Kupereka Umboni Wabwino ku Sukulu
Kupereka Umboni Wabwino ku Sukulu
Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Mexico
PAMENE Daniel, mnyamata wa zaka 17, amakayamba sukulu m’kalasi yatsopano anali wokonzeka kukadziwitsa anzake a m’kalasiyo kuti iye ndi wa Mboni za Yehova. Mwayi unapezeka pamene aphunzitsi amene amaphunzitsa Chingelezi anauza ana a m’kalasimo kuti azikafufuza alendo amene chilankhulo chakwawo chili Chingelezi ndipo akawapeza aziwafunsa mafuso. Cholinga cha aphunzitsiwo chinali chakuti anawo azipita malo amene alendo amakonda kupitako mu mzinda wa Mexico City, ndipo akawapeza aziwafunsa mafunso n’kujambula pa vidiyo zomwe akufunsazo kenako azikafotokoza zimene anajambulazo m’kalasi.
Daniel anaganiza zopita ku likulu la Mboni za Yehova ku Mexico kukafunsa m’mishonale aliyense wogwira ntchito pa malowo amene amalankhula Chingelezi ndipo anakonzanso zojambuala vidiyo ya m’Chingelezi yosonyeza zinthu zina ndi zina za pamalowo. Iye anakonzanso zoti akachite chionetsero cha timabuku tosiyanasiyana tofalitsidwa m’zinenero za eni nthaka ku Mexico ndiponso Nsanja za Olonda ndi Galamukani! zolembedwa m’zinenero zina. Kenako, Daniel anapempha aphunzitsi ake a Chingelezi aja kuti aonetse vidiyo ija ndiponso kuti achite chionetsero cha zinthu zimene anatenga zija.
Anzake a m’kalasimo pamodzi ndi aphunzitsi aja, anadabwa kwambiri kuona ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita ku Mexico. Anthuwo anachita chidwi kwambiri makamaka chifukwa cha mmene Mbonizo zikuyesetsera kufikira eni nthaka ku Mexico.
Atamaliza kuwaonetsa vidiyoyi imene anapeza nayo malikisi ambiri, yomwe inatenga mphindi 25, Daniel anagawira anthu onsewo magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso buku lakuti: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Ambiri analandira mabukuwa ndipo zimenezi zatsegula mwayi waukulu wokambirana za Baibulo. Ndipo Daniel akuti: “Ndikuthokoza Yehova kuti ndinatha kulemekeza dzina lake kudzera mu ntchito yosavuta ya kusukulu.”