa cha Kukongola kwa Choonadi

YOSIMBIDWA NDI TSUYOSHI FUJII

ZAKA zingapo zapitazo ndinapatsidwa mwayi wapadera kwambiri. Anandipempha kuti ndikaike maluwa m’chipinda chokongola kwambiri cha m’nyumba ya mfumu yaikulu ya ku Japan, imene ili ku Tokyo. Panthawiyi, ndinali wothandizira wa Senei Ikenobo, yemwe anali mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya kaikidwe ka maluwa yotchedwa Ikenobo. Pamene tinali kugwira ntchitoyo, chitetezo chinali chokhwima kwambiri. Mtima uli pha pha pha, ndinayesetsa kuti ndisadonthetsere pansi ngakhale kadontho kamodzi ka madzi. Imeneyi inali nthawi imodzi imene ndinasangalala kwambiri pa ntchito yanga ya kaikidwe ka maluwa. Tsopano ndikufuna ndifotokoze momwe ndinayambira ntchito imeneyi.

Ndinabadwa mu 1948 mu mzinda wa Nishiwaki, womwe uli kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Kobe, ku Japan. Kuyambira ndili mwana, ndinkakhudzidwa mtima kwambiri ndi momwe maluwa ankaonekera okongola nyengo zinayi zikamasinthasintha. Koma sindinaganizepo zoti kunja kuno kuli Mlengi chifukwa ndinaleredwa ndi agogo anga aakazi omwe anali odzipereka kwambiri pa chipembedzo cha Chibuda.

Mayi anga ankaphunzitsa ikebana, kapena kuti kaikidwe ka maluwa, kumudzi kwathu, ndipo mpaka pano akuphunzitsabe. Ku Japan, ikebana, yomwe imadziwikanso kuti kado, (kutanthauza kaikidwe ka maluwa), ndi ntchito yolemekezeka kwambiri. Ngakhale kuti mayi anga sanandiphunzitse mwachindunji luso limeneli, anandithandiza kwambiri kuti ndizilikonda. Nthawi yoti ndisankhe chomwe ndidzachite pamoyo wanga itafika, ndinafuna kuyamba kuphunzira ikebana. Aphunzitsi anga ndi mayi anga ankafuna kuti ndikaphunzire zimenezi ku yunivesite, koma mosachita kuganizira kaye kawiri ndinasankha kukaphunzira ku koleji ya Ikenobo. Ikenobo ndi mtundu wakale kwambiri wa ikebana ku Japan. Atandivomera pa kolejipo, ndinaphunzira mwakhama luso la kaikidwe ka maluwa.

Kuyamba Kuphunzira Ikebana

Ikebana, yomwe ndi luso la ku Japan, imakhudza momwe maluwa amaonekera akamamera. Ndifotokoze bwino pamenepa. Maluwa omwe ali m’kamphika m’sitolo yogulitsa maluwa akhoza kuoneka okongola, koma kodi mukawayerekezera ndi timaluwa timene tamera m’munda kapena mitengo yomwe yatulutsa maluwa m’mapiri, amene amakongola kwambiri ndi ati? Mukamayang’ana maluwa omera mwachilengedwe, mumatha kuona kuti ali ndi moyo ndipo amakukumbutsani nyengo yomwe muli. Pamenepa m’pamene mtima wanu umakhudzidwa kwambiri. Ikebana ndi njira yosonyezera kukongola kwachilengedwe kumeneko pogwiritsa ntchito maluwa ndi zomera, mwa kuwaika mogwirizana ndi mmene munawaonera ndi mmene anakukhudzirani mtima.

Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukufuna kuti munthu akaona maluwawo aone ngati ali m’nyengo ya phukuto. Mungachite zimenezo pogwiritsa ntchito maluwa amene amatuluka m’nyengo ya phukuto, monga gentian ndi patrinia, limodzi ndi masamba a m’nyengo imeneyi. Kodi mukufuna kuti zioneke ngati pakudutsa kamphepo? Mungaikemo timitengo tingapo ta udzu wa eulalia timene timagwedezeka pang’onopang’ono, ndipo anthu oona angamaone ngati kukuomba kamphepo kayeziyezi ka m’nyengo ya phukuto. Ndinakopeka kwambiri ndi ikebana, ndipo ndinkasangalala ndikamasonyeza momwe ndikumvera poika maluwa ndi zomera mu mphika wa maluwa.

