Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Logawanika Chifukwa cha Chuma

Dziko Logawanika Chifukwa cha Chuma

Dziko Logawanika Chifukwa cha Chuma

KUYAMBIRA m’ma 1940 mpaka m’ma 1980, dziko linagawanika patatu pa nkhani za ndale. Panali chidani chachikulu pakati pa mayiko amene ankatsatira chikomyunizimu, motsogozedwa ndi dziko la Union of Soviet Socialist Republics (USSR), ndi mayiko amene sankatsatira chikomyunizimu, motsogozedwa ndi dziko la United States. Mfundo zodzipatula za dziko la USSR zinawonjezera kusagwirizana kumeneku. Mayiko amene sanali ku mbali ziwiri zimenezi anali m’gulu laokhanso lachitatu.

Mayiko ambiri a m’gulu lachitatuli anali osauka. Choncho m’kupita kwa nthawi, pofuna kusiyanitsa mayikowa ndi mayiko a m’magulu awiri aja, anthu anayamba kuwatchula kuti mayiko osauka.

Panopa, dziko lapansi sililinso logawanika patatu pandale ngati mmene linalili kalelo. Komabe, pankhani ya chuma ndiponso ya ntchito za mafakitale, kusiyana pakati pa mayiko olemera ndi osauka kukadalipobe. Anthu odzaona malo ochokera m’mayiko olemera amakumana ndi anthu osauka amene akuvutika ngakhale kupezera mabanja awo chakudya.

Choncho, m’pofunikadi kufunsa funso loti: Kodi dzikoli lidzakhalabe logawanika chifukwa cha chuma mpaka kalekale, kapena kodi zingatheke kuti anthu opeza bwino ndi anthu osauka ayambe kukhala moyo wopeza mofanana?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© Qilai Shen/Panos Pictures