Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

“Popeza ndine wamanyazi, ndimangopita pa kompyuta n’kucheza ndi anthu pa Intaneti amene sindikanatha kucheza nawo maso ndi maso. Iwowo sadziwa kuti ndine ndani.”—Anatero Peter. *

“Pa Intaneti, munthu umaona kuti ndiwe womasuka kunena zilizonse zimene ukufuna.”—Anatero Abigail.

PA INTANETI pali “malo” ena ake ochezera amene anthu awiri amatha kumacheza mwa kutumizirana mauthenga kudzera pa kompyuta. Malo ochezera amenewa amalola anthu ambirimbiri kumatha kuwerenga ndi kuyankhana mauthenga wina ndi mnzake.

Malo ena ochezera amakhala osangalatsa kwambiri makamaka kwa achinyamata amene amagwiritsa ntchito Intaneti. Achinyamata mamiliyoni ambirimbiri a zikhalidwe zosiyanasiyana amacheza tsiku lililonse pa nkhani iliyonse imene akufuna. Sukulu zinanso zayamba kugwiritsa nawo ntchito njira imeneyi. Mwachitsanzo, ana a sukulu ku United States moyang’aniridwa ndi aphunzitsi awo, amatha kumakambirana nkhani zokhudza chikhalidwe ndi ana a sukulu anzawo amene ali ku Spain, England, kapenanso kumayiko ena. Ophunzira ena amathanso kumakambirana ndi mainjiniya odziwa bwino ntchito yawo, akatswiri a sayansi, kapenanso akatswiri ena zokhudza ntchito imene awapatsa m’kalasi mwawo.

Anthu ambiri amene amagwiritsa ntchito malo ochezera amenewa, sikuti onse amapitira kukakambirana nkhani zokhudza maphunziro zokhazokha. Ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti, kodi ndi misampha iti imene muyenera kusamala nayo?

Malo Amene Achidyamakanda Amakonda

Abigail akuti: “Ndinali kucheza ndi anthu ena pa Intaneti pamene mwamuna wina anandifunsa ngati ndikudziwapo anthu alionse amene ali ndi zaka 14. Mwamunayo amafuna kugona nawo. Anati ndi wokonzeka kuwapatsa ndalama kuti agonane nawo.”

Zimene Abigail anakumana nazozi si zachilendo ayi. Vuto loti achidyamakanda amakonda kugwiritsa ntchito Intaneti ndi lofala kwambiri moti maboma ena akonza malangizo othandiza achinyamata okhudza mmene angadzitetezere. Mwachitsanzo, ku United States bungwe la Federal Bureau of Investigation (FBI) linatulutsa buku lochenjeza za anthu amene amati akangoyamba “kulankhula” ndi wina pa Intaneti, amakamba nkhani zokhudza kugonana. Limachenjezanso za anthu amene “amayamba kunyengerera anthu ena pang’onopang’ono mwa kuwasonyeza kuti ali nawo chidwi, amawakonda, ndi achifundo, ndiponso mwina kuwapatsa mphatso kumene.”

Pofotokoza njira zimene ena mwa achidyamakanda amenewa amagwiritsa ntchito, a FBI anati: “Amakhala omvetsera kwambiri ndipo amasonyeza ngati kuti akufuna kuthandiza anawo pa mavuto amene akukumana nawo. Amafufuza nyimbo zimene zangotuluka kumene, ndiponso zinthu zina zimene ana amakonda. Anthu amenewa amayamba kuchotsa mantha mwa anawo pang’onopang’ono mwa kulowetsa timawu ndiponso nkhani zokhudza kugonana mwapang’onopang’ono pamene akucheza pa Intaneti.”

Sikuti ndi anthu akuluakulu opotoka maganizo okha amene amagwiritsa ntchito njira zotere. Muyeneranso kukhala osamala kwambiri ndi achinyamata amene sadziwa chilichonse chokhudza Baibulo kapenanso amene salemekeza mfundo zake za makhalidwe abwino. Tamvani zimene wachinyamata wina dzina lake Cody anakumana nazo. Anali kucheza ndi achinyamata ena pa Intaneti pamene mtsikana wina anam’pempha kuti apite pamalo ena pa Intanetipo pamene akhoza kukambirana zachinsinsi. Ndiyeno mtsikanayo anam’funsa funso lokhudza zakugonana. Koma Cody chifukwa chotha kudziletsa anasiya kucheza naye nthawi yomweyo.

