Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisayambe Kucheza ndi Anthu Olakwika?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisayambe Kucheza ndi Anthu Olakwika?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisayambe Kucheza ndi Anthu Olakwika?

“Ndinayamba kucheza ndi mtsikana winawake ku sukulu. . . . Sankagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuchita mapwando achiwawa, kapena kuchita zachiwerewere. Komanso sankatukwana, ndipo nthawi zonse ankakhoza bwino m’kalasi. Koma ndikudziwa kuti sanali munthu wabwino kucheza naye.”—Anatero Beverly. *

KODI n’chifukwa chiyani Beverly ananena mawu ali pamwambawa? Tsopano akudziwa kuti mtsikana ameneyu anamuyambitsa kuchita zinthu zoipa. Beverly akufotokoza kuti: “Pamene ndinapitiriza kucheza naye, ndinayamba kuwerenga mabuku onena zamizimu, ndipo ndinafika mpaka polemba nkhani yokhudzana ndi zamizimu.”

Mtsikana wina dzina lake Melanie nayenso anasocheretsedwa n’kuyamba khalidwe loipa, koma amene anamusocheretsa ndi munthu amene ankanena kuti anali Mkristu mnzake! Kodi mungadziwe bwanji ngati winawake angakhale mnzanu wabwino? Kodi nthawi zonse kucheza kwambiri ndi anthu amene ali osakhulupirira n’koopsa? Kodi mabwenzi amene mwapeza pakati pa Akristu anzanu nthawi zonse amakhala abwino?

Ndipo chofunika kwambiri, bwanji za zibwenzi za anyamata ndi atsikana? Ngati mukufuna kuti winawake adzakhale mkazi wanu kapena mwamuna wanu, kodi mungadziwe bwanji ngati ubwenzi wanuwo ungakulimbikitseni mwauzimu? Tiyeni tione momwe mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuyankha mafunso amenewa.

Kodi Mabwenzi Abwino Amakhala Otani?

Pankhani ya Beverly ija, popeza mnzake wa ku sukuluyo sankalambira Mulungu woona, kodi iye anayenera kuganiza kaye kawiri asanayambe kucheza naye? N’zoona kuti Akristu oona samangoganiza kuti munthu ndi wakhalidwe loipa kapena wachiwerewere kokha chifukwa choti si wokhulupirira mnzawo. Koma ngati mukuganiza zoti akhale mnzanu wapamtima, m’pofunika kusamala. Mtumwi Paulo anachenjeza anthu a mumpingo woyambirira wa ku Korinto kuti: “Kuyanjana ndi oipa kumawononga khalidwe.” (1 Akorinto 15:33, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Kodi anatanthauzanji?

N’kutheka kuti ena mwa Akristu a ku Korinto amenewo ankacheza ndi Aepikureya, otsatira Mgiriki wina wofufuza nzeru zapamwamba dzina lake Epicurus. N’zoona kuti Epicurus ankaphunzitsa otsatira ake kuchita zinthu mwanzeru, molimba mtima, modziletsa, ndiponso mwachilungamo pamoyo wawo. Ndipo ankawakaniza ngakhale kuchita machimo mobisa. Choncho, n’chifukwa chiyani Paulo ankaona kuti Aepikureya, ngakhalenso anthu ena mumpingomo amene anali ndi maganizo ofanana nawo, anali “mayanjano oipa”?

Aepikureya sankalambira Mulungu woona. Popeza sankakhulupirira zoti akufa adzauka, cholinga chawo chachikulu chinali kusangalala monga momwe angathere pa moyo wawo. (Machitidwe 17:18, 19, 32) Choncho n’zosadabwitsa kuti chifukwa chocheza ndi anthu oterowo, ena mu mpingo wa Korinto anayamba kusiya kukhulupirira zoti akufa adzauka. N’chifukwa chake mu chaputala 15 cha Akorinto Woyamba, mmene tikupezamo chenjezo la Paulo loletsa mayanjano oipa, muli mfundo zambiri zomwe cholinga chake chinali kuwathandiza Akristu oyambirira amenewo kuyambiranso kukhulupirira kuti chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chenichenidi.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngakhale anthu osapembedza Mulungu akhoza kusonyeza makhalidwe abwino. Koma ngati mucheza nawo kwambiri, maganizo anu, chikhulupiriro chanu, ndi khalidwe lanu zikhoza kuyamba kusintha. N’chifukwa chake m’kalata yake yachiwiri kwa Akorinto, Paulo anati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.”—2 Akorinto 6:14-18.

Fred, wa zaka 16, anazindikira kuti mawu a Paulo ndi anzerudi. Iye poyamba anavomera kulowa nawo gulu linalake ku sukulu lomwe zochita zake zinaphatikizapo kupita ku dziko linalake losauka kukathandiza kuphunzitsa ana kumeneko. Komabe, pamene ankakonzekera limodzi ndi anzake a ku sukuluwo, Fred anasintha maganizo. Iye anati: “Ndinaona kuti kukhala nthawi yaitali choncho ndili nawo limodzi kukanandipweteketsa mwauzimu.” Pachifukwa chimenechi, Fred anasankha kuchoka pagululo n’kukathandiza mwanjira zina anthu osowa.

Kupeza Mabwenzi Pakati pa Akristu Anzanu

Nanga bwanji zopeza mabwenzi m’kati mwa mpingo wachikristu? Polembera kalata Timoteo, yemwe anali wachinyamata, Paulo anamuchenjeza kuti: “Koma m’nyumba yaikulu simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu. Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.” (2 Timoteo 2:20, 21) Choncho Paulo sanabise zoti ngakhale pakati pa Akristu, pangapezeke ena amene khalidwe lawo lili lopanda ulemu. Ndipo sanapite m’mbali pochenjeza Timoteo kuti apewe anthu oterowo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kumakayikira Akristu anzanu? Ayi. Ndipo sizikutanthauzanso kuti muyenera kuyembekezera anzanu kukhala angwiro. (Mlaliki 7:16-18) Komabe, chifukwa chakuti wachinyamata amapita ku misonkhano yachikristu kapena ali ndi makolo amene ali achangu mumpingo, sizitanthauza kuti wachinyamatayo ndi munthu wabwino kukhala mnzanu wapamtima.

