Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malo Ovuta Kuwamvetsa a ku Africa

Malo Ovuta Kuwamvetsa a ku Africa

Malo Ovuta Kuwamvetsa a ku Africa

Mphepete mwa chipululu cha Namib, cha kumadzulo kwake, kuli dera la mtunda wotalika makilomita 2,000, lomwe kuli malo ambiri ozungulira a dothi lamchenga lomwe sipamera kalikonse. Malo ozungulirawa amakhala aakulu mamita awiri kapena mpaka 10 ndipo amapezeka m’dera lonselo. Malo alionse oterewa mphepete mwake muli udzu wautali. Kwa alendo ena obwera ku derali, malowa amaoneka ngati kuti nthaka ili ndi mathothomathotho kapena ngati kuti panakumbikakumbika ndi zimadontho zikuluzikulu za mvula. Anthu a m’derali amakhulupirira kuti malo ozungulirawa ali ndi mphamvu zinazake za mizimu. Mafuko ena a anthu amakhulupirira kuti malo alionse oterewa amazungulira manda a Mbathwa amene anafa pa nkhondo zambirimbiri zimene Abathwa anamenyana ndi atsamunda kwa zaka zambiri.

Asayansi nawonso kwa nthawi yaitali ayesera kufufuza kuti amvetse bwino malo ozungulirawa. Mu 1978, pokhulupirira kuti malowa adzasuntha pakapita nthawi, ochita kafukufuku ena anazika ndodo zachitsulo pakati pa malo ena kuti zikhale chizindikiro ngati malowa atasuntha. Patatha zaka 22, malo ozungulirawa anapezeka kuti sanasunthe. Nyuzipepala ya ku London ya The Daily Telegraph inati anthu anenapo zinthu zosiyanasiyana pofotokoza maganizo awo pankhani ya mmene malowa anapangidwira. Nyuzipepalayo inati ena amati anapangika chifukwa cha zinthu monga “chiswe, poizoni wa zomera zakupha za m’deralo, kuwonongeka kwa dothi chifukwa cha poizoni wa munthaka ndiponso ena anenapo kuti malo amenewa ndi amene nthiwatiwa zinkasewererapo mu mchenga.” Pulofesa wa sayansi ya zomera dzina lake Gretel van Rooyen wa ku yunivesite ya Pretoria, ku South Africa, posachedwapa anatsogolera kafukufuku wofuna kumvetsa malo ozungulirawa. Iye anati: “Tinayesa zinthu zonse zimene anthu amanena pofotokoza maganizo awo pa nkhani ya mmene malowa anapangikira ndipo zonse zinaoneka kuti sizoona.”

Mwina chinthu chochititsa chidwi chimene ofufuzawa anapeza n’choti udzu unkafota akaudzala pa dothi lotengedwa m’kati mwa malo aliwonse ozungulirawa. Komano unkamera bwinobwino akaudzala pa dothi lotengedwa mphepete mmene muli udzu wozungulira malowa. Zimenezi zikutsimikizira kuti pali kusiyana pakati pa dothi la m’kati ndi la m’mphepete mwa malowa. Ngakhale kuti atayeza dothi koyamba sanapeze chilichonse chogwira mtima, Van Rooyen akukhulupirira kuti akadzaliyezanso ndi makina amphamvu kwambiri oyezera dothi, adzadziwa zambiri zokhudza malowa. Iye akuganiza kuti mwina dothi la m’malo ozungulirawa lili ndi poizoni. Koma Van Rooyen ananena mu magazini ya New Scientist kuti “ngakhale titapeza kuti dothili lili ndi poizoni, funso lomwe lidzakhalepo lomwe lidzativute kuyankha n’loti poizoniyo anabwera bwanji m’dothimo.” Choncho pakadali pano, malo ozungulirawa akadali m’gulu la zinthu zambiri zovuta kuzimvetsa za padziko lapansi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

Courtesy of Austin Stevens