Chifukwa chakuti mwachibadwa timasangalala ndi zinthu zokhudza kugonana, kusiya kucheza mwamsanga ngati mmene anachitira Cody kungakhale kovuta kwambiri. Peter, amene tamutchula koyambirira uja anati: “Ndinkaganiza ngati kuti ndine munthu wotha kudziletsa kwambiri kuti ndikhoza kusiya kuchezako ngati titayamba kukamba nkhani yokhudza zakugonana. Koma nthawi ndi nthawi ndinkapezeka kuti tikukambirana nkhani zokhudzana ndi kugonana. Pamapeto pake, ndinkadziimba mlandu.” Mwina mungadzifunse kuti, ‘Ngati ndimadzibisa tikamacheza pa Intaneti, kodi pali kulakwika kulikonse ngati titamakambirana nkhani zokhudza kugonana?’

Kodi Kukambirana Zogonana pa Intaneti Nkoipa?

Baibulo limanena mosabisa za kugonana. (Miyambo 5:18, 19) Zoona zake n’zakuti, anthu amafunitsitsa kudziwa zakugonana panthawi ya unyamata. Choncho sikulakwa kukambirana nkhani za kugonana. Mufunika kupeza mayankho a mafunso amene mumakhala nawo okhudza nkhani yofunika imeneyi. * Komabe, dziwani kuti njira imene mungagwiritse ntchito kupezera mayankho a mafunso anu okhudzana ndi zakugonanawo, idzakhala ndi zotsatira zake zimene zidzakhudza chimwemwe chanu ponse pawiri, nthawi inoyi ndiponso mtsogolo.

Ngati musankha kukambirana nkhani zokhudza kugonana pa Intaneti, ngakhale muchite zimenezi ndi anthu amene mumati ndi anzanu, zotsatirapo zake zingakhale zofanana ndi za m’nyamata amene anamufotokoza m’Baibulo uja. Chifukwa cha chidwi, iye anadutsa pafupi ndi nyumba ya hule. Poyamba, anangolankhula naye. Koma chilakolako chake chitadzuka, kulankhulana kokha kunali kosakwanira. “Mnyamatayo am’tsata posachedwa, monga ng’ombe ipita kukaphedwa, . . . monga mbalame yothamangira msampha.”—Miyambo 7:22, 23.

Mofananamo, kukambirana nkhani zokhudza kugonana pa Intaneti kungakupangitseni mosavuta kufuna kuchitadi zimene mukukambiranazo pofuna kuziziritsa mtima. Mnyamata wina dzina lake Philip akufotokoza kuti: “Pamene ndinali kucheza pa Intaneti ndi munthu winawake, ndinangoona chithunzi chosonyeza zolaula chaonekera pa kompyuta yanga. Munthu amene ndimacheza nayeyo ndi amene anachitumiza pa kompyuta yangayo.” Chilakolako chanu chofuna kuona ndi kuganiza zinthu zokhudza kugonana chikadzuka, mukhoza kugwa m’chiyeso chofuna kudziwa zambiri monga kupita malo ena pa Intaneti amene anakonzera anthu akuluakulu okhaokha. * Anthu ambiri amene agwapo mu msampha woonerera zithunzi zolaula amafika mpaka pochita chiwerewere ndipo kenako amavutika ndi zotsatira zake zopweteka.—Agalatiya 6:7, 8.

Anthu amene amafuna kukambirana nanu zakugonana pa Intaneti sikuti amakhala ndi zolinga zabwino ayi. Anthu oipa amenewa amangofuna kukunyengererani kuti muzikambirana nkhani zakugonana ndipo kenako mudzagonane nawo kuti adzakhutiritse zokhumba zawo. * Mfumu Solomo pofuna kuteteza mwana wake kwa munthu wachiwerewere analemba kuti: “Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo, osayandikira ku khomo la nyumba yake; kuti ungapereke ulemu wako kwa ena, . . . kuti mphamvu yako isakhutitse alendo.” (Miyambo 5:8-10) Mfundo imene ili mu lemba limeneli tikhoza kuigwiritsa ntchito mwanjira iyi: Musayandikire pafupi ndi malo ochezera pa Intaneti pamene pamakambidwa nkhani zakugonana, kuti musapereke ulemu wanu kwa anthu oipa amene amangofuna kukhutiritsa zokhumba zawo pa inu.

Anthu Amene Amabisa Zolinga Zawo

Mwina munganene kuti simufuna kukambirana nkhani zokhudza kugonana pa Intaneti. Mofanana ndi Peter ndi Abigail amene tawatchula koyambirira aja, mukhoza kumaona malo ochezera a pa Intaneti kukhala malo amene mukhoza kumacheza ndi anthu ena koma osadziulula kuti ndinu ndani kwenikweni, ndiponso popanda kuchita manyazi. * Koma ngakhale zili choncho, pali msampha wina umene mufunika kusamala nawo.