Gulu Lokhala Ngati Banja Lalikulu

Mbiri ya ikebana ngati luso lokongoletsera zinthu inayamba zaka 500 zapitazo. Masukulu a ikebana amatsogoleredwa ndi mphunzitsi wamkulu. Udindo wa mphunzitsi wamkulu umakhala wosiyirana pamtundu. Popeza mphunzitsi wamkuluyo amakhala ataphunzira luso lakaleli kwa makolo ake, amakhala ngati tate wa gulu la anthu ambiri lokhala ngati banja. Kuwonjezera pa luso lakaleli, amayeneranso kuphunzitsa mbadwo wotsatira masitayilo atsopano amene wakhazikitsa mogwirizana ndi nyengo imene akukhalamo.

Nditamaliza maphunziro anga pa koleji ya Ikenobo n’kuphunziranso maphunziro a luso la kado kwa zaka ziwiri, ndinayamba kugwira ntchito ku Ikenobo Foundation mu January 1971. Ndinkakonza ndi kuonetsa “Zionetsero za Ikebana Zokonzedwa ndi Bungwe la Ikenobo” ku Japan konse. Ndinkapitanso kumalo osiyanasiyana m’dziko lonselo pamodzi ndi mphunzitsi wamkulu ngati mmodzi wa omuthandizira ake akamagwira ntchito yake yoika maluwa.

Ndimakumbukirabe nthawi yoyamba imene ndinaimirira pa pulatifomu ku malo ochitirako masewero a Fukuoka Sports Center kuti ndithandize mphunzitsi wamkuluyo pamene ankasonyeza kaikidwe ka maluwa. Ndinachita mantha kwambiri chifukwa panali anthu masauzande ambiri. Ndinapinda timitengo ndi kudula nthambi za maluwa, zomwe sindinayenere kuchita. Koma mphunzitsi wamkuluyo anangogwiritsa ntchito zimene ndinkachitazo poseketsa oonererawo pamene ankawafotokozera zomwe anali kuchita. Zimenezo zinandithandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo.

Pakakhala zochitika zapadera chifukwa choti kwabwera alendo ochokera kunja, ndinkapitira limodzi ndi mphunzitsi wamkuluyo kukaika maluwa. Monga momwe ndanenera poyamba paja, chochitika chimodzi choterocho n’chimene chinandichititsa kuti ndipite m’chipinda chokongola kwambiri m’nyumba ya mfumu yaikulu.

Kenaka anakhazikitsa sukulu ya Ikenobo Central Training School n’cholinga chophunzitsanso aphunzitsi m’dziko lonselo. Ineyo ndinapatsidwa ntchito yokhudzana ndi kuphunzitsa komanso kukonza maphunziro oti anthu aziphunzira. Ndinapatsidwanso ntchito yoyang’anira kupanga mabuku ndi mavidiyo oti azidzawagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu pafupifupi 200,000 m’masukulu 300 m’dziko lonse la Japan. Ndinapita malo osiyanasiyana m’dziko lonselo kuti ndizikaona momwe maphunzirowo anali kuyendera. Sukulu ya Ikenobo ilinso ndi masukulu kunja, choncho ndinkapita ku Taiwan nthawi zingapo pa chaka. Chifukwa cha zimenezi, mphunzitsi wamkulu anayamba kundikhulupirira ndipo ndinali ndi ntchito yapamwamba.

Ntchito yanga ndinkaikonda, koma sindinkasangalala kwenikweni pa moyo wanga. Ngakhale kuti ntchito yanga inkakhudzana ndi zinthu zokongola, panali zinthu zina zomwe zinkandikhumudwitsa. Ophunzira nthawi zambiri ankachitirana nsanje ndipo ankajedana ndi kunenerana zoipa, ndipo aphunzitsi m’malo amene ndinkapitako nthawi zambiri ankandifunsa kuti ndiwathandizeko nzeru. Koma popeza bungwe lathu linkakhulupirira kwambiri miyambo yakale ndi maudindo, panali zinthu zambiri zomwe sindikanatha kuzisintha. Popeza anthu ambiri ankakondadi ikebana kuchokera pansi pa mtima ndipo ankalimbikira maphunziro awo, ndinayesetsa kuwathandiza kuti aziphunzira mosangalala.

