Nkhani Yakale Inakhudza Mitima ya Anthu
Nkhani Yakale Inakhudza Mitima ya Anthu
PA SUKULU inayake ku Suwałki, kumpoto chakummawa kwa dziko la Poland, mphunzitsi wina anauza ana a sukulu kuti akonzekere kudzakambirana nkhani ya kuchotsa mimba. Justyna, yemwe anali ndi zaka 16, anafufuza mfundo zake m’mabuku a Mboni za Yehova. Pa tsiku lokambiranalo, mphunzitsiyo anapatsa ana a sukuluwo mwayi wolankhulapo maganizo awo.
Justyna akuti: “Ndinapita kwa aphunzitsiwo n’kuwaonetsa nkhani ya mutu wakuti ‘Zochitika Tsiku ndi Tsiku pa Moyo wa Mwana Wosabadwa,’ yomwe inafalitsidwa mu Galamukani! ya May 22, 1980.” Iye anauza aphunzitsiwo kuti: “Taonani kuti ailemba ngati kuti akulankhulayo ndi mwana wosabadwa, amene mayi ake atsala pang’ono kuchotsa mimba yake. Ndikukhulupirira kuti nkhaniyi ikusangalatsani kwambiri.” Aphunzitsiwo anayamba kuwerenga nkhaniyo mokweza mawu. Ana a sukuluwo anakhala chete, aliyense akumvetsera mwatcheru.
Aphunzitsiwo asanawerenge n’komwe theka la nkhaniyo, anaona kuti sangathe kuimaliza chifukwa ankafuna kulira, ndipo anapempha mwana wa sukulu kuti apitirize kuwerenga. Aphunzitsiwo anakhala pansi n’kuyamba kulira. Atamaliza kuwerengako, panali kukambirana kosangalatsa, ndipo ana a sukulu ena anapempha kuti akufuna atapeza nkhaniyo. Justyna akuti: “Anthu a m’kalasimo anasintha momwe amaonera mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Kale ankawanyoza, koma tsopano sawanyozanso. Mnyamata mmodzi mpaka anayamba kumawerenga magazini a Galamukani! nthawi zonse.”
Justyna anatha kugwiritsira ntchito bwino nkhani imene anaipeza mu magazini ya Galamukani! yomwe inafalitsidwa zaka zoposa 20 zapitazo. Inunso mukhoza kupeza “nzeru” m’magazini akale a Galamukani! (Yobu 28:18) Mukapita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kwanuko, mukhoza kuwerenga mavoliyumu a Galamukani! omwe mungawapeze pa mashelufu mu laibulale kumeneko. Mungasangalale powerenga nkhani zothandiza zomwe sizitha ntchito ngakhale zinatuluka kalekale. Mukhozanso kupeza magazini yaposachedwapa ya Galamukani! kwa Mboni za Yehova m’dera lanu.
[Chithunzi patsamba 18]
Justyna pa nthawi imene anali pa sukulu