Kodi Kupemphera kwa Mariya Virigo N’koyenera?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Kupemphera kwa Mariya Virigo N’koyenera?
ANTHU ambiri amene amachidziwako bwino ndithu Chikristu amamudziwa Mariya. Malemba amati Mulungu Wamphamvuyonse anamudalitsa kwambiri mtsikana ameneyu pomusankha kuti akhale mayi a Yesu. Kubadwa kwa Yesu kunali kwapadera chifukwa Mariya anali namwali, kapena kuti virigo, pamene anakhala ndi pakati. Matchalitchi ena achikristu kuyambira kale amapembedza Mariya m’njira yapadera. M’chaka cha 431 C.E., Bungwe la ku Efeso linalengeza kuti Mariya ndi “Amayi a Mulungu,” ndipo masiku ano anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti azipemphera kwa iye. *
Anthu amene amafuna kulambira moona mtima amadziwa kuti amafunika kupemphera kwa munthu woyenera. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani imeneyi? Kodi Akristu ayenera kupemphera kwa Mariya Virigo?
“Tiphunzitseni Ife Kupemphera”
Uthenga wabwino wa Luka umanena kuti mmodzi mwa ophunzira a Yesu anamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.” Poyankha, Yesu anati: “Mmene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe.” Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anauzanso otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.”—Luka 11:1, 2; Mateyu 6:9.
Choncho chinthu choyamba chomwe tikuphunzira n’choti pemphero, kapena kuti mawu olambira, ayenera kupita kwa Atate a Yesu, omwe ndi Yehova. Palibe paliponse pamene Baibulo limatiuza kuti tizipemphera kwa wina aliyense. Zimenezi Eksodo 20:5.
n’zoyenera, chifukwa monga momwe Mose anauzidwira atalandira Malamulo Khumi, Yehova ndi “Mulungu wansanje.”—Nanga Bwanji Kugwiritsa Ntchito Korona Popemphera?
Anthu ambiri amene amapemphera kwa Mariya anaphunzitsidwa kuti akhoza kupeza madalitso akamanena mobwerezabwereza mapemphero enaake m’njira inayake. Mapemphero ake ndi monga, Tikuoneni Mariya, Atate Athu, ndi ena otero. Buku lakuti Symbols of Catholicism limati, kwa Akatolika “mosakayikira njira yofala kwambiri yopembedzera Mariya ndiyo korona.” Kupemphera pogwiritsa ntchito korona ndi mbali ya kulambira yomwe imalemekeza Mariya Virigo. Korona ndi kachingwe kokhala ndi mikanda imene imagwiritsidwa ntchito powerenga mapemphero. Buku talitchulali limafotokozanso kuti: “Mikanda khumi yokhala m’magulu asanu olekanitsidwa ndi mkanda umodzi imalimbikitsa munthuyo kulakatula ma ‘Tikuoneni Mariya’ 50, ma ‘Atate Athu’ asanu, ndi ma ‘Ulemu kwa Inu Atate’ asanu.” Kodi Mulungu amasangalatsidwa kumva anthu akulakatula mapemphero ndi mtima wonse pogwiritsa ntchito korona?
Pa nkhani imeneyinso, malangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake amatipatsa yankho lomveka bwino. Iye anati: “Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.” (Mateyu 6:7) Choncho Yesu anachita kuletseratu otsatira ake kuti asamanene mapemphero omangobwereza zomwezomwezo.
Koma mwina munthu angafunse kuti, ‘Kodi Yesu si paja anaphunzitsa ophunzira ake kuti azibwereza mawu a Atate Athu, omwe ali mbali ya mapemphero opemphera ndi korona?’ N’zoona kuti Yesu anatisiyira pemphero la chitsanzo, limene masiku ano limadziwika kuti Atate Athu, kapena Pemphero la Ambuye. Koma tisaiwale kuti analipereka atangotha kupereka chenjezo lili pamwambali, loti ‘asamabwerezebwereze chabe iyayi.’ Chinanso chomwe chikusonyeza kuti Yesu sanafune kuti pemphero la chitsanzo lizilakatulidwa pamtima n’choti pa nthawi ziwiri zolembedwa m’Baibulo zomwe anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera, iye anagwiritsa ntchito mawu osiyana. (Mateyu 6:9-15; Luka 11:2-4) Mfundo zomwe Yesu anatchula pa nthawi ziwirizo zinali zofanana, koma mawu ake anali osiyana. Zimenezi zikutithandiza kuona kuti Yesu ankangopereka chitsanzo cha momwe otsatira ake angapempherere ndi zinthu zomwe zili zoyenera kuzipempherera. Ndipo chofunika kwambiri n’choti mawu ake anasonyeza kuti tiyenera kupemphera kwa ndani.
Kulemekeza Mariya
Popeza Malemba saphunzitsa kuti Akristu azipemphera kwa Mariya sizitanthauza m’pang’onong’ono pomwe kuti sayamikira ntchito imene Mariya anagwira pokwaniritsa zolinga za Mulungu. Madalitso amene anabwera kudzera mwa Mwana wake adzathandiza anthu mpaka muyaya. Mariya mwiniwakeyo ananena kuti: “Anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.” Ndipo mbale wake Elisabeti, anati Mariya anali “wodalitsika . . . mwa akazi.” Ndipo analidi wodalitsika. Unali mwayi wapadera kwambiri kwa Mariya kuti asankhidwe kubereka Mesiya.—Luka 1:42, 48, 49.
Komabe, Mariya si mkazi yekhayo amene Malemba amamutcha wodala. Chifukwa cha zimene Yaeli anachita pothandiza mtundu wakale wa Israyeli, nayenso ananenedwa kuti anali “wodalitsika, woposa akazi.” (Oweruza 5:24) Yaeli wokhulupirikayo, Mariya, ndi akazi ena oopa Mulungu otchulidwa m’Baibulo ndi ofunikadi kuti tiziwatsanzira, koma osati kuwalambira.
Mariya anali wotsatira wa Yesu wokhulupirika. Nthawi zingapo pamene Yesu anali kuchita utumiki wake padziko lapansi, Mariya ankakhala m’gulu la anthu opezeka pamene panali Yesu ndipo analiponso pa nthawi ya kufa kwake. Yesu ataukitsidwa, iye “analikukangalika m’kupemphera” pamodzi ndi abale a Yesu. Zimenezi zimatipatsa chifukwa chokhulupirira kuti limodzi ndi abale a Yesuwo, Mariya nayenso anadzozedwa ndi mzimu woyera pa Pentekoste mu 33 C.E. Choncho anali ndi chiyembekezo chodzakhala mbali ya gulu la mkwatibwi lomwe lidzalamulire kumwamba ndi Kristu.—Mateyu 19:28; Machitidwe 1:14; 2:1-4; Chivumbulutso 21:2, 9.
Komabe, palibe chilichonse mwa mfundo zonsezi chomwe chikusonyeza kuti tiyenera kupemphera kwa Mariya. Kupemphera kochokera pansi pa mtima ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira, ndipo Akristu amalimbikitsidwa ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera.’ (Aroma 12:12) Koma mapemphero onse oterowo ayenera kupita kwa Yehova yekha basi, kudzera mwa Yesu Kristu.—Mateyu 4:10; 1 Timoteo 2:5.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Zoti Mariya ndi amayi a Mulungu zinachokera pa chiphunzitso chosagwirizana ndi malemba cha Utatu, chomwe chimati Yesu ndi Mulungu.