Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingapewe Bwanji Mavuto Pocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

Kodi Ndingapewe Bwanji Mavuto Pocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingapewe Bwanji Mavuto Pocheza ndi Anthu Osawadziwa pa Intaneti?

“Nthawi zambiri ndinkacheza pa Intaneti kwa maola atatu kapena anayi patsiku. Masiku ena ndinkacheza mpaka maola sikisi kapena seveni osapuma.”​—Anatero José. *

MALO OCHEZERA PA INTANETI ali ngati malo ena aliwonse amene munthu angachezerepo ndi anthu oti sakuwadziwa, motero amakhala ndi zinthu zoopsa zimene muyenera kuzidziwa. Tifanizire motere: ngati mutapita mumzinda winawake waukulu, mwanzeru, mungayesetse kuchita zinthu zosaika moyo wanu pachiswe podziwa ndi kupewa madera amene ali oopsa.

Nzeru zomwezi n’zimene muyenera kutsatira musanatsegule malo ena alionse ochezera pa Intaneti. Mu Galamukani! ya October 8, anatchulamo zoopsa ziwiri zomwe zimakonda kupezeka m’malo oterewa. Choyamba n’chakuti mungathe kuyamba kucheza ndi achidyamakanda ndipo china n’chakuti inuyo panokha mungathe kuyamba khalidwe lachinyengo. Palinso zoopsa zina zofunika kuziganizira. Koma poyamba, tiyeni tidziwe kuti kodi malo ochezera a pa Intaneti amawakonza m’njira yotani?

Amawakonza N’cholinga Chinachake

Nthawi zambiri malo amenewa amakhala ndi nkhani zosanjidwa moti zizikopa anthu osiyanasiyana mogwirizana ndi zokonda zawo. Ena amakhala okopa anthu okonda masewera kapena zochitika zinazake. Ena amangokhala ongochezerapo nkhani zokhudza pulogalamu inayake ya pa TV. Ndipo ena amakhala okhudza anthu amene amati ali chipembedzo chinachake.

Ngati inuyo muli wa Mboni za Yehova, mungathe kukopeka kuti mutsegule malo a pa Intaneti amene akuti achinyamata a Mboni a padziko lonse angathe kudziwaniranapo. N’zoona kuti ndi bwino kumalakalaka kukhala ndi anzanu a chipembedzo chanu. Koma malo a pa Intanetiwa ali ndi zinthu zambiri zobisika zomwe zingathe kuvulaza Akristu. Kodi zinthu zake n’zotani?

Amawononga Khalidwe

Mnyamata wina dzina lake Tyler anati: “Ndinali pa malo enaake pamene ndimacheza ndi anthu omwe ineyo ndinkangoti onse ndi Mboni za Yehova. Koma kenaka ena mwa anthuwa anayamba kunyoza zikhulupiriro zathu. Posakhalitsa ndinadziwa kuti kwenikweni anthuwa anali opanduka.” Inde, amenewa anali anthu omwe cholinga chawo chenicheni chinali chofuna kuwononga khalidwe la anthu amene ankawanamiza kuti ndi Amboni anzawowo.

Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anachenjeza kuti ena mwa anthu amene ankamutsatira adzatembenuka n’kuyamba kulimbana ndi okhulupirira anzawo. (Mateyu 24:48-51; Machitidwe 20:29, 30) M’masiku ake, mtumwi Paulo anawatcha anthu oterewa kuti abale abodza ndipo anati ‘analowera m’tseri’ kudzavulaza anthu a mumpingo wachikristu. (Agalatiya 2:4) Yuda m’buku lake la m’Baibulo, analemba kuti iwowa “anakwawira m’tseri” n’cholinga choti ‘asandutse chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.’ (Yuda 4) Yuda analongosolanso kuti anthuwa ali ngati “miyala yaikulu yobisika pansi pa madzi.”—Yuda 12, NW.

Onani kuti Paulo ndi Yuda analongosola njira zakabisira zimene anthu opanduka amagwiritsira ntchito. Olemba Baibulo onsewa analemba kuti opandukawa ‘analowera m’tseri’ kapena kuti “anakwawira m’tseri” n’cholinga choti awononge khalidwe la anthu mumpingo wachikristu. Masiku ano, msampha wabwino kwambiri umene anthu oterewa angawonjolerepo anthu mosavuta ndiwo malo ochezera a pa Intaneti. Monga miyala yobisika pansi pa madzi, Akristu abodzawa amabisa cholinga chawo chenicheni ponamizira kuti akufuna kuthandiza achinyamata a Mboni. Koma cholinga chawo ndicho kuwononga chikhulupiriro cha osazindikira.—1 Timoteo 1:19, 20.

Magazini ino, pamodzi ndi mabuku ena ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, akhala akuchenjeza mobwerezabwereza za kuopsa kwa ampatukowa pa Intaneti. * Motero, munthu aliyense amene mungakumane naye pa malo otere, omwe achita kulembapo kuti akonzera Mboni za Yehova, ndiye kuti iyeyo samvera malangizo amenewa. Kodi inuyo ndithu mungafune kuti anzanu akhale anthu osafuna kumvera malangizo a m’Baibulo?—Miyambo 3:5, 6; 15:5.

Mukhoza Kuyamba Kudzipatula

Chinthu chinanso chokhudza malo ochezerapo pa Intaneti chimene muyenera kuchiganizira ndicho nthawi imene amakuwonongerani. José, amene tam’tchula kumayambiriro kwa nkhani ino anati: “Nthawi zina ndinkakomedwa kwambiri ndi macheza oterewa moti ndinkachita kuiwala nazo kudya.”

