Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mayankho Othandiza a Mafunso Amene Mwakhala Mukufunsa

Mayankho Othandiza a Mafunso Amene Mwakhala Mukufunsa

Mayankho Othandiza a Mafunso Amene Mwakhala Mukufunsa

• Kodi n’chifukwa ninji makolo anga samandimvetsetsa?

• Kodi n’chifukwa ninji amayi ndi atate analekana?

• Kodi ndingapange motani mabwenzi enieni?

• Kodi n’chifukwa ninji ndimachita tondovi kwambiri?

• Kodi n’chifukwa ninji achichepere samaleka kundivutitsa?

• Bwanji ponena za kugonana ukwati usanachitike?

Buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza n’losiyana ndi mabuku ena a achinyamata. Nkhani zimene anazilemba m’buku limeneli anazisankha atakambirana ndi achinyamata ambirimbiri padziko lonse lapansi. Ndipo mayankho ake ochokera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, amathandizadi. Mafunso ali pamwambawa ndi ena chabe mwa mafunso amene buku la masamba 320 limeneli limayankha.

Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.