Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunika kwa Mgwirizano M’chilengedwe

Kufunika kwa Mgwirizano M’chilengedwe

Kufunika kwa Mgwirizano M’chilengedwe

M’chilengedwe, “kukhala ndi moyo kumadalira osati pa kukula ndi kuberekana kokha komanso pa kugwirizana ndi zamoyo zina zokhala pafupi.” —Limatero buku lotchedwa “Liaisons of Life.”

PA NYANJA ya mchere panali bata ndipo kunja kunali zii. Phokoso limene linkamveka linali lapansipansi la mbalame zambirimbiri za kunyanja. Kulira kwa mbalameko kumasonyeza kuti chinachake chinali kuchitika m’madzimo. Mwadzidzidzi, pamwamba pa madzipo panaoneka thovu, lomwe pang’ono ndi pang’ono linayamba kuchuluka pamadzipo. Patapita kanthawi, pakati pa thovu la m’madzi oyerawo panaoneka zinyama ziwiri zikuluzikulu. Anali anamgumi awiri okhala ndi linunda pamsana ndipo amachokera pansi pa nyanjayo, kukamwa kuli yasa! Atafika pamwamba pa madziwo, anatseka kukamwa kwawo kwakukuluko, anamina madzi, n’kutulutsa nthunzi mkamwa mwawo, kenaka n’kumiranso m’madzimo kuti akayambirenso.

Anamgumi awiriwo anali kugwira ntchito mothandizana kuti asonkhanitse pamodzi ndi kudya zamoyo zangati nkhanu zambirimbiri. Mokhala ngati akuvina m’madzi, anamgumi olemera matani 40 amenewo anamira pansi pa nyama zooneka ngati nkhanuzo n’kusambira mozizungulira uku akutulutsa mpweya mphuno mwawo. Kuvina kwanzeru kotereku kunapanga thovu lomwe linazungulira nyama zangati nkhanuzo ngati mmene ukonde umachitira. Kenaka anamgumiwo anakwera kufika pamwamba pa madzi kudzera pakati pa thovu lokhala ngati ukonde lija n’kumadya nyamazo.

M’zigwa za ku Africa kuno, anyani ndi mbawala nthawi zambiri zimachita zinthu mogwirizana. Magazini yotchedwa Scientific American inati: “Nyama za mitundu iwiri zimenezi zimachenjezana ngati kukubwera zoopsa.” Mbawala zimanunkhiza bwino kwambiri pamene anyani amaona bwino kwambiri, choncho zikakhala pamodzi zimathandizana kuona nyama zolusa zikamabwera, motero nyamazi zimadziwa kuti kukubwera nyama zolusa, nyama zolusazo zidakali kutali. Palinso mgwirizano wofanana ndi umenewu pakati pa nthiwatiwa ndi mbidzi. Nthiwatiwa zimaona bwino kwambiri, pamene mbidzi zimamva bwino kwambiri.

Izi ndi zitsanzo zochepa chabe mwa zitsanzo zambiri za mgwirizano m’chilengedwe. Indedi, kuthandizana kumaoneka pa zamoyo zosiyanasiyana, kuyambira pa zamoyo zosaoneka ndi maso paokha kufika pa anthu, ndiponso pakati pa zamoyo zamtundu umodzi ndi za mitundu yosiyana. Zaka masauzande ambiri zapitazo, Mfumu Solomo, yemwe ankadziwa bwino za chilengedwe, anaona zomwe tinyerere timachita. Iye analemba kuti: “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitawo, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta dzinthu zawo m’masika.”—Miyambo 6:6-8.

Nyerere zimapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha mgwirizano, khama, ndi dongosolo labwino. Nthawi zambiri zimagwirira ntchito limodzi, kukokera ku mauna awo zinthu zazikulu kwambiri kuposa izozo. Nyerere zina mpaka zimathandiza nyerere zovulala kapena zotopa kuzipititsa ku una wawo. Chifukwa cha makhalidwe amenewa, n’zosadabwitsa kuti Solomo anasankha nyerere monga chitsanzo choti tizitsatira.

Mu nkhani zotsatirazi, tiona momwe mgwirizano umapezekera paliponse m’chilengedwe, zomwe zimachititsa kuti moyo, kuphatikizapo moyo wa anthu, ukhale wotheka. Tionanso zinthu zosemphana ndi zimenezi zimene anthu amachita powononga chilengedwe, kuchiipitsa, ndi kupulula zachilengedwe. Kodi Mlengi alola kuti zimenezi zipitirirebe mpaka kalekale?

[Chithunzi patsamba 3]

Pamwambapa: Anyani ndi mbawala zimachenjezana ngati kukubwera zoopsa

[Chithunzi patsamba 4]

Nyerere zimapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha mgwirizano

[Chithunzi patsamba 4]

Pali mgwirizano pakati pa nthiwatiwa, zomwe zimaona bwino kwambiri, ndi mbidzi, zomwe zimamva bwino kwambiri