Nthawi Yoyamba Kuona Kukongola kwa Choonadi

Ndinkadana ndi chipembedzo chifukwa ndinkaganiza kuti chikhoza kundichititsa kuti ndisamaganize bwinobwino. Kuwonjezera apo, ndinaona kuti pakati pa anthu amene amalankhula za mtendere ndi chimwemwe panali chinyengo chachikulu. Koma mkazi wanga, Keiko, anakhala akufunafuna choonadi kuyambira ali mwana. Anachitapo chidwi ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndipo anamvetsera ziphunzitso zawo, koma palibe chimene chinathetsa njala yake yauzimu.

Choncho munthu wa Mboni za Yehova atabwera kunyumba kwathu, Keiko anavomera kuphunzira Baibulo. Ankandiuza chilichonse chomwe waphunzira ndiponso chilichonse chomwe chamuchititsa chidwi. Zimene Keiko ankandiuza zinkamveka zosangalatsa, koma ndinalibe nazo chidwi kwenikweni ngati mmene iyeyo ankachitira.

Komabe, Keiko anapitiriza kundiuza mosonyeza kuti akukhulupiriradi zomwe anali kuphunzira m’Baibulo. Ndikamapita ku ulendo, nthawi zonse ankaika magazini angapo ofotokoza za m’Baibulo m’chikwama changa. Koma sindinkawawerenga. Ndinkafuna kuteteza zinthu zimene ndinakhetsera thukuta kwa zaka zambiri. Tinali titangogula kumene nyumba yathu, ndipo pa chifukwa chosadziwika bwino ndinkaganiza kuti ndikayamba kukhulupirira ziphunzitso za m’Baibulo ndidzafunika kupatsa munthu wina nyumbayo. Panthawi imeneyi, Keiko anapita patsogolo mofulumira ndipo ankatsatira zomwe anali kukhulupirira. Ndinkaona ngati akundipatula ndipo ndinali wosungulumwa. Ngakhale ndinkadziwa kuti zomwe ankandiuzazo zinali zoona, ndinayamba kumutsutsa.

Ndinkatsutsa Komanso Ndinali N’chidwi ndi Choonadi

Nthawi zambiri ndinkabwera kunyumba usiku kwambiri kuchokera ku ntchito, koma masiku amene Keiko ankapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova, ndinkabwera dala mochedwa kwambiri kuposa masiku ena. Ngakhale ndibwere kunyumba 2 koloko kapena 3 koloko m’mawa, Keiko ankakhala akundidikirira kuti andiuze zomwe zachitika tsiku limenelo, kusonyeza kuti akundidera nkhawa. Koma sindinkafuna zoti banja langa lizichoka panyumbapo kwa maola angapo kupita ku misonkhano yachikristu. Ndinayamba kutsutsa kwambiri ndipo ndinayamba kunena zoti ndikufuna kuti banja lithe. Koma Keiko anakhalabe wolimba.

Ndinkalephera kumumvetsa Keiko. Ngakhale kuti iyeyo ndi ine sitinali kugwirizana ndiponso ankadwala mphumu, anali wachimwemwe pa zonse zomwe ankachita. Chomwe chinandichititsa kuti ndikopeke ndi Keiko koyambirira kwenikweni chinali chifukwa choti anali ndi mtima wabwino ndiponso anali wofatsa komanso wosachedwa kukhulupirira anthu. Ndipo n’chifukwa chake ndinkada nkhawa kuti akhoza kunyengezedwa atayamba kuphunzira Baibulo.

Komabe, Keiko ankagwiritsa ntchito zomwe anali kuphunzira ndipo ankayesetsa kukhala mkazi ndi kholo labwino. Ngakhale kuti ndinkamutsutsa, akandichonderera kuti ndipite ku misonkhano yachikristu ndi misonkhano ikuluikulu, ndinkapita nthawi ndi nthawi. Mwina ndinkapita chifukwa choti ndinkamunyadira.

