Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amalemekezeka Tikamachita Zinthu Moona Mtima

Mulungu Amalemekezeka Tikamachita Zinthu Moona Mtima

Mulungu Amalemekezeka Tikamachita Zinthu Moona Mtima

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU UKRAINE

TSIKU linalake, anthu a m’banja la a Chibisov, omwe ndi Mboni za Yehova ku Ukraine ankachokera ku msonkhano wachikristu kupita kunyumba ndipo anapeza kachikwama kali ndi zinthu zofunika m’kati mwake. Zina mwa zinthuzo zinali laisensi yoyendetsera galimoto, makadi ogulira zinthu pangongole, ndi ndalama zokwana pafupifupi madola 500 zakwawoko. M’banja la anthu asanu limeneli, ndi bambo okha amene anali pantchito. Ankalandira ndalama zokwana pafupifupi madola 70 okha pamwezi. Choncho ndalama zimenezi zikanatha kuwathandiza kwambiri. Koma kodi anachita chiyani?

Amayi a m’banjamo anafotokoza kuti: “Ana athu nthawi yomweyo anayamba kukambirana zobweza kachikwamako kwa mwini wake, amene, malinga ndi laisensi imene inali m’kachikwama ija, anali mzimayi. Ine ndi mwamuna wanga tinakondwa kuona momwe ana athu anasonyezera kuti ali ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino. Tsiku lotsatira ndinaimbira foni mayi amene anataya kachikwamayo, dzina lake Olha. Misozi yachimwemwe ikuyenderera m’masaya, Olha anabwera ndipo anatiuza kuti iye ndi mwamuna wake ali ndi masitolo ang’onoang’ono angapo m’tawuni yathu. Ndalama zimene zinali m’kachikwamazo zinali malipiro apamwezi a antchito awo. Komanso, chipepala chimodzi chomwe chinali m’kachikwamako chinali chofunika kwambiri pa ntchito yowerengetsera ndalama za bizinezi yawo.

“Olha anatifunsa komwe tinatola kachikwamako. Tinamuuza komwe tinakapeza, ndipo tinamuuzanso kuti tinali kumeneko chifukwa tinkachokera ku msonkhano wathu wachikristu. Titamupatsa mabuku angapo ofotokoza za m’Baibulo, analandira mwaulemu.

“Patatha milungu ingapo, wa Mboni mnzathu wa mu mpingo mwathu anatiuza kuti pamene anali kugawira mabuku ofotokoza Baibulo kwa anthu mumsewu, mayi wina anamufotokozera kuti kale sakanamvetsera Mboni za Yehova. Koma tsopano anali wokonzeka osati kungomvetsera chabe, komanso kutengako mabuku athu. Mayiyo anati chifukwa chimene chinamuchititsa kusintha n’choti Mboni zinabwezera mwana wake wamkazi kachikwama komwe kanamutayika.”

[Chithunzi patsamba 18]

Banja la a Chibisov