Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limapondereza Akazi?

Kodi Baibulo Limapondereza Akazi?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Baibulo Limapondereza Akazi?

TERTULLIAN, anali munthu wa maphunziro apamwamba a zaumulungu amene anakhalapo zaka pafupifupi 1,800 zapitazo. Iyeyu analembapo kuti akazi ndi “polowera mdyerekezi.” Anthu ena agwirapo mawu a m’Baibulo posonyeza kuti akazi ndi anthu osafunika kwenikweni powayerekezera ndi amuna. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amaona kuti Baibulo limapondereza akazi.

Elizabeth Cady Stanton, mzimayi wa m’zaka za m’ma 1800 amene anapititsa kwambiri patsogolo ufulu wa akazi ku United States, anati: “Baibulo ndiponso matchalitchi ndizo zimene zabwezera m’mbuyo kwambiri ntchito yolimbikitsa ufulu wa akazi.” Ponena za mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo, Stanton nthawi inayake anati: “Palibenso mabuku ena amene amaphunzitsa kwambiri za kupondereza ndi kunyoza akazi kuposa amenewa.”

Ngakhale kuti anthu ena masiku ano ali ndi maganizo onyanyira ngati amenewo, anthu ambiri amakhulupirirabe kuti mbali zina za Baibulo zimalimbikitsa kupondereza akazi. Kodi maganizo amenewa ali ndi maziko alionse?

Zimene Malemba Achihebri Amanena Zokhudza Akazi

“Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Anthu otsutsa amati lemba limeneli n’chiweruzo cha Mulungu kwa Hava ndipo likusonyeza kuti Mulungu amavomereza zoti amuna azipondereza akazi. Komabe, amenewa ndi mawu olondola ofotokoza zinthu zomvetsa chisoni zomwe zinayamba kuchitika chifukwa choti anthu anachimwa ndiponso anakana kulamulidwa ndi Mulungu, osati mawu ofotokoza maganizo a Mulungu. Kuzunza akazi kunayamba chifukwa cha kuchimwa kwa munthu, osati chifukwa cha chifuniro cha Mulungu. Zoonadi, akazi m’zikhalidwe zosiyanasiyana aponderezedwadi ndi azimuna awo, ndipo nthawi zambiri amazunzidwanso. Koma chimenechi sichinali cholinga cha Mulungu.

Adamu ndi Hava anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. Ndiponso Mulungu anawapatsa lamulo lofanana, loti abalane, adzaze dziko lapansi, ndi kuligonjetsa. Anafunika kuchitira zinthu limodzi mogwirizana. (Genesis 1:27, 28) Mwachionekere, panthawi imeneyo palibe aliyense wa awiriwo amene anali kupondereza mnzake mwankhanza. Lemba la Genesis 1:31 limati: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”

Nthawi zina nkhani za m’Baibulo sizisonyeza maganizo a Mulungu pankhaniyo. Mwina nkhanizo zimangokhala zofotokoza zinthu zomwe zinachitika. Nkhani yonena za nthawi imene Loti anapereka ana ake aakazi kwa anthu a ku Sodomu inafotokozedwa popanda kusonyeza ngati Mulungu anagwirizana nazo kapena ayi, kapenanso kusonyeza chiweruzo chake. *Genesis 19:6-8.

Zoona zake n’zakuti, Mulungu amadana ndi kuponderezana ndiponso kuzunzana kwa mtundu uliwonse. (Eksodo 22:22; Deuteronomo 27:19; Yesaya 10:1, 2) Chilamulo cha Mose chinaletsa kugwiririra akazi ndi kuchita uhule. (Levitiko 19:29; Deuteronomo 22:23-29) Chigololo chinaletsedwa, ndipo anthu akapezeka akuchita chigololo, chilango chake chinali choti onse awiri aphedwe. (Levitiko 20:10) M’malo mopondereza akazi, Chilamulo chinawalemekeza ndi kuwateteza kuti asamadyeredwe masuku pamutu, zomwe zinali zofala m’mitundu yowazungulira. Mkazi wachiyuda wodziwa ntchito yake anali munthu wolemekezeka ndiponso wofunika kwambiri. (Miyambo 31:10, 28-30) Aisrayeli analephera okha kutsatira malamulo a Mulungu oti azilemekeza akazi, ndipo ichi sichinali chifuniro cha Mulungu. (Deuteronomo 32:5) Pamapeto pake, Mulungu analanga mtundu wonsewo chifukwa cha kusamvera kwawo kwadalako.

Kodi Kugonjera N’kuponderezedwa?

Pagulu lililonse la anthu, zinthu sizingayende bwino ngati palibe dongosolo labwino lochitira zinthu. Zimenezi zimafuna kuti pakhale anthu enaake otsogolera. Kupanda kutero, pamakhala chisokonezo. “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.”—1 Akorinto 14:33.

Mtumwi Paulo anafotokoza umutu wa m’banja motere: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Aliyense, kupatulapo Mulungu, amagonjera winawake wamkulu kuposa iyeyo. Kodi popeza Yesu ali ndi mutu ndiye kuti akuponderezedwa? Ayi! Motero, popeza m’Malemba amuna anapatsidwa udindo woti azitsogolera ku mpingo ndi m’banja sizitanthauza kuti akazi akuponderezedwa. Kuti zinthu ziyende bwino m’banja ndi mu mpingo, akazi ndi amuna amafunika kugwira ntchito imene apatsidwa mwachikondi ndiponso mwaulemu.—Aefeso 5:21-25, 28, 29, 33.

Yesu nthawi zonse ankapatsa akazi ulemu. Iye sanatsatire miyambo ndi malamulo opondereza amene Afarisi ankaphunzitsa. M’malo mwake, iye ankalankhula ndi akazi, ngakhale amene sanali Ayuda. (Mateyu 15:22-28; Yohane 4:7-9) Ankaphunzitsa akazi. (Luka 10:38-42) Anateteza akazi kuti asasiyidwe ndi amuna awo n’kukhala opanda owathandiza. (Marko 10:11, 12) Mwina chinthu chimene chinali chosiyana kwambiri ndi zimene anthu ena onse ankachita panthawi imeneyo n’choti Yesu anali ndi anzake apamtima aakazi. (Luka 8:1-3) Monga munthu amene anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe onse a Mulungu, Yesu anasonyeza kuti anthu onse ndi ofanana pamaso pa Mulungu, kaya akhale akazi kapena amuna. Ndipotu, pakati pa Akristu oyambirira, amuna ndi akazi analandira mphatso ya mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4, 17, 18) Kwa anthu odzozedwa amenewo, amene amakakhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Kristu, sakhalanso osiyana kuti uyu ndi wamkazi kapena wamwamuna akaukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba. (Agalatiya 3:28) Mlembi wa Baibulo, Yehova, sapondereza akazi.

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 28]

Mosiyana ndi anthu ambiri a mu nthawi yake, Yesu ankalemekeza akazi