Koma ndinkachitanso nsanje ndi Yehova. Pamene ndinaona kuti Keiko akuyesetsa kusintha, ndinadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani ziphunzitso za m’Baibulo zinali ndi mphamvu yaikulu choncho pa anthu. Ndinadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mkazi wanga ali wokonzeka kulimbana ndi mavuto ambirimbiri kuti akondweretse Yehova?’

Pasanapite nthawi yaitali, abale ena achikristu a mu mpingo wa Keiko anafuna kubwera kunyumba kwathu kudzandichezera. Sindinkafuna kukumana nawo. Komabe, ndinkafuna kudziwa chimene chinkamuchititsa Keiko kuti akhale ndi mtendere wa mumtima woterowo. Pomaliza, chifukwa chofuna kudziwa zomwe zinali kuchitika, ndinavomera kuti ndiziphunzira Baibulo. Pamene ndinayamba kuwadziwa bwino anthu amene ankabwera kudzandichezera, ndinaona kuti panali chinachake chimene chinkawachititsa kuti akhale anthu otsitsimula kukhala nawo. Kudzera mu phunziro la mlungu ndi mlungulo, choonadi cha m’Baibulo pang’ono ndi pang’ono chinayamba kundifika pamtima, ndipo maganizo anga anayamba kusintha.

Kukongola kwa Chilengedwe ndi kwa Choonadi

Pamene ndinkayesera kusonyeza kukongola kwa chilengedwe pogwiritsa ntchito ikebana, ndinkavutika kuti ndisonyeze bwinobwino kuchititsa chidwi kwake. Kenaka, pamene ndinaphunzira kuti ndi Yehova amene analenga zodabwitsa zonse zopezeka m’chilengedwe, ndinayamba kuzimvetsa zonse bwinobwino. Kodi munthu wamba angapikisane bwanji ndi Mlengi waluso? Yehova ndiye Waluso Wamkulu! Komabe, poyesera kumutsanzira, ndinayamba kuika maluwa mwa njira yabwino kuposa kale. Ndipo nditayamba kuphunzira Baibulo, anthu anayamba kundiuza kuti kaikidwe kanga ka maluwa kasintha. Ankandiuza kuti maluwawo ndikumawaika m’njira yoti azioneka okhazika mtima pansi, kuwonjezera pa kukhala okopa.

Mfundo zoona za m’Baibulo zinandithandiza kumvetsetsa bwino zinthu zambiri kwa nthawi yoyamba. Ndinaphunzira kuti Satana Mdyerekezi ndi amene akuchititsa mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano chifukwa iye ndi amene ali wolamulira wa dziko lino. Ndinaphunziranso kuti mtima wathu ndi wonyenga chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu. Nditaphunzira zinthu zimenezi zinandithandiza kumvetsa tanthauzo lenileni la zimene zikuchitika masiku ano. (Yeremiya 17:9; 1 Yohane 5:19) Ndinaphunzira kuti Yehova ndi Mulungu wamtendere, wodzadza ndi chikondi, chilungamo, mphamvu, ndi nzeru. (Deuteronomo 32:4; Aroma 11:33; 1 Yohane 4:8; Chivumbulutso 11:17) Ndinaphunziranso kuti Mulungu anatumiza Yesu kudzatifera chifukwa cha chikondi chake (Yohane 3:16; 2 Akorinto 5:14); ndi kuti idzafika nthawi imene sipadzakhalanso kuvutika kapena imfa (Chivumbulutso 21:4). Kukongola kwa mfundo zoona zimenezi kunandichititsa chidwi kwambiri. Kuwonjezera apo, Mboni za Yehova zimatsatira zomwe Yesu anaphunzitsa zoti, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” Kuona zimenezi zikuchitikadi kunanditsimikizira kuti ichi ndi chipembedzo choona.—Mateyu 22:39.

