Kodi Akazi Azibisa Kukongola Kwawo?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Akazi Azibisa Kukongola Kwawo?
“AKAZI amakonda mafashoni,” anatero George Simonton, katswiri wokonza zinthu za m’fasho ndiponso pulofesa pa sukulu ya Fashion Institute of Technology ku New York. Iye anafotokoza kuti: “Akazi amafuna kuoneka mosiyana ndi ena, amakonda kudzikonzakonza ndiponso kudzikongoletsa . . . Ndikuganiza kuti potero amakhala akudzilemekeza okha ndiponso amakhala akupereka ulemu kwa anthu ena amene amakhala nawo pafupi.” Zoonadi, kwa nthawi yaitali akazi akhala akudzikometsera ndi cholinga chofuna kusonyeza ukazi wawo, kungodzikongoletsa, ndiponso kuti azimva kuti ndi ofunika.
Komabe, pazifukwa za chipembedzo, ena amadana nazo kuona akazi akudzikometsera. Tertullian yemwe anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 200 C.E. analemba kuti: “Akazi opemphera . . . ngati . . . anabadwa okongola, . . . asawonjezere kukongola kwawoko, koma ayesetse kukuchepetsa.” Ponena za zodzoladzola, iye anapitiriza kuti: “Akazi amachimwira Mulungu ngati amadzola mafuta kumaso kwawo, kufiiritsa masaya awo, kapena kutalikitsa nsidze zawo.” Ndipo anafotokoza kuti “zinthu zodzikongoletsera” zasiliva ndi zagolidi ndi “zida zokopera amuna.”
Masiku anonso, anthu ochuluka amadana kwambiri ndi kudzikongoletsa kwa akazi. Zipembedzo zina zimaletsa ngakhale kuvala zinthu ngati ndolo, zibangili, ndi zina zotero, kudzola zodzoladzola, kapena kuvala zovala zamaluwamaluwa. Kodi akazi achikristu ayenera kubisa kukongola kwawo kapena kodi akhoza kudzikongoletsa kuti azioneka bwino?
Mmene Mulungu Amaonera
Baibulo silinena zambiri pa nkhani yokhudza kuvala zinthu ngati zibangili, ndolo, ndiponso kudzola zodzoladzola. Komabe, pali umboni
wokwanira wosonyeza kuti Mulungu saletsa zinthu ngati zimenezi kapenanso mitundu ina ya kudzikometsera.Mwachitsanzo, pofotokoza za momwe anadalitsira Yerusalemu, Mulungu analankhula ngati kuti mzindawo unali mkazi, ndipo anati: “Ndinakukometseranso ndi zokometsera, . . . ndipo unali wokongola woposa ndithu.” (Ezekieli 16:11-13) Zokometsera zimenezi, ngakhale kuti zinali zophiphiritsa, zinali zinthu ngati zigwinjiri kapena kuti zibangili, unyolo wa m’khosi kapena kuti mkanda, ndi maperere kapena kuti ndolo. Malemba amayerekezeranso zokometsera za golidi ndi “wanzeru wodzudzula” amene anthu amasangalala kumvetsera mawu ake. (Miyambo 25:1, 12) Choncho m’pomveka kunena kuti ngati malemba akugwiritsa ntchito zinthu zimenezi poziyerekezera ndi zinthu zabwino, ndiye kuti Mulungu sangaletse akazi kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi podzikongoletsa.
Akazi Achikristu Amadzikometsera
Malemba ena a m’Baibulo amafotokoza mwachindunji nkhani ya kudzikometsera kwa akazi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera.” Ngati akazi achita zimenezi mwa “manyazi, ndi chidziletso,” zimasonyeza kuti amaopa Mulungu. (1 Timoteo 2:9, 10) Akazi akamadzikongoletsa modziletsa choncho, zimapereka ulemu ku ziphunzitso za Mulungu ndi ku mpingo.
Koma ena amatsutsa kuti lemba lomweli limanena kuti kudzikometsera kusakhale kwa “tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti akazi sayenera kukonza tsitsi lawo kapena kuti sayenera kuvala zinthu ngati ndolo, zibangili, ndi zina zotero?
Ayi, sizikutanthauza zimenezo, chifukwa Baibulo limanena zinthu zosonyeza kuti silidana ndi kudzikometsera. Palemba limeneli, Paulo sankaletsa kudzikometsera ndi zinthu zinazake koma ankalimbikitsa akazi kuti ayenera kudzikometsera ndi makhalidwe achikristu ndi ntchito zabwino.
Chofunika Kwambiri N’cholinga Chake
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chom’punthwitsa.” (Aroma 14:13) Kodi lemba limeneli likukhudzana bwanji ndi zodzikongoletsera zimene timasankha?
Choyamba, Paulo akutiuza kuti “tisaweruzanenso wina mnzake.” Tiyenera kuyesetsa kuti ‘tisaike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wathu.’ Zinthu zimene zili zoyenera zingasiyanesiyane malinga ndi dera ndi chikhalidwe cha kuderalo. Zinthu zimene zingakhale zololeka panthawi ina ndi kudera kwina, zingakhale zosaloleka panthawi ina ndiponso kudera lina. Tisakhumudwitse ena podzikongoletsa m’njira imene anthu a kumalo kumene tikukhala amaona kuti ndi mmene amadzikongoletsera anthu a khalidwe loipa. Akazi oopa Mulungu ayenera kudzifunsa kuti: Kodi zimene ndimavala anthu a m’dera lathu amaziona bwanji? Kodi anthu a ku mpingo kwathu ndimawachititsa manyazi kapena kuwadabwitsa ndi zimene ndimavala? Ngakhale kuti mkazi wachikristu akhoza kukhala ndi ufulu wovala kapena kudzikongoletsa m’njira inayake, angafunikire kusintha ngati kudzikongoletsa koteroko kungakhumudwitse ena.—1 Akorinto 10:23, 24.
Ndiponso, kuganizira kwambiri za kudzikongoletsa kungayambitse mtima woipa. M’madera ambiri masiku ano akazi ena amadzikongoletsa mwachikoka kuti azikopa amuna. Komabe, akazi achikristu amapewa kotheratu kudzikongoletsa kotere, ndipo amayesetsa kukhala odziletsa, odekha m’zochita zawo, “kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.”—Tito 2:4, 5.
Akazi oopa Mulungu amazindikira kuti mulimonse mmene angadzikongoletsere, kukongola kwawo kwenikweni ndi kwa “munthu wobisika wamtima” ndipo kumaonekera mwa khalidwe lawo ndi mmene amachitira zinthu. (1 Petro 3:3, 4) Mkazi amene amasankha mwanzeru zovala zake, zodzoladzola zake, ndiponso ndolo, zibangili ndi zina zotero zimene amavala, amapatsidwa ulemu ndiponso amalemekeza Mlengi wake.