Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinapeza Chinachake Chabwino Koposa

Tinapeza Chinachake Chabwino Koposa

Tinapeza Chinachake Chabwino Koposa

YOSIMBIDWA NDI FRANCIS DEL ROSARIO DE PÁEZ

M’chaka cha 1988, ine ndi azichimwene anga, limodzi ndi magulu ena oimba, tinaimba pamaso pa anthu masauzande ambiri ku Madison Square Garden ku New York City. Anthu anasangalala kwambiri ndi gulu lathu, lomwe ineyo ndinali wovina wake. Zaka zingapo m’mbuyomo, bambo athu ndi amene anatiyalira maziko kuti tithe kutchuka chonchi.

BAMBO athu nawonso anali woimba, ndipo anaona kuti azichimwene anga aakulu seveni anali ndi luso loimba. Choncho anagulitsa nyumba yathu n’kugula zida zoimbira ndi zida zina zofunika kuti awathandize kuyambitsa gulu loimba. Panthawi imeneyo ine ndinali mwana, chifukwa ndinabadwa zaka zochepa m’mbuyomo mu 1966. Panthawiyo, tinkakhala m’tawuni ya Higüey m’dziko la Dominican Republic.

Nthawi yoyamba imene azichimwene anga anaimba nyimbo pagulu inali mu 1978 mu holo ya tawuni ya Higüey. Kenaka anasamuka n’kukakhazikika ku likulu la dziko lathu, ku Santo Domingo. Anayamba kuimba ndi kuvina sitayilo yamakono ya chamba cha merengue, ndipo chifukwa cha zimenezi, anatchuka kwambiri. * Gululo linayamba kutchedwa Los Hermanos Rosario (Anthu Apachibale a M’banja la a Rosario).

Popeza kuyambira kalekale ndinkafuna n’takhala wovina wotchuka, ndinafuna kulowa nawo gulu la azichimwene anga. Tsiku linalake paphwando, mchimwene wanga Pepe, amene anali m’tsogoleri wa gululo, anandipempha kuti ndivine, ndipo anati: “Francis ndi mchemwali wanga wamng’ono kwambiri, ndipo amadziwa kuvina.” Kavinidwe kanga kanachititsa chidwi anthuwo. Popezerapo mwayi pamenepa, ndinauza Pepe kuti ndikufuna ndizivina nawo m’gululo. Choncho ndili ndi zaka 16 ndinayamba kuvina nthawi zonse gulu la Los Hermanos Rosario likamaimba.

Kutchuka Pantchito Yanga

M’mbuyomo, kunali azimayi oimba ndi magulu a chamba cha merengue, koma kunali kusanakhaleko mzimayi wovina pakati pa gulu la amuna oimba. Ndinayambitsa kavinidwe kangakanga pogwiritsa ntchito sitayilo yatsopano yovinira nyimbo zathu za merengue. Kavinidwe kanga katatchuka kwambiri, kankatchedwa a lo Francis Rosario (kavinidwe ka Francis Rosario).

Tinali ndi nyimbo ya merengue yotchedwa “Cumandé,” yomwe mawu ake ena anali oti: “Y ahora todo el mundo como Francis Rosario.” (Tsopano aliyense avine ngati Francis Rosario). Zikatero anthu ankatsanzira kavinidwe kanga. Nthawi zina ankangokhala pansi n’kumandionerera m’malo movina. Patapita nthawi, akafuna kulengeza kuti gulu lathu liimba kwinakwake ankangosonyeza chithunzi changa basi. Aliyense ankadziwa kuti chithunzicho chikutanthauza kuti gulu la Los Hermanos Rosario likaimba kwinakwake.

Nditayamba kuimba limodzi ndi azichimwene anga, anthu ena analowa nawo m’gululo, kuphatikizapo anthu atatu apachibale omwe dzina la bambo awo linali Páez. M’modzi mwa iwo, woimba lipenga dzina lake Roberto, kenaka anadzakhala mwamuna wanga. Ana a Páez amenewo anayamba kupeza nawo phindu chifukwa cha kutchuka kwa gululo. Gulu la Los Hermanos Rosario linkaitanidwa kambirimbiri kukaimba pa TV ku Santo Domingo, kuphatikizaponso kukaimba m’mayiko ena.

