Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Amene Amalalikira Mogwira Mtima

Achinyamata Amene Amalalikira Mogwira Mtima

Achinyamata Amene Amalalikira Mogwira Mtima

Achinyamata ambiri a Mboni za Yehova amalankhula molimba mtima za chikhulupiriro chawo kusukulu ndiponso mu utumiki wachikristu, ndipo zinthu zawayendera bwino kwambiri. Taonani zitsanzo zotsatirazi. *

Kristina anati: “Pamene ndinali mu sitandade 3, aphunzitsi athu anapatsa aliyense buku loti azilembamo zochita zake za tsiku ndi tsiku. Aphunzitsiwo ankawerenga mabuku athuwo n’kulembamo maganizo awo pa zimene awerengazo. Ndinaganiza zolemba m’buku mwanga za nkhani ya mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene ndinali nditatsala pang’ono kukakamba. Aphunzitsiwo anaoneka kuti zawafika pamtima, choncho ndinaganiza zowaitana kuti abwere ku Nyumba ya Ufumu kudzamvera nkhani yangayo. Iwo sanangobwera okha, koma anabwera pamodzi ndi aphunzitsi anga amene anandiphunzitsa ndili mu sitandade wani. Atabwerera ku sukulu, aphunzitsiwo anauza anthu onse m’kalasi mwathu kuti anasangalala kwambiri ndi nkhani yanga. Ndinali wokondwa kwambiri. Koma sizinathere pomwepo. Patatha mwina chaka chimodzi, ndinafotokoza zimene zinachitikazi pa msonkhano wadera wa Mboni za Yehova ndipo aphunzitsi anga aja anabweranso ku msonkhano umenewo. Patapita nthawi, ine ndi mnzanga amene anali mpainiya tinapita kukawachezera aphunzitsiwo ndipo tinawapatsa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ndipo mpaka anabwera ku msonkhano wathu wina wachigawo!”

Pamene Sydnee anali ndi zaka sikisi, ankalankhula molimba mtima kwa anthu a m’kalasi mwake mfundo zoona zopezeka m’Mawu a Mulungu, kuphatikizapo zofotokoza zomwe zimachitika munthu akafa ndi udindo wa Yesu poyerekezera ndi Mulungu. Mayi ake anati: “Iye ndi mtumiki wamng’ono koma wachangu kwambiri ndiponso wopanda mantha.” Kumapeto kwa chaka chake choyamba ku sukulu, Sydnee ananena kuti anali wachisoni. Iye anati: “Ndikuwamvera chisoni anthu a m’kalasi mwanga. Kodi adzadziwa bwanji za Yehova?” Sydnee ataganizaganiza, anadziwa zochita. Patsiku lotsekera sukulu, iye anapatsa mwana wa sukulu aliyense mphatso ataikulunga bwino m’pepala. Mphatso yake inali Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Sydnee anagawa mabuku okwana 26, ndipo anauza ana a sukuluwo kuti akhoza kukatsegula mphatso yawoyo kunyumba limodzi ndi makolo awo. Sydnee amaona anthu a m’kalasi mwake ngati gawo lakelake loti azilalikiramo. Ndipo atawapatsa mabukuwo anawaimbira foni kuti amve ngati anasangalala nalo bukulo. Mtsikana wina anati amawerenga buku lakelo limodzi ndi mayi ake usiku uliwonse.

Pamene Ellen anali ndi zaka 15, anapatsa aphunzitsi ake a mbiri yakale magazini angapo a Galamukani! Ellen anati: “Aphunzitsiwo anawakonda kwambiri magaziniwo, ndipo akhala akuwerenga Galamukani! kwa zaka ziwiri tsopano.” Ellen anapitiriza kuti: “Posachedwapa ndinawapatsa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndipo anandiuza kuti ana awo aakazi awiri akusangalala nalo kwambiri. Choncho ndinawapatsa buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Kenaka anandipatsa khadi lomwe analembapo kuti: ‘Zikomo kwambiri chifukwa chotipatsa mabukuwa. Ine ndi ana anga tikusangalala nawo kwambiri powerenga. N’zosangalatsa kwambiri kuona wachinyamata wokhwima maganizo ndiponso wodzipereka ngati iwe. Palibe mphatso imene ingakhale yabwino kwambiri kuposa chikhulupiriro chimene uli nacho. Wandiphunzitsa zambiri kuposa zimene ineyo ndikanakuphunzitsa!’ Zimene zinachitikazi zinandisonyeza kuti anthu amayamikira kwambiri choonadi cha m’Baibulo tikayesetsa kuwafotokozera choonadicho.”