Khalidwe losafuna kudziulula limeneli lingakupangitseni kukhala munthu wachinyengo. Abigail akuti: “Ndinkati ndikayamba kucheza ndi anthu kenako ndimasintha n’kudzipanga kukhala ngati munthu winawake kuti ndigwirizane ndi zimene tikukambiranazo.” Mofanana ndi Abigail, nanunso mungamadziyerekezere kukhala ngati anthu a khalidwe linalake kuti muyenerane ndi gulu la anthu amene amachezera mbali imeneyo pa Intanetipo. Mukhoza kuyamba kutengera chinenero chawo kapena zokonda zawo ndi cholinga chakuti mupange mabwenzi atsopano. Komanso mukhoza kuyamba kuona malo ochezera pa Intaneti kukhala malo amene mungamasuke kunena zakukhosi kwanu, zimene mukuganiza kuti makolo anu kapena anzanu sangagwirizane nazo. Mulimonsemo, mapeto ake mumapezeka kuti mukunamiza limodzi mwa magulu awiriwa. Mukamadziyerekezera kukhala ngati munthu winawake mukamacheza pa Intaneti, ndiye kuti mukunamiza anzanu amene mukucheza nawowo. Kwinaku, ngati simufotokozera anthu a m’banja mwanu ndi mabwenzi anu zakukhosi kwanu, ndiye kuti mukuwanamizanso.

Ngakhale kuti malo ochezera a pa Intaneti ndi chinthu chatsopano, anthu anayamba kunama kalekale. Baibulo limanena za amene anayambitsa mabodza, Satana Mdyerekezi, kuti ndiye anayambitsa machenjera amene amachita anthu ena omwe amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Iye asananene bodza lake loyamba, anayamba wadzibisa kaye. (Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9, 10) Kutsatira chitsanzo cha Mfumu Davide kungakuthandizeni kupewa kunamizidwa ndi anthu abodza. Iye analemba kuti: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika,” kapena kuti obisa zolinga zawo.—Salmo 26:4.

Monga mmene taonera koyambirira kuja, malo ena ochezera a pa Intaneti ndi othandiza kwambiri. Komabe, achinyamata amene akufuna kusangalatsa Yehova, ayenera kukhala osamala kwambiri pamene akugwiritsa ntchito njira yamakono yolankhulirana imeneyi. Ngati mukufuna kukhala nayo, mwachitsanzo kuti muzikambirana zinthu zakusukulu, muzipempha makolo anu kapena munthu wina wokhwima mwauzimu kuti azikhala nanu pamene mukukambirana. Nkhani ya m’tsogolo idzapereka zifukwa zina ziwiri zosonyeza chifukwa chake muyenera kukhala osamala kwambiri pamene mukufuna kuyamba kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Idzafotokozanso mmene mungachitire ndi mavuto amene mungakumane nawobe ngakhale mutamachita zinthu mosamala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 15 Buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza lili ndi malangizo abwino ochokera m’Baibulo okhudza za kugonana ukwati usanachitike, psotopsoto, ndi mitu ina yofanana ndi imeneyi.

^ ndime 17 Pali malo ena ochezera pa Intaneti amene amati ndi a anthu akuluakulu okhaokha ndipo salola munthu wa zaka zochepa kupita pa malo amenewo. Izi zili choncho chifukwa nthawi zambiri, nkhani zake ndiponso zithunzi zimene amatumizirana zimakhala zolaula. Komabe, kafukufuku akusonyeza kuti achinyamata aang’ono kwambiri mpaka azaka naini amanama kuti ali ndi zaka zambiri pofuna kuti apeze chilolezo choti azitha kugwiritsa nawo ntchito malo ochezera a anthu akuluakulu.

^ ndime 18 Popeza kuti pa Intaneti simungathe kum’dziwa bwinobwino munthu amene mukukambirana naye, m’posavuta kukunamizani kuti munthuyo ndi wamkazi kapena wamwamuna koma pamene zoona zake zenizeni n’zakuti ndi mwamuna mnzanu kapena mkazi mnzanu.

^ ndime 20 Buku lolangiza makolo lakuti A Parent’s Guide to Internet Safety limanena kuti amene amacheza pa Intaneti asamatchule dzina lawo, adiresi, kapena nambala yawo ya telefoni kwa anthu achilendo amene amacheza nawo pa Intanetipo.

[Chithunzi pamasamba 13, 14]

Kucheza pa Intaneti kungakhale koopsa