Mu 1988 tinapita pa ulendo wokaimba ku United States ndi ku Canada. Nthawi imodzi imene tinaimba ndi imene ndaitchula koyambirira kuja ku Madison Square Garden. Magulu ambiri a merengue otchuka anaimba nawo kumeneko, ndipo gulu lathu ndi limene anthu analikonda kwambiri. Chitatha chionetsero chimenechi, anthu okonza zoimbaimba nthawi zonse ankatiika kuti tikhale omaliza kuimba pakakhala zionetsero. Kuposa kale lonse, anthu ambiri anayamba kudziwa za kavinidwe kanga, ndipo anthu okonda gulu la Los Hermanos Rosario anali kuchuluka. Malonda a nyimbo zathu analinso kuwonjezeka kwambiri.

Tinkayenda kwambiri, ndipo tinapita ku Colombia, Ecuador, Panama, Puerto Rico, Curaçao, Spain, Germany, ndi mayiko ena. Pasanapite nthawi yaitali tinakhala limodzi mwa magulu otchuka kwambiri a nyimbo ku Latin America. Kuvinako, malo ovinira, zovala, ndi kuphoda kumaso, zinakhala zinthu zofunika kwambiri pamoyo wanga.

Pamene ndinali mbeta, ndinkanena kuti ngati mwamuna akanandifuna koma wosakonda kuvina, ndikanamusiya m’malo mosiya kuvina. Komabe, maganizo anga a zinthu zomwe zinali zofunika pamoyo anayamba kusintha.

Kuzindikira Kufunika kwa Zinthu Zauzimu

Kusintha kumeneku kunayamba pamene tinali pa ulendo woimba ku zilumba za Canary mu 1991. Ndinali nditangokwatirana kumene ndi Roberto. Mchimwene wake Freddy, amenenso ankaimba m’gululo, anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo nthawi zonse ankakhala ndi mabuku awo.

Tsiku lina ndinaona buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi m’chipinda cha Freddy, ndipo ndinayamba kuliwerenga patalipatali. Ndinachita chidwi ndi mutu wakuti “Kodi Helo Ndimalo Amtundu Wotani?” Ndinachita nawo chidwi chifukwa mayi anga anandiuza kuti munthu amene wachita zoipa adzapsa ndi moto ku helo. Choncho ndinkaopa kupitako.

Patapita milungu yochepa, tikadali ku zilumba za Canary komweko, ndinapita padera. Atandipititsa kuchipatala, ndinauza Roberto kuti apemphe Freddy buku limene ndinaliona m’chipinda mwake lija. Ndinkafuna ndiziliwerenga pamene ndinali kuchira. Ndinalikonda kwambiri bukulo. Mwa zina, ndinazindikira kuti Baibulo siliphunzitsa kuti kuli helo wamoto, ndikuti Mulungu sanaganizepo zowotcha anthu ndi moto. (Yeremiya 7:31) Zinandikhudza mtima kwambiri kuzindikira kuti Baibulo limaphunzitsa kuti anthu akufa sadziwa kalikonse.—Mlaliki 9:5, 10.

Titabwerera ku Dominican Republic, Freddy anatumiza munthu wa Mboni za Yehova kuti adzatichezere. Iye anatiuza chiyembekezo cha m’Baibulo cha paradaiso wa padziko lapansi, ndipo zimenezi zinachititsanso mwamuna wanga kukhala ndi chidwi. (Salmo 37:29; Luka 23:43) Tinapempha kuti tiziphunzira Baibulo.

Kusintha Mmene Ndinkaonera Zinthu Ndiponso Zolinga Zanga

Pamene ndinayamba kudziwa zambiri za m’Baibulo, ndinayamba kusintha momwe ndinkaonera ntchito yanga, yomwe ndinkaikonda kwambiri. Mfundo za m’Baibulo zinayamba kusintha maganizo anga. (Aroma 12:2) Ndinayamba kumadzifunsa kuti: ‘Kodi ndiyeneradi kumavina chonchi pamalo ngati ano anthu onsewa akundionerera? Izi si zimene ndikufuna ayi.’ Ndinapemphera kwa Mulungu kuti, “Chonde ndithandizeni kusiya zimenezi.” Ndinauza mwamuna wanga maganizo angawo, ndipo nayenso ankaganiza chimodzimodzi. Anandiuza kuti: “Leza mtima, wokondedwa wanga. Uyambe ndi iweyo kuchoka m’gululi, ndipo ine nditsatira pambuyo pako.”