Vuto Limene Ndinafunika Kulithetsa

Pamene ndinayamba kumvetsetsa choonadi, ndinakumana ndi vuto. Mphunzitsi wamkulu akakhala kuti sangathe kupita ku maliro, nthawi zambiri ineyo ndinkapita m’malo mwake kukachita nawo mapemphero a Chibuda. Chimenechi chinakhala chiyeso kwa ine pamene ndinkaganizira zodzipereka kwa Yehova. Ndinatsimikiza mtima pandekha kuti sindizichita nawonso mapemphero a Chibuda. (1 Akorinto 10:21) Mwaulemu, ndinafotokozera mphunzitsi wamkuluyo kuti ndikufuna kubatizidwa posachedwapa, ndipo ndaganiza zosiya kuchita nawo mapemphero a mtundu wina uliwonse, ngakhale atakhala mbali ya ntchito yanga. Mphunzitsi wamkuluyo anandiuza kuti analibe vuto ndi zoti ine ndikhale Mkristu ndipo ndikhoza kumachita zinthu zokhudza chipembedzo m’njira iliyonse imene ineyo ndikufuna. Yankho limeneli linandisangalatsa komanso linandidabwitsa chifukwa ndinkaganiza kuti andikalipira ndiponso andichotsa ntchito.

Nditathetsa vuto limenelo, ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova pa msonkhano waukulu wachikristu mu June 1983, patatha chaka chimodzi chiyambireni phunziro langa la Baibulo. Potuluka m’dziwe lobatizira, Keiko anandichingamira akumwetulira kwambiri komanso misozi yachimwemwe ikutsika m’maso mwake. Inenso misozi ikutsika m’maso mwanga, ndinathokoza Yehova, Keiko ali pomwepo chifukwa cha chimwemwe chomwe tinali nacho limodzi.

Kusankha Kusiya Ntchito Yanga Yolembedwa

Mphunzitsi wamkulu anakhala akundimvetsa kwambiri pamene ndinakhala Mkristu wodzipereka. Ndinkagwira ntchito yanga mwakhama kwambiri kuposanso kale. Komabe, ndinkayesetsa kukwanitsa zomwe ndinafunika kuchita monga Mkristu kwinakunso ndikukwanitsa udindo wanga wakuntchito. Kwa zaka seveni, ndinkachita zowonjezereka pa utumiki wachikristu kwa miyezi ingapo chaka chilichonse.

Komabe, ndinafunika kuganizira mozama za moyo wauzimu wa mwana wanga wamwamuna mmodzi yekha, ndiponso za matenda a Keiko amene anali kukulirakulira. Ndinaganiza kuti, ‘Ndiyenera kumakhala nthawi yambiri ndi banja langa.’ Ndinkafunanso kuika poyamba zinthu za Ufumu pa moyo wanga. Zolinga ndi zofuna zimenezi zinandichititsa kupemphera kwa Yehova kumuuza kuti ndikufuna kusiya ntchito yanga ya ikebana. Mphunzitsi wamkulu anazindikira kuti ndatsimikizadi mtima, ndipo ndinatha kusiya ntchitoyo bwinobwino mu July 1990 ndili ndi zaka 42.

Kuthandiza Ena Kuti Aone Kukongola kwa Choonadi

Nditangosiya ntchito, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse kuti ndithandize anthu ena kuzindikira choonadi. Masiku ano ndimaphunzitsa kaikidwe ka maluwa tsiku limodzi pa mlungu, ndipo sinditsatira malamulo a Ikenobo. Ndili ndi mwayi wotumikira monga mkulu mu mpingo, ndipo Keiko akusangalala ndi utumiki waupainiya ndiponso matenda ake a mphumu achepako masiku ano kusiyana ndi kale. Mwana wathu wamwamuna anakwatira, ndipo ndi mtumiki wothandiza mu mpingo wapafupi. Ndi mwayi wapadera kwambiri kuti tonsefe monga banja tikutumikira Yehova!

Pamene Yesu Kristu adzakhala akutilamulira mu Ufumu, ndikufuna ndizidzagwiritsa ntchito zomera zimene ndimadzala pakhomo panga pokonza ndi kuika maluwa mokongola kwambiri. Chikhumbo changa chachikulu n’choti, limodzi ndi banja langa lokondedwa, ndidzatamande mpaka muyaya dzina lolemekezeka la Yehova, Mlengi wa zinthu zonse zokongola.

[Chithunzi patsamba 31]

Ndili ndi mkazi wanga, mwana wathu, ndi banja lake

[Zithunzi patsamba 31]

Pogwiritsa ntchito ikebana, mukhoza kusonyeza momwe mumaonera kukongola kwa chilengedwe