Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsogolo la Ntchito Zokopa Alendo

Tsogolo la Ntchito Zokopa Alendo

Tsogolo la Ntchito Zokopa Alendo

“Pali zitsanzo zochokera pafupifupi ku dziko lililonse, zosonyeza kuti ntchito zokopa alendo ndiye chinthu chachikulu chomwe chawononga zachilengedwe.”—Limatero buku lotchedwa An Introduction to Tourism, lolembedwa ndi Leonard J. Lickorish ndi Carson L. Jenkins.

KUWONJEZEKA kwa ntchito zokopa alendo sikuti kungangowononga zachilengedwe zokha, koma kungayambitsenso mavuto ena. Tiyeni mwachidule tione ena mwa mavuto amenewa. Kenaka tifotokoza momwe zidzathekere kuti m’tsogolo anthu azidzatha kupita kokaona dziko lathu lokongolali ndi kudziwa bwino zinthu zochititsa chidwi zomwe zilimo, makamaka anthu ake osangalatsa kucheza nawo.

Mavuto a Zachilengedwe

Kuchuluka kwa anthu okaona malo masiku ano kwabweretsa mavuto. Malinga ndi zimene ochita kafukufuku omwe mayina awo ndi Lickorish ndi Jenkins analemba, “alendo akuwononga nyumba yotchedwa Taj Mahal ku India. Ku Igupto, manda a mfumu za ku Igupto ooneka ngati zulu akuwonongekanso chifukwa cha kuchuluka kwa alendo amene amabwera kudzawaona.”

Kuwonjezera pamenepo, alembi amenewa anachenjezanso kuti kukaona malo kwachisawawa kungaphe kapena kuchepetsa zomera, dothi la m’malo osungirako zachilengedwe likamagangatika chifukwa cha kuchuluka kwa alendo. Kuwonjezera apo, zamoyo zikhoza kuyamba kutha alendo akamatenga zinthu monga ziganamba zosowa za nkhono ndi miyala yokongola ya pansi pa nyanja, kapena anthu a m’deralo akamasonkhanitsa zinthu zimenezi kuti azigulitse kwa alendo odzaona malo.

Alendo odzaona malo amasiya zinyalala, zokwana pafupifupi kilogalamu imodzi tsiku lililonse mlendo aliyense, malinga ndi ziwerengero za bungwe la UN Environment Programme. Ngakhale malo a kutali kwambiri akuoneka kuti akukumana ndi vuto limeneli. Lipoti laposachedwapa lochokera ku bungwe loteteza nkhalango lotchedwa Rainforest Action Network linati: “M’njira zimene anthu odzaona malo ku mapiri a Himalaya amakonda kudzera, mwangoti mbwee! zinyalala. Ndiponso nkhalango za m’mapiriwa zikusakazidwa ndi anthu apaulendo amene akumadulamo nkhuni zophikira zakudya kapena zotenthetsera madzi osamba.”

Kuwonjezera apo, anthu odzaona malo nthawi zambiri amawononga zinthu zambiri zimene anthu okhala kuderako akanagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo, James Mak analemba m’buku lake lotchedwa Tourism and the Economy kuti: “Anthu odzaona malo ku Grenada amawononga madzi owirikiza kaseveni kuposa amene anthu okhala m’dzikolo amawononga.” Iye anapitiriza kuti: “Mwachindunji kapena mwa njira zina, ntchito zokopa alendo n’zimene zimawononga pafupifupi theka la magetsi onse amene amagwiritsidwa ntchito ku Hawaii, ngakhale kuti pa avereji ndi munthu mmodzi yekha pa anthu eyiti alionse ku Hawaii amene ndi mlendo wodzaona malo.”

Ngakhale kuti anthu okaona malo angawononge ndalama zambiri kuti apite ku dziko losauka, zambiri mwa ndalamazo sizithandiza anthu a m’dziko losaukalo. Bungwe la World Bank linati mwina ndalama zosakwana theka la ndalama zimene ntchito zokopa alendo zimabweretsa n’zimene zimathandiza anthu a m’dziko limene alendowo apita. Zambiri zimabwerera ku mayiko olemera kudzera m’makampani akunja amene amakonza za maulendo ndi mahotela ndi malo ena amene eni ake ndi anthu akunja.

Kuwononga Chikhalidwe cha Anthu

Alendo olemera amene akukayenda ku dziko losauka akhoza kuwononganso chikhalidwe cha anthu a m’mayiko enawo mwina mosachita kuonekera, koma nthawi zina mochita kuonekeratu. Alendo odzaona malo nthawi zambiri amabweretsa katundu wamtengo wapatali kuti asangalale paulendo wawowo. Kwa anthu a kuderako, zimakhala zachilendo kwambiri kuona chuma chochuluka choncho. Anthu ambiri a kuderako amayamba kufuna katundu wamtengo wapataliyo koma sangathe kumukwanitsa popanda kusintha kwambiri moyo wawo, ndipo kusintha kumeneko kukhoza kuwononga kwambiri chikhalidwe chawo.

Potchulapo mavuto ena amene angabwere, Mak anati kuwonjezeka kwa ntchito zokopa alendo “kungachititse kuti anthu asiye chikhalidwe chawo. Kungayambitsenso kusemphana maganizo pa nkhani ya momwe malo ndi zinthu zina zachilengedwe zomwe n’za munthu aliyense m’mudzimo ziyenera kugwiritsidwira ntchito, ndipo kungawonjezere makhalidwe oipa, monga umbanda ndi uhule.”