Ndinakhalanso woyembekezera kachiwiri, ndipo popeza zimenezi zinatanthauza kuti sindikanatha kumavina nthawi zambiri, ndinakhala womasuka n’kumatha kupita ku misonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu nthawi zambiri. Misonkhanoyi inandilimbikitsa, ndipo inamulimbikitsanso Roberto, amene ankapita nawo. Inatichititsanso kuzindikira kufunika kosonkhana ndi anthu a Yehova. Tinazindikira kuti, kuti tipitirize kupita patsogolo mogwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo, tinafunika maphunziro ndi chilimbikitso zomwe tinkazipeza ku misonkhano yachikristu. (Ahebri 10:24, 25) Ngakhale tikamagwira ntchito kunja kwa dziko la Dominican Republic, ine ndi Roberto tinkafunafuna Nyumba ya Ufumu ndipo tinkapita ku misonkhano.

Nditabereka, ndinayambiranso ntchito, koma chidwi changa chovina chinali chitayamba kuchepa. Kusinthako kunayamba kuonekera, ndipo atolankhani anayamba kundinena. Nthawi zambiri ankandifunsa kuti: “Bwanji suvinanso ngati mmene unkavinira kale muja?” Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kudziwa chochita kuti ndisasemphane maganizo ndi azichimwene anga. Ndinali nditakhala mmodzi wa eni gululo, ndipo sindinkafuna kuyambana nawo.

Nditakhalanso woyembekezera, ndinauza Rafa, amene ankatsogolera gululo mchimwene wathu Pepe atamwalira, kuti ndinkafuna ndizikhala nthawi yaitali ndi ana anga ndipo ndikufuna kusiya ntchito yovina. Anandiuza kuti ndichite zimene ndikuona kuti n’zabwino kwa ine. Palibe mchimwene wanga aliyense amene anadana nane n’tayamba kuphunzira Baibulo, ndipo ndimayamikira kwambiri zimenezo.

Moyo Watsopano Wotumikira Yehova

Mu 1993, nditakhala zaka 10 m’gululo, ndinasiya ntchito yanga yovina ndipo ndinadzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova. Ndinakhala wofalitsa wa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo Roberto atachoka m’gululo, tinabatizidwa mu 1994. (Mateyu 24:14) Freddy ndi Julio, azichimwene a Roberto, anakhala Mboni. Manuel Pérez, woimba wina wa m’gululo, anakhalanso Mboni. Mpaka lero, onsewa akutumikirabe Yehova mokhulupirika.

Anthu ambiri sanamvetse chifukwa chimene ndinasiyira ntchito yovina, chifukwa ndinkaikonda kwambiri. Ena ankaganiza ngati momwe ankaganizira mkonzi wina wotchuka wa pa TV m’dziko mwathu, kuti ndikungopumira kaye ntchito yangayo. Iye anati: “Mofanana ndi anthu ena onse aluso, akapumapuma abwereranso.” Koma zimenezo sizinachitike. Ndinatsimikiza kudzipereka ndi mtima wonse kutumikira Yehova.

Tsopano tili ndi ana atatu: Katty, Roberto, ndi Obed. Timayesetsa kuwaphunzitsa kuti zinthu zofunika kwambiri m’moyo ndi zinthu zauzimu, osati chuma. Chifukwa cha zomwe taona pa moyo wathu, tingathe kuwachenjeza za zinthu zosokeretsa za m’dzikoli ndi kuwapatsa malangizo abwino owathandiza pamoyo wawo. Phunziro la Baibulo la banja lathu la mlungu ndi mlungu latipindulira kwambiri, ndipo latithandiza kukhala ogwirizana m’dziko limene mabanja ambiri akugawikana.