Daniel anali ndi zaka sikisi pamene anakhala ndi wophunzira Baibulo wakewake woyamba. Iye anati: “Ndinkakhala ndi mayi anga akamachititsa maphunziro awo, koma ndinkafuna munthu woti ndizimuphunzitsa ndekha.” Daniel anasankha Mayi Ratcliff, amayi achikulire omwe anawasiyirapo mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Iye anawauza kuti: “Ndikufuna ndikusonyezeni buku limene ndimalikonda kwambiri, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.” Ndipo anawonjezera kuti, “ndikufuna kudziwa ngati mungandilole kuti ndizibwera mlungu uliwonse kudzakuwerengerani buku limeneli.” Mayi Ratcliff anavomera kuti Daniel azibwera. A Laura, amayi ake a Daniel, anati: “Tinayamba kuphunzira ndi Mayi Ratcliff tsiku lomwelo masana. Daniel ndi Mayi Ratcliff ankawerenga ndime za m’bukulo mosinthanasinthana, kenaka Daniel ankawauza kuti awerenge malemba amene wasankha otchulidwa kumapeto kwa nkhani iliyonse. Ndinkapitira limodzi ndi Daniel, koma zinkaoneka kuti Mayi Ratcliff ankangofuna kukambirana ndi Daniel yekha basi!” Patapita nthawi, Daniel ndi Mayi Ratcliff anayamba kuphunzira buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Panthawi imeneyi, mlongo wake wa Daniel, Natalie anali atadziwa kuwerenga, choncho anayamba kumakhala nawo pa phunzirolo. Mayi Ratcliff ankafunsa mafunso ambiri, ndipo ena anali ovuta ndithu. Koma Daniel ndi Natalie anagwiritsa ntchito kabuku ka Mitu ya Nkhani ya Baibulo Yokambitsirana ndi mawu ondandalikidwa kumapeto kwa Baibulo kuti aziyankha mafunsowo mogwirizana ndi Malemba. Mayi Ratcliff, omwe anali Mkatolika kwa moyo wawo wonse, anasangalala kwambiri ndi zimene anali kuphunzira. Pamapeto pa phunzirolo tsiku lina, iwo anati: “Ndikudandaula kuti sindinayambe kuphunzira Baibulo zaka zambiri zapitazo!” N’zomvetsa chisoni kuti Mayi Ratcliff anamwalira posachedwapa ali ndi zaka 91. Koma chifukwa chophunzira Baibulo, anatha kudziwa mfundo za choonadi zofunika kwambiri, kuphatikizapo chiyembekezo cha m’Baibulo choti anthu adzauka pa dziko lapansi la paradaiso. Panopa Daniel ali ndi zaka teni ndipo amachititsa maphunziro a Baibulo awiri. Natalie, yemwe panopa ali ndi zaka eyiti, amaphunzira Baibulo ndi mtsikana wina wa msinkhu wake.

Achinyamata ngati Kristina, Sydnee, Ellen, Daniel, ndi Natalie amakondweretsa makolo awo achikristu. Koma chofunika koposa, amakondweretsa mtima wa Yehova, ndipo Yehova sadzaiwala chikondi chomwe achinyamata ngati amenewa amaonetsera pa dzina lake.—Miyambo 27:11; Ahebri 6:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mabuku onse amene atchulidwa mu nkhani ino ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 26]

Kristina (pamwamba) ndi Sydnee

[Chithunzi patsamba 27]

Daniel ndi Natalie

[Chithunzi patsamba 27]

Ellen