Nthawi zambiri masiku ano, alendo odzaona malo amaona kuti akhoza kuchita chilichonse popanda chowaletsa, choncho amachita zinthu zimene sakanachita akanakhala kwawo limodzi ndi mabanja awo ndi anzawo. Motero khalidwe la chiwerewere la alendo odzaona malo lasanduka vuto lalikulu kwambiri. Potchulapo chitsanzo chimodzi chodziwika bwino, Mak anati: “Padziko lonse anthu akuda nkhawa kwambiri chifukwa cha momwe ntchito zokopa alendo zikuwonjezera uhule wa ana.” M’chaka cha 2004, bungwe lofalitsa nkhani pa TV la CNN linalengeza kuti: “‘Umboni wodalirika ukusonyeza kuti pali ana amene amakakamizika kuchita zachiwerewere okwana pakati pa 16,000 ndi 20,000’ ku Mexico, ‘makamaka m’madera a kufupi ndi mayiko ena, m’mizinda, ndi m’madera amene alendo odzaona malo amakonda kupita.’”

Ubwino Woyenda

Dziko lathuli ndi malo okongola kwambiri okhalamo, ndipo nthawi zonse pamakhala zinthu zochititsa chidwi kwambiri zomwe tingathe kuona, monga kulowa kwa dzuwa kokongola, kumwamba kowala kodzadza ndi nyenyezi, ndi zomera ndi zinyama zamitundumitundu. Kaya tikukhala kuti, timaona zina mwa zinthu zokongola zimenezi ndi zinthu zina zochititsa chidwi pa dziko lathuli. Komabe, zimakhala zosangalatsa kwambiri kupeza mpata woyenda n’kukaona zinthu zina zokongola padziko lapansili.

Ngakhale kuti alendo okaona malo amasangalala kwambiri ndi zinthu zochititsa chidwi zomwe amaona, ambiri amati chimene chimawasangalatsa kwambiri paulendo wawo wonsewo ndicho kudziwana ndi anthu a zikhalidwe zosiyana ndi zawo. Nthawi zambiri anthu akayenda amazindikira kuti zinthu zoipa zimene ankamva za anthu enawo si zoona. Kuyendako kumawathandiza kumvetsa bwino anthu a mitundu ndi zikhalidwe zina ndi kupeza anzawo atsopano abwino kwambiri.

Phunziro limene anthu ambiri okaona malo amaphunzira n’loti katundu si amene amachititsa munthu kukhala wosangalala. Chimene chili chofunika kwambiri ndi ubwenzi umene munthu ali nawo ndi anthu ena, kutha kusangalala ndi anzako ndiponso kupeza anzako atsopano. Nkhani inayake ya m’Baibulo imafotokoza momwe “zokoma” zomwe anthu “akunja” a ku Melita anachitira apaulendo a m’zaka 100 zoyambirira zinawathandizira pamene ngalawa ya apaulendowo inasweka kumeneko. (Machitidwe 28:1, 2) Kupita ku mayiko ena ndi kukumana ndi anthu a mitundu ina masiku ano kwathandiza anthu ambiri kuzindikira kuti ndifedi anthu a banja limodzi ndipo tikhoza kukhala limodzi mwamtendere pa dziko pano.

Masiku ano, ndi anthu ochepa amene amatha kupita kukaona malo osiyanasiyana pa dziko lapansili. Koma bwanji m’tsogolo? Kodi n’kutheka kuti anthu ambiri, mwinanso onse, adzakhala ndi mwayi woyenda maulendo oterowo?

Zimene Tingayembekezere M’tsogolo

Zoona zake n’zakuti, tonsefe ndife pachibale, anthu a banja limodzi. N’zoona kuti mwamuna ndi mkazi woyamba anafa, monga momwe anawachenjezera kuti zimenezo n’zimene zidzawachitikire akadzapanda kumvera Mulungu. (Genesis 1:28; 2:17; 3:19) Choncho ana awo onse, kuphatikizapo ifeyo masiku ano, timakalamba ndi kufa. (Aroma 5:12) Koma Mulungu akulonjeza kuti cholinga chake choyambirira choti padziko lapansi pakhale anthu amene amamukonda chidzakwaniritsidwa. Mawu ake amati: “Ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.”—Yesaya 45:18; 46:11; 55:11.

Tangoganizirani tanthauzo la mawu amenewo! Baibulo limalonjeza kuti mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29; Mateyu 6:9, 10) Pofotokoza momwe anthu adzakhalire m’tsogolo pa dziko lapansi, Baibulo limati: “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Tangoganizirani za mwayi wabwino kwambiri womwe tidzakhale nawo nthawi imeneyo woyenda padziko lonse lapansi n’kudziwa bwino zinthu zochititsa chidwi zomwe zilipo, makamaka anthu ake osangalatsa kwambiri. Panthawi imeneyo sitidzachita mantha poyenda! Anthu onse okhala padziko lapansi adzakhala anzathu, amene Baibulo limawafotokoza kuti “abale anu ali m’dziko.”—1 Petro 5:9.

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Chinthu chimodzi chimene chimasangalatsa kwambiri munthu akayenda ndicho kupanga ubwenzi ndi anthu a chikhalidwe china

M’tsogolo tidzatha kupita ku malo osiyanasiyana ndiponso kukumana ndi anthu osiyanasiyana