Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyanja ya Pinki?

Nyanja ya Pinki?

Nyanja ya Pinki?

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Senegal

KODI nyanja ingakhaledi ya pinki? Nyanja ya Retba imatchedwa kuti Nyanja ya Pinki, ndiye popeza kuti ili pa mtunda wa makilomita 30 kuchokera kunyumba kwathu kuno, ku Dakar, Senegal, kumadzulo kwa Africa, taganiza zopita kumeneko kuti tikaone ngati nyanja imeneyi ikuyenera kukhaladi ndi dzina limeneli. Tsopano tafika, tikuona madzi akunyezimira chifukwa cha dzuwa. Kunena zoona, nyanjayi ikuonekadi ya pinki ndipo ndi yokongola kwambiri. Amene akutionetsa malowa akufotokoza kuti dzuwa likawomba pamadziwa, tinthu tinatake tamoyo timene n’tosatheka kutiona ndi maso timasintha mtundu ndiyeno pamenepa m’pamene pamabwerera mtundu wokongolawu. Komabe, kuno kuli zambiri zoti n’kuona osati mtundu wa nyanja wokhawu.

Pansi pa nyanjayi m’malo amene ali osazama kwambiri pali thanthwe la mwala wa mchere. Madzi ake ndi a mchere kwambiri moti munthu umatha kumangoyandama osasambira ndipo alendo ena amapezerapo mwayi woyandama panyanja imeneyi.

Choncho n’zosachita kufunsa kuti Nyanja ya Pinki imeneyi imathandiza anthu ambiri kupeza ndalama. Mwachitsanzo: (1). M’mphepete mwa nyanjayi, muli antchito amene akupakira mchere m’mathiraki. Tayamba taima kaye pang’ono ndipo tikuona mmene anthu akuchotsera mchere m’nyanjayi. Tikuona anthu aimirira m’madzi amene akuwalekeza m’chifuwa, ndipo anthuwa akukumba mchere pogwiritsa ntchito mapiki ataliatali. Akatero akumauika m’mabasiketi n’kukaupakira m’bwato. Mmodzi wa ogwira ntchitowa watiuza kuti, pamatenga maola atatu kuti akumbe mchere wokwana tani imodzi. Mabwato amawadzadza kwambiri moti amayandama pang’onopangono movutikira (2). Mabwatowa akafika kumtunda, azimayi amatsitsa mcherewu n’kuusenza pamutu m’ndowa (3). Amagwira ntchito imeneyi mogwirizana pamodzi ngati mmene amachitira makina aakulu onyamulira katundu.

Ulendo wathuwu unali ulendo wosangalatsa kwambiri. Nyanja ya pinki ndi imodzi mwa zinthu zosangalatsa zomwe zili padziko lathuli lomwe ndi mphatso ya mtengo wapatali yochokera kwa Yehova.—Salmo 115:16.

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Photo by Jacques CLEMENT, Clichy, FRANCE at http://community.webshots.com/user/pfjc