Lemba la Miyambo 20:11 limati: “Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” Choncho muyenera kudzifunsa kuti: Kodi n’zachionekere kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa munthu ameneyu ndi ubwenzi wake ndi Yehova? Kapena, kodi pali umboni woti maganizo ake akusonyeza “mzimu wa dziko lapansi”? (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2) Kodi mukakhala ndi munthuyo amakulimbikitsani kulambira Yehova?

Ngati mumacheza ndi anthu amene amakonda kwambiri Yehova ndi zinthu zauzimu, sikuti mudzangopewa chabe mavuto, koma adzakulimbikitsani kwambiri kutumikira Mulungu. Paulo anauza Timoteo kuti: ‘Utsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.’2 Timoteo 2:22.

Kupeza Chibwenzi

Ngati ndinu wachikulire ndithu ndipo mukufuna kukwatira, kodi mwaganiza mofatsa za momwe mfundo zomwezi ziyenera kukutsogolerani posankha munthu woti mukwatirane naye? Pali zinthu zambiri zimene zingakuchititseni kukopeka ndi mtsikana kapena mnyamata, koma palibe chimene chili chofunika kwambiri kuposa chidwi chimene munthuyo ali nacho pa zinthu zauzimu.

Choncho Baibulo mobwerezabwereza limatichenjeza kuti tisakwatirane ndi munthu amene sali “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; Deuteronomo 7:3, 4; Nehemiya 13:25) N’zoona kuti anthu amene si okhulupirira anzathu akhoza kukhala odalirika, olemekezeka, ndi achifundo. Komabe, alibe mtima wofunitsitsa kulimbikitsa makhalidwe amenewo ndi kupirira mu ukwati kwa zaka zambiri.

Koma munthu amene anadzipereka kwa Yehova ndipo ndi wokhulupirika kwa iye amayesetsa kupitirizabe kukhala ndi makhalidwe achikristu, ngakhale akumane ndi zotani. Iye amadziwa kuti Baibulo limasonyeza kuti kukonda mkazi wako kapena mwamuna wako n’kofunika kuti ukhale ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Aefeso 5:28, 33; 1 Petro 3:7) Choncho, ngati mwamuna ndi mkazi onse amakonda Yehova, amakhala ndi chifukwa chachikulu kwambiri chokhalira okhulupirika kwa wina ndi mnzake.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti maukwati onse a anthu okhulupirira amayenda bwino? Ayi. Mwachitsanzo, ngati mutakwatira munthu amene salimbikira kwenikweni zinthu zauzimu, kodi n’chiyani chingachitike? Popeza alibe mphamvu zomuthandiza kulimbana ndi mavuto a m’dzikoli, n’zosavuta kuti munthu wofooka mwauzimu asiyane ndi mpingo wachikristu. (Afilipi 3:18; 1 Yohane 2:19) Tangoganizirani momwe mtima wanu ungapwetekere ndiponso momwe ukwati wanu ungasokonekere ngati mwamuna wanu kapena mkazi wanu angakopeke ndi “zodetsa za dziko lapansi.”—2 Petro 2:20.

Musanayambe chibwenzi ndi munthu amene pamapeto pake mungakwatirane naye, dzifunseni kuti: Kodi munthu ameneyu amasonyeza kuti amakonda zinthu zauzimu? Kodi amapereka chitsanzo chabwino monga Mkristu? Kodi iyeyu ndi wokhazikika m’choonadi cha m’Baibulo, kapena akufunika nthawi kuti akule mwauzimu? Kodi mukukhulupirira kuti zinthu zimene amachita pamoyo wake amazichita makamaka chifukwa chokonda Yehova? Kudziwa kuti munthuyo ali ndi mbiri yabwino n’kothandiza. Komabe, pomalizira pake, muyenera kukhulupirira kuti munthu amene mukumufunayo ndi wodziperekadi kwa Yehova ndipo mosakayikira adzakhala mkazi kapena mwamuna wabwino.

Kumbukiraninso kuti anthu ena amene amayamba kucheza ndi “anthu olakwika” choyamba amakopeka ndi zinthu zolakwika, monga zosangalatsa kapena zochita zinazake zosayenera. Achinyamata a chitsanzo chabwino mumpingo wachikristu sangachite nanu zinthu ngati zimenezo. Choncho, dzipendeni zimene mukufuna mu mtima mwanu.

Ngati mukuona kuti mtima wanu ukufunika kulangidwa, musataye mtima. Mtima ukhoza kusintha ukalangidwa. (Miyambo 23:12) Mfundo yofunika kwambiri ndi iyi: Kodi inuyo mukufuna chiyani kwenikweni? Kodi mukufuna kumachita zinthu zabwino ndi kumachezanso ndi anthu amene amachita zabwino? Ndi thandizo la Yehova, mukhoza kukhala ndi mtima wofuna zinthu zimenezo. (Salmo 97:10) Ndipo mukadziphunzitsa kuganiza mwanzeru kuti muzitha kuzindikira chabwino ndi choipa, mudzaona kuti sizovuta kudziwa anthu amene angakhale mabwenzi abwino, okulimbikitsani.—Ahebri 5:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina.

[Chithunzi patsamba 14]

Anzanu abwino amakulimbikitsani kuchita zinthu zauzimu