Mwina inuyo simungachite kukomedwa kwambiri mpaka pofika pomwe anafika José. Komabe, nthawi iliyonse imene mungawononge pocheza pa Intaneti imakhala nthawi yoti bwenzi mukuchitira zinthu zina. Mwina poyamba simungawononge nthawi imene mumachita zinthu monga ntchito yakusukulu yochitira kunyumba kapena ntchito zina zapakhomo. Koma mungayambe ndi kuwononga nthawi imene mumacheza ndi anthu am’banja mwanu. Adrian, amene amakhala ku Spain, anati: “Ndinkati tikangomaliza kudya chakudya nthawi yomweyo ndinkayatsa kompyuta n’kuyamba kucheza pa Intaneti. Macheza oterewa anandilowerera kwambiri moti ndinachita kufika posiyiratu kucheza ndi azibale anga.”

Ngati macheza oterewa akukuwonongetsani nthawi yochitira zinthu zopindulitsa, ndiye kutitu mukudzipatula kwa anthu amene ali ofunika kwambiri kwa inuyo. Baibulo limapereka chenjezo lofunika lotsatirali: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Anthu osawadziwa amene mumakumana nawo m’malo ambiri ochezera a pa Intaneti si anthu oti angakulimbikitseni kutsatira nzeru zenizeni za m’Baibulo. Kwenikweni zomwe anthu oterewa angakulimbikitseni ndizo kufuna kuchita zinthu zongokukomerani inuyo basi ndipo angakunyengeni kuti musiye kutsatira makhalidwe achikristu.

Inde, macheza otere angakukopeni chifukwa mungaone kuti sizikuvutani kucheza ndi munthu pa Intaneti kusiyana ndi kucheza ndi achibale anu. Mungaone kuti anzanu a pa Intanetiwo amafunitsitsa kumva maganizo anu pa nkhani zosiyanasiyana ndipo amatha kukuuzani zakukhosi kwawo. Komano azibale anu angaoneke kuti amachulukidwa ndi zinthu moti safuna kumva mukamafotokoza mavuto anu ndipo zimawavuta kukuuzani zakukhosi kwawo momasuka.

Komabe, dzifunseni kuti: ‘Kodi anzanga a pa Intaneti amandidziwadi ineyo bwinobwino? Kodi amaganizadi za tsogolo langa?’ Abale anu ndi amene kwenikweni angaganiziredi za nkhawa zanu ndiponso za moyo wanu wauzimu. Ngati makolo anu amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, ndiye kuti amafuna kumakambirana nanu. (Aefeso 6:4) Yesani kuwauza zakukhosi kwanu mwaulemu ndipo mudzadabwa kuona akutchera khutu n’kukumvetsani bwino kwambiri.—Luka 11:11-13.

Mmene Mungapewere Mavutowo

Nthawi zina mungalephere kupeweratu kucheza pa Intaneti, mwina chifukwa choti achita kukuuzani kusukulu monga mbali ya phunziro linalake. * Zikatero, samalani kuti musagwe m’vuto ndi malo oterewa pomvera malangizo otsatirawa.

Choyamba, pewani kugwiritsira ntchito Intaneti muli nokha m’chipinda chimene mumagonamo. Chifukwatu kutero n’chimodzimodzi n’kumayenda nokhanokha mumsewu wamdima wa mumzinda umene simukuudziwa. Kutero n’kuputa dala tsoka. M’malo mwake ikani kompyutayo pamalo oonekera mosavuta kwa aliyense m’nyumbamo.

Chachiwiri, muzimasuka nawo makolo anu pankhaniyi powasonyeza malo amene mumapitapo mukatsegula Intaneti ndiponso alongosolereni chifukwa chimene mukufunikira kutsegula malo enaake ochezera a pa Intaneti. Chinanso ikani malire a nthawi imene mukhale mutatsegula kompyutayo, ndipo musapitirire malirewo.

Chachitatu, mukompyutamo ikanimo mapulogalamu amene angakutetezeni potsekereza mauthenga aliwonse a pa Intaneti ochoka kwa anthu ofuna kukuchitani zachipongwe zokhudza kugonana. Winawake pa Intanetipo akakutumizirani uthenga woti akufuna kuchita nanu zopusa, nthawi yomweyo dziwitsani makolo ano kapena aphunzitsi anu. M’mayiko ena achidyamakanda amene akudziwa kuti ndinu mwana, koma n’kumatumiza mauthenga okunyengererani, amatha kumangidwa. Motero m’pofunika kukawanenera kupolisi.

Kuphatikiza apo, munthu aliyense amene mwakumana naye pa malo ochezera pa Intaneti musamamuuze dzina lanu, adiresi yanu, dzina la sukulu imene mumaphunzirako, kapena telefoni yanu. Komanso osayerekeza ngakhale pang’ono kulola kukumana pamasom’pamaso ndi munthu amene mwadziwana naye pa Intaneti.

Ngakhale kuti mawu otsatirawa a mfumu yanzeru Solomo analembedwa zaka zambirimbiri zapitazo, n’ngothandizabe pa nkhani ya zoopsa zimene zimapezeka pa malo ochezera a pa Intaneti. Mawu ake ndi akuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani Galamukani! ya Chingelezi ya December 8, 2004, masamba 18 mpaka 21.

^ ndime 21 Mayina ena tawasintha.

[Chithunzi patsamba 18]

N’chinthu chanzeru kusonyeza makolo anu malo amene mumatsegula pa Intaneti