Tayesetsa kuphunzitsa ana athu kuti azimuona Yehova ngati munthu weniweni amene angamukhulupirire. (Miyambo 3:5, 6; Ahebri 11:27) Tawasonyezanso kufunika kopita ku misonkhano yachikristu ndi kutenga nawo mbali. Kuona ana anthu akukula m’njira ya choonadi cha m’Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali. Kwa zaka ziwiri zapitazi, ndatumikira monga mpainiya wothandiza, dzina limene Mboni za Yehova zimapatsa anthu amene amatha maola 50 kapena kuposa pamenepo mwezi uliwonse kuuza anthu ena zikhulupiriro zawo za m’Baibulo. Ndipo kwa zaka zingapo tsopano mwamuna wanga wakhala akutumikira monga mkulu mu mpingo wachikristu.

Ndimaonabe kuti merengue ndi mtundu wabwino kwambiri wa nyimbo zovina. Koma n’zomvetsa chisoni kuti nyimbo za merengue zambiri zimene zili zofala masiku ano n’zosiyana kwambiri ndi mmene zinalili kale. Kalelo, zambiri zinkakhala zabwino. Masiku ano, kuti tipeze nyimbo zabwino za merengue, timafunika kusankha mosamala kwambiri.

Ubwino Wotumikira Yehova

Munthu akhoza kupeza zinthu zambiri m’dzikoli, koma pamafunika kuganizira kaye komwe zonsezo zikuchokera. Zimenezi n’zoona pa ntchito yoimba, imene kunjaku ikhoza kuoneka yokopa ndiponso yopanda vuto lililonse. Koma zoona zake n’zoti siili choncho. Anthu ambiri ogwira ntchito imeneyi amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso amachita zachiwerewere. Kuimba nyimbo pagulu kumaika munthu pamalo amodzi ndi anthu amene amangofuna kusangalala pakadali panopa basi ndipo chikumbumtima chawo chinafa kalekale.—1 Akorinto 15:33.

Tazindikira kuti chinthu chabwino koposa zonse chimene munthu aliyense angachite ndicho kutumikira Yehova. Ndikukumbukira tsiku linalake nditabwerera ku hotela titamaliza kuimba bwino kwambiri, ndipo ndinkamva kuti moyo wanga unali wopanda phindu lililonse. Tsopano ndikudziwa kuti chifukwa chake chinali choti sitinali kupeza chosowa chathu chachikulu, chomwe ndi zinthu zauzimu.—Mateyu 5:3.

Cholinga chathu chachikulu m’moyo tsopano ndicho kusangalatsa Mlengi wathu, makamaka mwa kulalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu wake. (Mateyu 24:14; Machitidwe 20:35) Kuchita zimenezi kumachititsa banja lathu kukhala losangalala kwambiri. Ndifedi oyamikira kwambiri kukhala m’gulu la anthu a Mulungu ndi kukhala ndi mabwenzi enieni, abale ndi alongo a chikhulupiriro chofanana ndi chathu. Limodzi nawo, tili ndi chiyembekezo chochititsa chidwi chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.—Marko 10:29, 30; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Tinapeza chuma chambiri pantchito yathu yosangalatsa anthu. Koma chifukwa chodziwa Mulungu wathu, Yehova, tapeza chuma chauzimu chomwe chili chamtengo wapatali kuposa chuma china chilichonse. Ndife osangalala kwambiri kutumikira Mulungu wokhala ndi cholinga, Mulungu wachimwemwe amene amatipempha kuti timukhulupirire. (Salmo 37:3) Tikukhulupirira ndi mtima wonse kuti tapeza chinthu chabwino kwambiri kuposa kutchuka ndi chuma, ndipo tikupempha Yehova kuti atithandize, pamodzi ndi banja lathu, kuchita chifuniro chake kosatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Merengue ndi chamba cha nyimbo zovina mofulumira. Kale, oimba nyimbo za merengue ankakhala gulu la anthu ochepa ndipo ankaimbira zida zosiyanasiyana. Patapita nthawi, anayamba kupanga magulu a anthu ambiri. Masiku ano, magulu ambiri a merengue amaimba nyimbo zawozo pogwiritsa ntchito malipenga, ng’oma, ndi zida zina.

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili limodzi ndi anthu ena a m’gululo kumayambiriro kwa ntchito yanga

[Chithunzi patsamba 29]

Tikuimba ku New York City, cha m’ma 1990

[Chithunzi patsamba 31]

Tili kutsogolo kwa Nyumba ya Ufumu

[Chithunzi patsamba 31]

Chithunzi chaching’onocho: Tikuchita phunziro la Baibulo la banja